Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 1:1-31

  • Mawu oyamba (1-3)

  • Paulo anayamikira Mulungu chifukwa cha Akorinto (4-9)

  • Anawalangiza kuti akhale ogwirizana (10-17)

  • Khristu ndi mphamvu komanso nzeru ya Mulungu (18-25)

  • Kudzitama mwa Yehova (26-31)

1  Ine Paulo, woitanidwa kukhala mtumwi+ wa Khristu Yesu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, pamodzi ndi Sositene mʼbale wathu, 2  ndikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto.+ Ndikulembera inu amene mwayeretsedwa mwa Khristu Yesu,+ amene mwaitanidwa kuti mukhale oyera, pamodzi ndi onse amene ali kulikonse omwe akuitana pa dzina la Ambuye wathu, Yesu Khristu,+ Ambuye wawo ndiponso wathu. 3  Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu zikhale nanu. 4  Nthawi zonse ndimathokoza Mulungu wanga chifukwa cha inu, poona kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kumene anakusonyezani kudzera mwa Khristu Yesu. 5  Chifukwa chogwirizana naye, ndinu olemera mʼzinthu zonse, ndipo wakuthandizani kukhala ndi luso la kulankhula ndiponso kudziwa zinthu zonse,+ 6  popeza umboni wonena za Khristu+ wakhazikika pakati panu. 7  Palibe mphatso imene mukuperewera pamene mukuyembekezera mwachidwi kuululidwa kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 8  Komanso Mulungu adzakulimbitsani mpaka pamapeto, kuti musakhale ndi chifukwa chokunenezerani mʼtsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 9  Mulungu amene anakuitanani kuti mukhale ogwirizana ndi Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu, ndi wokhulupirika.+ 10  Tsopano ndikukudandaulirani abale, mʼdzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzilankhula mogwirizana ndipo pakati panu pasakhale kugawanika,+ koma mukhale ogwirizana kwambiri pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.+ 11  Chifukwa anthu ena a mʼbanja la Kuloe andiuza za inu, abale anga, kuti pakati panu pali kugawanika. 12  Ndikutanthauza kuti, ena mwa inu akumanena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ena akuti, “Ine ndine wa Apolo,”+ enanso akuti, “Ine ndine wa Kefa,”* pamene ena akuti, “Ine ndine wa Khristu.” 13  Kodi Khristu wakhala wogawanika? Kodi Paulo anapachikidwa pamtengo wozunzikirapo* kuti inu mupulumutsidwe? Kapena kodi munabatizidwa mʼdzina la Paulo? 14  Ndikuthokoza Mulungu kuti sindinabatize aliyense wa inu kupatulapo Kirisipo+ ndi Gayo,+ 15  moti wina sanganene kuti munabatizidwa mʼdzina langa. 16  Nʼzoona kuti ndinabatizanso anthu a mʼbanja la Sitefana.+ Koma za enawo, sindikudziwa ngati ndinabatizapo aliyense. 17  Khristu sananditume kuti ndizibatiza anthu, koma kuti ndizilengeza uthenga wabwino,+ osati mwa luso la kulankhula,* kuopera kuti mtengo wozunzikirapo* wa Khristu ungakhale wopanda ntchito. 18  Nkhani yokhudza mtengo wozunzikirapowo* ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akupita kukawonongedwa,+ koma kwa ife amene tikupulumutsidwa, imeneyi ndi mphamvu ya Mulungu.+ 19  Chifukwa Malemba amati: “Ndidzathetsa nzeru za anthu anzeru ndipo ndidzakana* kuchenjera kwa anthu anzeru.”+ 20  Kodi wanzeru ali kuti? Mlembi* ali kuti? Katswiri wa mtsutso wa nthawi* ino ali kuti? Kodi Mulungu sanapange nzeru zadzikoli kukhala zopusa? 21  Mwa nzeru zake, Mulungu sanalole kuti dziko ligwiritse ntchito nzeru zake+ pomudziwa.+ Mʼmalomwake, Mulungu anaona kuti ndi bwino kupulumutsa okhulupirira kudzera mu uthenga umene anthu ena amauona kuti ndi wopusa.+ 22  Ayuda amafuna kuona zizindikiro+ ndipo Agiriki amafunafuna nzeru. 23  Koma ife timalalikira za Khristu amene anaphedwa popachikidwa pamtengo wozunzikirapo.* Ayuda amaona kuti zimenezi nʼzokhumudwitsa ndipo anthu a mitundu ina amaona kuti nʼzopusa.+ 24  Ngakhale zili choncho, Ayuda ndi Agiriki amene anaitanidwa amaona kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru za Mulungu.+ 25  Chifukwa chinthu cha Mulungu chimene anthu amachiona kuti nʼchopusa, nʼchanzeru kuposa anthu. Ndipo chinthu cha Mulungu chimene anthu amachiona kuti nʼchofooka, nʼchamphamvu kuposa anthu.+ 26  Mukuona mmene anakuitanirani abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa, si ambiri amphamvu amene anaitanidwa, si ambiri a mʼmabanja olemekezeka.+ 27  Koma Mulungu anasankha zopusa za dziko kuti achititse manyazi anthu anzeru, ndipo Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko kuti achititse manyazi zinthu zamphamvu.+ 28  Mulungu anasankhanso zinthu zonyozeka za dziko ndi zinthu zimene anthu amaziona ngati zachabechabe, zinthu zimene palibe, kuti achititse zinthu zimene zilipo kukhala zopanda mphamvu.+ 29  Anachita zimenezi kuti pasapezeke munthu wodzitama pamaso pa Mulungu. 30  Koma inu ndinu ogwirizana ndi Khristu Yesu chifukwa cha Mulunguyo. Yesuyo amatisonyeza nzeru za Mulungu ndiponso chilungamo cha Mulungu.+ Kudzera mwa Yesu, anthu akhoza kuyeretsedwa,+ ndipo kudzera mwa dipo* akhoza kumasulidwa,+ 31  kuti zigwirizane ndi zimene Malemba amanena zoti: “Amene akudzitama, adzitame mwa Yehova.”*+

Mawu a M'munsi

Amatchedwanso Petulo.
Kapena kuti, “polankhula mochenjera.”
Kapena kuti, “ndidzakankhira pambali.”
Kutanthauza katswiri wa Chilamulo.