2 Mbiri 13:1-22

  • Abiya, mfumu ya Yuda (1-22)

    • Abiya anagonjetsa Yerobowamu (3-20)

13  Mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yerobowamu, Abiya anakhala mfumu ya Yuda.+ 2  Iye analamulira zaka zitatu ku Yerusalemu. Mayi ake anali Mikaya+ mwana wa Uriyeli wa ku Gibeya.+ Ndipo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu panachitika nkhondo.+ 3  Choncho Abiya anapita kunkhondoko ndi gulu la asilikali amphamvu komanso ophunzitsidwa bwino* okwana 400,000.+ Nayenso Yerobowamu anapita kukamenyana ndi Abiya ndipo anapita ndi asilikali 800,000 amphamvu komanso ophunzitsidwa bwino, ndipo anali okonzeka kumenya nkhondo. 4  Kenako Abiya anaimirira paphiri la Zemaraimu limene lili mʼdera lamapiri la Efuraimu nʼkunena kuti: “Tamvera iwe Yerobowamu ndi Aisiraeli nonsenu. 5  Kodi simukudziwa kuti Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka ufumu kwa Davide kuti azilamulira Isiraeli mpaka kalekale?+ Simukudziwa kodi kuti anaupereka kwa iye ndi ana ake+ pochita naye pangano la mchere?*+ 6  Koma Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anali mtumiki wa Solomo mwana wa Davide, anagalukira mbuye wake.+ 7  Ndipo anthu osowa zochita ndi opanda pake anakhala kumbali yake. Iwo anakhala amphamvu kuposa Rehobowamu mwana wa Solomo chifukwa Rehobowamuyo anali wamngʼono komanso wamantha ndipo sakanatha kulimbana nawo. 8  Tsopano mukuganiza zolimbana ndi ufumu wa Yehova umene uli mʼmanja mwa ana a Davide, chifukwa chakuti mulipo ambiri komanso muli ndi ana a ngʼombe agolide amene Yerobowamu anakupangirani kuti akhale milungu yanu.+ 9  Kodi simunathamangitse ansembe a Yehova,+ omwe ndi mbadwa za Aroni, komanso Alevi? Ndipo kodi simunadziikire ansembe ngati mmene amachitira anthu a mayiko ena?+ Aliyense amene wabwera ndi ngʼombe yaingʼono yamphongo komanso nkhosa zamphongo 7, amakhala wansembe wa zinthu zomwe si milungu. 10  Koma ife, Mulungu wathu ndi Yehova+ ndipo sitinamusiye. Ansembe athu, omwe ndi mbadwa za Aroni, akutumikira Yehova, ndipo Alevi akuthandiza pa ntchitoyi. 11  Iwo akupereka nsembe zopsereza kwa Yehova mʼmawa uliwonse+ ndi madzulo alionse limodzi ndi mafuta onunkhira.+ Ndipo mikate yosanjikiza*+ ili patebulo la golide woyenga bwino. Komanso madzulo alionse+ amayatsa nyale zomwe zili pachoikapo nyale chagolide.+ Tikuchita zimenezi chifukwa tikukwaniritsa udindo wathu kwa Yehova Mulungu wathu, koma inuyo mwamusiya. 12  Ndiye tamverani! Mulungu woona ali nafe ndipo akutitsogolera ndi ansembe ake ndiponso malipenga otiitanira ku nkhondo yomenyana nanu. Inu Aisiraeli, musamenyane ndi Yehova Mulungu wa makolo anu chifukwa simupambana.”+ 13  Koma Yerobowamu anatumiza asilikali kuti akawabisalire kumbuyo, choncho Yerobowamuyo ndi asilikali ena anakhala kutsogolo kwa Ayuda ndipo obisalawo anali kumbuyo kwa Ayudawo. 14  Ayudawo atatembenuka, anangoona kuti adani awo ali kumbuyo ndi kutsogolo kwawo. Choncho anayamba kufuulira Yehova+ kwinaku ansembe akuliza malipenga mokweza. 15  Kenako Ayuda anafuula kuti nkhondo iyambike. Atatero, Mulungu woona anagonjetsa Yerobowamu ndi Aisiraeli onse pamaso pa Abiya ndi Ayuda. 16  Aisiraeli anayamba kuthawa Ayuda, koma Mulungu anawapereka mʼmanja mwa Ayudawo. 17  Abiya ndi anthu ake anapha Aisiraeli ambirimbiri. Anapitiriza kupha Aisiraeliwo moti asilikali ophunzitsidwa bwino* okwana 500,000, anaphedwa. 18  Choncho pa nthawiyi Aisiraeli anachititsidwa manyazi, koma Ayuda anapambana chifukwa anadalira Yehova Mulungu wa makolo awo.+ 19  Abiya anapitiriza kuthamangitsa Yerobowamu ndipo anamulanda mizinda yake. Analanda Beteli+ ndi midzi yake yozungulira, Yesana ndi midzi yake yozungulira ndiponso Efuraini+ ndi midzi yake yozungulira. 20  Yerobowamu sanakhalenso ndi mphamvu mʼmasiku a Abiya ndipo kenako Yehova anamupha.+ 21  Koma Abiya anapitiriza kukhala wamphamvu. Patapita nthawi, anakwatira akazi 14+ ndipo anabereka ana aamuna 22 ndi aakazi 16. 22  Nkhani zina zokhudza Abiya, zimene anachita komanso mawu ake, zinalembedwa mu zimene mneneri Ido+ analemba.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ochita kusankhidwa.”
Limeneli ndi pangano losatha komanso limene silingasinthidwe.
Imeneyi ndi mikate yachionetsero.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ochita kusankhidwa.”