2 Mbiri 3:1-17
3 Kenako Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova+ ku Yerusalemu paphiri la Moriya,+ pamalo amene Yehova anaonekera kwa Davide+ bambo ake. Anamanga nyumbayo pamalo amene Davide anali atakonza, pamalo opunthira mbewu a Orinani+ Muyebusi.
2 Iye anayamba kumanga nyumbayi pa tsiku lachiwiri mʼmwezi wachiwiri, mʼchaka cha 4 cha ufumu wake.
3 Maziko amene Solomo anayala omangira nyumba ya Mulungu woona, mogwirizana ndi muyezo wakale, anali mikono* 60 mulitali ndi mikono 20 mulifupi.+
4 Khonde lakutsogolo linali mikono 20 mulitali ndipo linkafanana ndi mulifupi mwa nyumbayo. Kuchoka pansi kufika pamwamba, khondelo linali lalitali mikono 20* ndipo mkati mwake anakutamo ndi golide woyenga bwino.+
5 Nyumba yaikuluyo anaikuta ndi matabwa a mitengo ya junipa,* kenako anaikutanso ndi golide wabwino.+ Atatero, anaikongoletsa ndi matcheni+ ndiponso zithunzi za mitengo yakanjedza zojambula mochita kugoba.+
6 Anakongoletsanso nyumbayo poikuta ndi miyala yamtengo wapatali.+ Golide+ wakeyo anali wochokera ku Paravaimu.
7 Ndipo matabwa ake akudenga, pamakomo, makoma ndi zitseko za nyumbayo anazikuta ndi golide.+ Pamakoma ake anajambulapo akerubi mochita kugoba.+
8 Kenako iye anapanga chipinda cha Malo Oyera Koposa.+ Mulitali mwake chinali mikono 20 mofanana ndi mulifupi mwa nyumbayo ndipo mulifupi mwake chinali mikono 20. Anachikuta ndi golide wabwino wokwana matalente* 600.+
9 Golide wa misomali yake anali wolemera masekeli* 50 ndipo zipinda zake zapadenga anazikuta ndi golide.
10 Mʼchipinda cha Malo Oyera Koposa anapangamo zifaniziro ziwiri za akerubi nʼkuzikuta ndi golide.+
11 Mapiko a akerubiwo+ anali aatali mikono 20. Phiko limodzi la kerubi woyamba linali lalitali mikono 5 ndipo linagunda khoma la chipindacho. Phiko lina linalinso lalitali mikono 5 ndipo linakagunda phiko la kerubi wina.
12 Phiko limodzi la kerubi winayo linali lalitali mikono 5 ndipo linagunda khoma lina la chipindacho. Phiko lina linalinso lalitali mikono 5 ndipo linakagunda phiko la kerubi woyamba uja.
13 Mapiko otambasula a akerubiwo anali aatali mikono 20. Akerubiwo anali ataimirira ndipo nkhope zawo zinayangʼana mkati.*
14 Iye anapanganso katani*+ pogwiritsa ntchito ulusi wabuluu, ubweya wapepo, nsalu yofiira ndi nsalu yabwino kwambiri. Kenako anajambulapo akerubi.+
15 Kutsogolo kwa nyumbayo anamangako zipilala ziwiri+ zazitali mikono 35. Mutu wa chipilala chilichonse unali wautali mikono 5.+
16 Atatero anapanganso matcheni okhala ngati ovala mʼkhosi nʼkuwaika pamwamba pa zipilalazo ndipo anapanga makangaza* 100 nʼkuwaika kumatcheniwo.
17 Zipilalazo anaziika kutsogolo kwa kachisi, china anachiika kumanja* china kumanzere.* Chipilala chakumanja anachipatsa dzina lakuti Yakini* ndipo chakumanzere anachipatsa dzina lakuti Boazi.*
Mawu a M'munsi
^ Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Koma ena amaona kuti mawu akuti “muyezo wakale” amatanthauza mkono wautali womwe unali masentimita 51.8. Onani Zakumapeto B14.
^ Mipukutu ina yakale imati linali lalitali “120” pomwe mipukutu komanso Mabaibulo ena amati linali lalitali “mikono 20.”
^ Mitengo ya junipa ndi yofanana ndi mitengo ya mkungudza.
^ Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
^ Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “zinayangʼana mʼMalo Oyera.”
^ Kapena kuti, “nsalu yotchinga.”
^ “Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
^ Kapena kuti, “kumʼmwera.”
^ Kapena kuti, “kumpoto.”
^ Kutanthauza “Iye [Yehova] Akhazikitse.”
^ Nʼkutheka kuti likutanthauza “Mu Mphamvu.”