Kalata Yoyamba ya Yohane 2:1-29
2 Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo. Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi wotithandiza wolungama,+ Yesu Khristu,+ amene ali ndi Atate.
2 Iye anakhala nsembe yophimba+ machimo athu.*+ Osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.+
3 Tingasonyeze kuti tikumudziwa ngati titapitiriza kusunga malamulo ake.
4 Munthu amene amanena kuti, “Ine ndikumudziwa,” koma nʼkumalephera kusunga malamulo ake ndi wabodza ndipo alibe choonadi mumtima mwake.
5 Koma aliyense wosunga mawu a Khristu, amasonyeza kuti amakondadi Mulungu.+ Chifukwa cha zimenezi, timadziwa kuti ndife ogwirizana naye.+
6 Munthu amene amanena kuti ndi wogwirizana naye, ayenera kupitiriza kuyenda mmene iyeyo ankayendera.+
7 Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano. Koma ndikukulemberani lamulo lakale limene mwakhala nalo kuyambira pachiyambi.+ Lamulo lakaleli ndi mawu amene munawamva.
8 Komabe, ndikukulemberani lamulo latsopano limene Yesu ankalitsatira, limenenso inuyo mukulitsatira, chifukwa mdima ukupita ndipo kuwala kwenikweni kwayamba kale kuunika.+
9 Munthu amene amanena kuti ali mʼkuwala koma amadana+ ndi mʼbale wake, ndiye kuti adakali mumdima.+
10 Amene amakonda mʼbale wake ndiye kuti ali mʼkuwala+ ndipo palibe chimene chingachititse kuti apunthwe.
11 Koma amene amadana ndi mʼbale wake ali mumdima ndipo akuyenda mumdimawo+ komanso sakudziwa kumene akupita+ popeza maso ake sakuona chifukwa cha mdimawo.
12 Ndikulembera inu ana anga okondedwa, popeza machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina lake.+
13 Ndikulembera inu abambo, chifukwa mukumudziwa amene wakhala alipo kuyambira pachiyambi. Ndikulemberanso inu anyamata chifukwa mwagonjetsa woipayo.+ Ndikulembera inu ana okondedwa chifukwa mukuwadziwa Atate.+
14 Ndikulembera inu abambo chifukwa mukumudziwa iye amene wakhalapo kuyambira pachiyambi. Ndikulembera inu anyamata chifukwa ndinu olimba+ ndipo mumakhulupirira mawu a Mulungu+ komanso mwagonjetsa woipayo.+
15 Musamakonde dziko kapena zinthu zamʼdziko.+ Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate.+
16 Chifukwa chilichonse chamʼdzikoli, monga zimene thupi limalakalaka,+ zimene maso amalakalaka+ komanso kudzionetsera ndi zinthu zimene munthu ali nazo pa moyo wake,* sizichokera kwa Atate koma mʼdzikoli.
17 Kuwonjezera pamenepa, dzikoli likupita ndiponso chilichonse cha mʼdzikoli chimene anthu amalakalaka chikupita.+ Koma wochita zimene Mulungu amafuna adzakhala mpaka kalekale.+
18 Ana inu, ino ndi nthawi yakumapeto. Munamva kuti wokana Khristu akubwera,+ ndipo panopa okana Khristu ambiri aonekera.+ Chifukwa cha zimenezi tikudziwa kuti ino ndi nthawi yakumapeto.
19 Amenewo anachoka pakati pathu, koma sanali mʼgulu lathu,*+ chifukwa akanakhala a mʼgulu lathu, akanakhalabe ndi ife. Koma anachoka kuti zidziwike kuti si onse amene ali mʼgulu lathu.+
20 Inu munadzozedwa ndi mzimu wa Mulungu amene ndi woyera,+ ndipo nonsenu mukudziwa choonadi.
21 Ndakulemberani zimenezi, osati chifukwa chakuti simukudziwa choonadi+ koma chifukwa chakuti mukuchidziwa ndiponso chifukwa chakuti palibe bodza lililonse limene limachokera mʼchoonadi.+
22 Kodi wabodza angakhalenso ndani kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu?+ Ameneyu ndi wokana Khristu,+ yemwe amakana Atate komanso Mwana.
23 Aliyense amene amakana Mwana sangakhale pa ubwenzi ndi Atate.+ Koma amene amavomereza Mwana+ amakhalanso pa ubwenzi ndi Atate.+
24 Koma inu, zimene munamva pachiyambi zikhalebe mumtima mwanu.+ Zimene munamvazo zikakhalabe mumtima mwanu, mudzapitirizanso kukhala ogwirizana ndi Mwana komanso Atate.
25 Ndipotu paja iye anatilonjeza moyo wosatha.+
26 Ndakulemberani zinthu zimenezi zokhudza anthu amene akufuna kukusocheretsani.
27 Koma inuyo, Mulungu anakudzozani ndi mzimu wake+ ndipo mzimu umenewo udakali mwa inu, moti simukufunikira wina aliyense woti azikuphunzitsani. Koma kudzozedwako kukukuphunzitsani zinthu zonse+ ndipo ndi koona osati konama. Monga mmene kudzozedwako kwakuphunzitsirani, pitirizani kukhala ogwirizana naye.+
28 Tsopano inu ana anga okondedwa, khalanibe ogwirizana naye kuti akadzaonekera, tidzakhale ndi ufulu wa kulankhula.+ Komanso kuti tisadzachoke pamaso pake mwamanyazi pa nthawi ya kukhalapo* kwake.
29 Ngati mukudziwa kuti iye ndi wolungama, ndiye kuti mukudziwanso kuti aliyense wochita zinthu zabwino anabadwa kuchokera kwa Mulungu.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “anakhala njira yosangalatsira Mulungu.”
^ Kapena kuti, “komanso kulankhula modzitama zokhudza zinthu zimene munthu ali nazo.”
^ Kapena kuti, “sanali athu.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.