Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Baibo siinena kalikonse za kumenyanitsa matambula, nanga n’cifukwa ciani Mboni za Yehova sizicita nawo zimenezi?
Kumenyanitsa matambula amene muli vinyo (kapena cakumwa cina coledzeletsa) ni cizolowezi cakale ndiponso cofala, ngakhale kuti kacitidwe kake kamasiyana-siyana malinga na dela lake. Nthawi zina anthu amangokweza m’mwamba matambula awo, osawamenyanitsa. Munthu amene wanena kuti anthu amenyanitse matambula, nthawi zambili amafunila munthu wina moyo wacimwemwe, thanzi labwino, moyo wautali, na zina zotelo. Anthu ena amene akucita nawo zimenezi mwina amanena mawu ovomelezana na munthuyo kapena amakweza m’mwamba matambula awo n’kumwako vinyo pang’ono. Anthu ambili amaona kuti umenewu ni mwambo wopanda vuto lililonse kapena n’kusonyeza ulemu, koma pali zifukwa zabwino zimene Mboni za Yehova sizimenyanitsila nawo matambula.
Akhristu sacita nawo zimenezi, osati cifukwa coti safunila anzawo moyo wacimwemwe kapena thanzi labwino. Kalata imene bungwe lolamulila la Akhristu oyambilila linalembela mipingo, inatha na mawu amene angatanthauze “thanzi labwino,” “tikufunilani zabwino zonse,” kapena “tsalani bwino.” (Machitidwe 15:29) Ndipo olambila oona ena anauza mafumu kuti: “Mbuye wanga . . . akhale ndi moyo nthawi zamuyaya,” kapena “Mfumu ikhale ndi moyo kosatha.”—1 Mafumu 1:31; Nehemiya 2:3.
Koma kodi mwambo womenyanitsa matambula unayamba bwanji? Nsanja ya M’londa yacingelezi ya January 1, 1968, inagwila mawu buku la The Encyclopædia Britannica (la 1910), Voliyumu 13, tsamba 121. Bukuli limati: “Mwambo womwa vinyo pofunila anthu amoyo ‘thanzi labwino’ mwina unacokela ku mwambo wakale wacipembedzo womwa vinyo pofuna kukondweletsa milungu na anthu akufa. Agiriki na Aroma akamadya cakudya anali kuthila vinyo pansi monga nsembe kwa milungu yawo, ndipo akamadya pa mwambo wapadela anali kumwa vinyo pofuna kukondweletsa milunguyo na anthu akufa.” Bukulo linapitiliza kuti: “Mwambo womwa vinyo monga nsembe umenewu, unali kugwilizana kwambili na kumwa vinyo pofunila anthu amoyo thanzi labwino.”
Kodi zili concobe masiku ano? Buku lakuti International Handbook on Alcohol and Culture la mu 1995, limati: “[Kumenyanitsa matambula] mwina ni mbali yomwe yatsala ya mwambo wacipembedzo wakale wopeleka nsembe kwa milungu pothila pansi magazi kapena vinyo. Pamwambo umenewu anali kupeleka nsembezi posinthanitsa na pempho, kapena pemphelo limene anali kulinena mwacidule m’mawu awa: ‘Ukhale na moyo wautali!’ kapena ‘Ukhale na thanzi labwino!’”
N’zoona kuti wolambila woona saona kuti cizolowezi cinacake kapena zinthu zinazake n’zoipa kokha cifukwa coti zinayambila ku zipembedzo zonyenga zakale kapena zimafanana na zocitika za m’zipembedzozi. Taganizilani za makangaza. Buku lina lodziŵika bwino lofotokoza za m’Baibo limati: “Zikuoneka kuti makangaza anali kugwilitsidwanso nchito monga cizindikilo copatulika m’zipembedzo zacikunja.” Komabe, Mulungu ananena kuti makangaza opangidwa na nsalu aikidwe mu mpendelo wa malaya a mkulu wa ansembe, ndipo nsanamila zamkuwa za kacisi wa Solomo zinakongoletsedwa na makangaza. (Eksodo 28:33; 2 Mafumu 25:17) Komanso, mphete ya ukwati panthawi ina inali kugwilitsidwa nchito m’zipembedzo zonyenga. Koma anthu ambili masiku ano sadziŵa zimenezo, ndipo mphete amangoiona ngati umboni woti munthu ali pa banja.
