2 Mbiri 2:1-18
-
Kukonzekera kumanga kachisi (1-18)
2 Tsopano Solomo analamula kuti amange nyumba ya dzina la Yehova+ ndi nyumba yachifumu ya Solomoyo.+
2 Solomo anasankha amuna 80,000 kuti akhale osema miyala kumapiri+ ndiponso amuna 70,000 kuti azigwira ntchito zina.* Anasankhanso amuna 3,600 kuti aziwayangʼanira.+
3 Komanso Solomo anatumiza uthenga kwa Hiramu+ mfumu ya Turo, wakuti: “Mundichitire zomwe munachitira bambo anga Davide. Paja munawatumizira mitengo ya mkungudza kuti amangire nyumba* yawo yokhalamo.+
4 Ine ndikumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wanga kuti ikhale yopatulika kwa iye. Ndikufuna kuti ndiziperekamo nsembe za mafuta onunkhira pamaso pake+ ndiponso kuti nthawi zonse muzikhala mkate wosanjikiza.*+ Ndiziperekamonso nsembe zopsereza mʼmawa ndi madzulo,+ pa Masabata,+ masiku amene mwezi watsopano waoneka+ ndi pa nthawi ya zikondwerero+ za Yehova Mulungu wathu. Aisiraeli afunika azichita zimenezi mpaka kalekale.
5 Nyumba imene ndikumangayi idzakhala yochititsa chidwi, chifukwa Mulungu wathu ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.
6 Ndipo ndani angathe kumangira Mulunguyo nyumba? Chifukwa kumwamba, ngakhalenso kumwamba kwa kumwamba, nʼkosakwanira kuti akhaleko.+ Ndiye ine ndine ndani kuti ndimumangire nyumba, kupatulapo yoperekeramo nsembe pamaso pake?
7 Choncho nditumizireni munthu waluso pa ntchito za golide, siliva, kopa,*+ chitsulo, ubweya wapepo komanso za ulusi wofiira ndi wabuluu. Munthuyo akhalenso wodziwa kujambula ndi kulemba mochita kugoba. Azidzagwira ntchito ku Yuda ndi ku Yerusalemu limodzi ndi anthu anga aluso amene Davide bambo anga anawasankha.+
8 Munditumizirenso matabwa a mitengo ya mkungudza, mitengo ina yofanana ndi mkungudza+ ndiponso a mitengo ya mʼbawa+ kuchokera ku Lebanoni. Ndikudziwa kuti antchito anu ndi akatswiri podula mitengo ya ku Lebanoni.+ Antchito anga azidzagwira ntchito limodzi ndi antchito anu+
9 kuti andikonzere matabwa ambiri, chifukwa nyumba imene ndikufuna kumanga idzakhala yogometsa kwambiri.
10 Ineyo ndipereka chakudya cha antchito anu+ odula mitengo. Ndipereka tirigu wokwanira makori* 20,000, balere makori 20,000, vinyo mitsuko* 20,000 ndi mafuta mitsuko 20,000.”
11 Hiramu mfumu ya Turo atamva zimenezi, analembera Solomo uthenga wakuti: “Yehova amakonda anthu ake, choncho wakuikani inuyo kuti mukhale mfumu yawo.”
12 Kenako Hiramu anati: “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa wapereka kwa Mfumu Davide mwana wanzeru,+ wozindikira komanso womvetsa zinthu+ yemwe amange nyumba ya Yehova komanso ya ufumu wake.
13 Tsopano ndikutumiza munthu waluso ndi womvetsa zinthu, dzina lake Hiramu-abi.+
14 Mayi ake ndi a fuko la Dani, koma bambo ake anali a ku Turo. Iye ndi wodziwa ntchito za golide, siliva, kopa, chitsulo, miyala, matabwa, ubweya wapepo, nsalu zabwino kwambiri komanso ulusi wabuluu ndi wofiira.+ Amathanso kujambula ndi kulemba mochita kugoba ndipo amadziwa kupanga chilichonse chimene angauzidwe.+ Iye azidzagwira ntchito limodzi ndi anthu anu aluso ndiponso anthu aluso a mbuye wanga Davide bambo anu.
15 Ndipo inu mbuye wanga tumizani tirigu, balere, mafuta ndi vinyo zimene mwatilonjeza ife akapolo anu.+
16 Ife tidula mitengo yambiri mmene inu mukufunira kuchokera ku Lebanoni,+ ndipo tiziimanga mʼmaphaka oti aziyandama nʼkuitumiza panyanja kukafika ku Yopa.+ Inu muzikaitengera kumeneko nʼkupita nayo ku Yerusalemu.”+
17 Kenako Solomo anawerenga amuna onse amene anali alendo mʼdziko la Isiraeli+ ngati mmene Davide bambo ake anachitira.+ Ndipo panapezeka amuna okwana 153,600.
18 Choncho iye anasankhapo amuna 80,000 kuti akhale osema miyala+ kumapiri, amuna 70,000 kuti azigwira ntchito zina* komanso amuna 3,600 kuti akhale oyangʼanira anthuwo pa ntchito yawo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “onyamula katundu.”
^ Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
^ Umenewu unali “mkate wachionetsero.”
^ Kapena kuti, “mkuwa.”
^ Muyezo wa kori unali wokwana malita 220. Onani Zakumapeto B14.
^ Mtsuko umodzi unkakwana malita 22. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “azinyamula katundu.”