1 Mafumu 5:1-18

  • Mfumu Hiramu anapereka zipangizo zomangira (1-12)

  • Antchito yokakamiza a Solomo (13-18)

5  Hiramu, mfumu ya ku Turo,+ atamva kuti Solomo wadzozedwa kukhala mfumu mʼmalo mwa bambo ake, anatuma atumiki ake kuti apite kwa Solomo popeza Hiramuyo anali mnzake wa Davide.+ 2  Kenako Solomo anatumiza uthenga kwa Hiramu wakuti:+ 3  “Inuyo mukudziwa bwino kuti Davide bambo anga sanathe kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wake, chifukwa cha nkhondo zimene adani ake ankamenyana naye mʼmadera onse omuzungulira, mpaka pamene Yehova anamuthandiza kugonjetsa adani akewo.*+ 4  Koma panopa Yehova Mulungu wanga wandipatsa mpumulo moti adani anga onse ondizungulira sakumenyana nane.+ Palibe aliyense amene akulimbana nane komanso palibe choipa chilichonse chimene chikuchitika.+ 5  Choncho ndikuganiza zomanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wanga, mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza Davide bambo anga kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamuike pampando wako wachifumu mʼmalo mwa iweyo, ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 6  Ndiye lamulani anthu anu kuti andidulire mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+ Antchito anga azidzagwira ntchito limodzi ndi antchito anu ndipo ndidzalipira antchito anu mogwirizana ndi malipiro amene munganene. Inuyo mukudziwa kuti pakati pathu palibe odziwa kudula mitengo ngati Asidoni.”+ 7  Hiramu atamva zimene Solomo ananenazi, anasangalala kwambiri ndipo anati: “Yehova atamandike lero chifukwa wapereka kwa Davide mwana wanzeru woti alamulire anthu ochulukawa.”+ 8  Choncho Hiramu anatumiza uthenga kwa Solomo wakuti: “Ndamva uthenga wanu. Ndichita zonse zimene mukufuna ndipo ndikupatsani mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ya junipa.*+ 9  Antchito anga adzainyamula ku Lebanoni nʼkupita nayo kunyanja, ndipo ndidzaimanga pamodzi ngati phaka nʼkuiyandamitsa panyanja kuti ikafike kumalo kumene mudzandiuze. Kenako akaimasula ndipo inuyo mukaitengera kumeneko. Malipiro ake mudzandipatsa chakudya cha banja langa.”+ 10  Choncho Hiramu anapereka kwa Solomo mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ina yofanana ndi mkungudza imene Solomo ankafuna. 11  Ndipo Solomo anapereka kwa Hiramu tirigu wokwana miyezo 20,000 ya kori,* kuti chikhale chakudya cha banja lake, ndiponso mafuta a maolivi oyenga bwino okwana miyezo 20 ya kori. Zinthu zimenezi ndi zomwe Solomo ankapereka kwa Hiramu chaka chilichonse.+ 12  Ndiyeno Yehova anapatsa Solomo nzeru mogwirizana ndi zimene anamulonjeza.+ Pakati pa Hiramu ndi Solomo panali mtendere ndipo awiriwa anachita pangano. 13  Mfumu Solomo inalemba amuna kuchokera ku Isiraeli konse kuti azigwira ntchito yokakamiza, ndipo anthu amene anawalembawo analipo 30,000.+ 14  Inkawatumiza ku Lebanoni mʼmagulu a anthu 10,000 pamwezi. Anthuwo ankakhala mwezi umodzi ku Lebanoni ndipo miyezi iwiri ankakhala kwawo. Adoniramu+ ndi amene ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yokakamizawo. 15  Solomo anali ndi anthu 70,000 onyamula katundu ndiponso anthu 80,000 osema miyala+ kumapiri.+ 16  Solomo analinso ndi nduna 3,300+ zomwe zinkayangʼanira anthu ogwira ntchito. 17  Ndiyeno mfumuyo inalamula kuti aseme miyala ikuluikulu yokwera mtengo,+ kuti akamange maziko+ a nyumbayo ndi miyala yosema.+ 18  Choncho amisiri omanga a Solomo ndi amisiri omanga a Hiramu ndiponso anthu a ku Gebala+ anasema miyalayo, ndipo anadula mitengo komanso kusema miyala pokonzekera kumanga nyumbayo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “anaika adani akewo pansi pa mapazi ake.”
Mitengo ya junipa ndi yofanana ndi mitengo ya mkungudza.
Muyezo wa kori unali wokwana malita 220. Onani Zakumapeto B14.