Nanga bwanji kugwilitsila nchito vinyo pazocitika zacipembedzo? Mwacitsanzo, panthawi ina amuna a ku Sekemu, amene anali kulambila Baala analowa “m’nyumba ya mulungu wawo, nadya, namwa, natembelela Abimeleki,” mwana wa Gideoni. (Oweruza 9:22-28) Kodi mukuganiza kuti munthu wokhulupilika kwa Yehova akanamwa nawo vinyo ameneyo, mwina n’kupempha kuti mulungu wonyenga awathandize kuthana na Abimeleki? Pofotokoza nthawi imene anthu ambili mu Isiraeli anapandukila Yehova, Amosi anati anthuwo anali kugona pansi “ku maguwa a nsembe alionse, ndi m’nyumba ya Mulungu wawo akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.” (Amosi 2:8) Kodi olambila oona akanacita nawo zimenezo, kaya vinyoyo anathilidwa pansi monga nsembe kwa milunguyo kapena anangomwedwa pa zocitika zimenezo? (Yeremiya 7:18) Kapena kodi wolambila woona angakweze m’mwamba tambula yake ya vinyo n’kupempha kuti mulungu winawake acitile munthu zinazake kapena am’patse tsogolo labwino?
N’zocititsa cidwi kuti nthawi zina, anthu olambila Yehova anali kukweza manja awo m’mwamba n’kupempha kuti zinthu ziwayendele bwino. Anali kukweza manja awo kwa Mulungu woona. Timaŵelenga kuti: “Solomo anaimilila ku guwa la nsembe la Yehova . . . natambasulila manja ake kumwamba, nati, Yehova Mulungu wa Israyeli, palibe Mulungu wolingana ndi inu . . . ndipo mvelani inu m’Mwamba mokhala inumo; ndipo pamene mukumva, khululukilani.” (1 Mafumu 8:22, 23, 30) Mofanana na zimenezi, “Ezara analemekeza Yehova . . . navomeleza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja awo, nawelama, nalambila Yehova.” (Nehemiya 8:6; 1 Timoteyo 2:8) N’zoonekelatu kuti anthu okhulupilika amenewo sanali kukweza manja awo m’mwamba kuti adalitsidwe na mulungu winawake wopatsa mwayi.—Yesaya 65:11.
Anthu ambili amene amamenyanitsa matambula masiku ano mwina saganiza kuti akupempha kuti mulungu winawake awayankhe kapena awadalitse, koma sangafotokozenso cifukwa cimene amakwezela m’mwamba matambula awo a vinyo. Komabe, zilibe kanthu kuti anthuwa saganizila mozama nkhani imeneyi. Akhristu oona sangawatsanzile.
N’zodziŵika bwino kuti pankhani zinanso, Mboni za Yehova sizicita nawo zinthu zimene anthu ambili amacita. Mwacitsanzo anthu ambili amacita zinthu zolemekeza zizindikilo za dziko, kapena mbendela, ndipo saona kuti kucita zimenezi n’kulambila. Akhristu oona saletsa anthu ena kucita zimenezi, koma iwowo sacita nawo. Mboni zambili zikadziŵa nthawi imene zinthu zimenezi zicitike, zimacita zinthu mwanzelu n’colinga coti zisakhumudwitse anthu ena. Mulimonse mmene zingakhalile, sizifuna kucita nawo zinthu zosonyeza kukonda dziko lawo mopitilila muyeso, cifukwa n’zosemphana na zimene Baibo imanena. (Eksodo 20:4, 5; 1 Yohane 5:21) Masiku ano, anthu ambili mwina saona kuti kumenyanitsa matambula n’kokhudzana na kupembedza. Komabe, pali zifukwa zomveka zimene Akhristu amapewela kumenyanitsa matambula. Kunacokela ku zipembedzo zonyenga ndipo ngakhale masiku ano kumaonedwa ngati kupempha winawake amene ali kumwamba kuti atidalitse, kapena kupempha winawake wa mphamvu zoposa zathu kuti atithandize.—Eksodo 23:2.