2 Mbiri 33:1-25
33 Manase+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 12 ndipo analamulira zaka 55 ku Yerusalemu.+
2 Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova ndipo ankatsatira zinthu zonyansa zomwe ankachita anthu a mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa Aisiraeli.+
3 Iye anamanganso malo okwezeka amene Hezekiya bambo ake anagwetsa.+ Anamanga maguwa ansembe a Abaala komanso mizati yopatulika,* ndipo ankagwadira gulu lonse la zinthu zakumwamba ndiponso kuzitumikira.+
4 Anamanganso maguwa ansembe mʼnyumba ya Yehova,+ imene Yehova ananena kuti: “Dzina langa lidzakhala ku Yerusalemu mpaka kalekale.”+
5 Iye anamanga maguwa ansembe a gulu lonse la zinthu zakumwamba mʼmabwalo awiri a nyumba ya Yehova.+
6 Manase anatentha* ana ake aamuna pamoto+ mʼChigwa cha Mwana wa Hinomu,+ ankachita zamatsenga,+ ankawombeza, ankachita zanyanga ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu ndi olosera zamʼtsogolo.+ Iye anachita zinthu zoipa kwambiri pamaso pa Yehova ndipo anamukwiyitsa.
7 Iye anaika mʼnyumba ya Mulungu woona+ chifaniziro chimene anapanga. Koma ponena za nyumba imeneyo, Mulungu anauza Davide ndi mwana wake Solomo kuti: “Mʼnyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa mpaka kalekale.+
8 Sindidzachotsanso mapazi a Aisiraeli mʼdziko limene ndinapereka kwa makolo awo, ngati atayesetsa kutsatira zonse zimene ndinawalamula zomwe ndi Chilamulo chonse, malangizo onse ndi ziweruzo zonse zimene ndinawapatsa kudzera mwa Mose.”
9 Manase anapitiriza kusocheretsa Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu ndipo anawachititsa kuti azichita zinthu zoipa kuposa zimene ankachita anthu a mitundu yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa Aisiraeli.+
10 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Manase ndiponso anthu ake, koma iwo sanamvere.+
11 Choncho Yehova anawabweretsera atsogoleri a asilikali a mfumu ya Asuri ndipo anagwira Manase ndi ngowe.* Atatero anamʼmanga ndi matcheni awiri akopa* nʼkupita naye ku Babulo.
12 Iye atavutika kwambiri ndi zimenezi, anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo* ndipo anadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.
13 Manase anayamba kupemphera kwa Mulungu ndipo iye anamva pemphero lake lochonderera ndiponso lopempha chifundo. Kenako anamʼbwezera ku Yerusalemu ndipo anakhalanso mfumu.+ Zitatero, Manase anadziwa kuti Yehova ndi Mulungu woona.+
14 Pambuyo pa zimenezi, Manase anamanga mpanda kunja kwa Mzinda wa Davide,+ kumadzulo kwa Gihoni,+ kuyambira mʼchigwa kukafika ku Geti la Nsomba.+ Mpandawo unazungulira nʼkukafika ku Ofeli+ ndipo anaukweza kwambiri. Iye anaikanso akuluakulu a asilikali mʼmizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.
15 Kenako anachotsa milungu yachilendo, fano limene linali mʼnyumba ya Yehova+ ndi maguwa onse ansembe amene anamanga mʼphiri la nyumba ya Yehova+ ndi mu Yerusalemu. Atatero anakataya zinthu zimenezi kunja kwa mzindawo.
16 Komanso Manase anakonza guwa lansembe la Yehova+ nʼkuyamba kuperekapo nsembe zamgwirizano+ ndi nsembe zoyamikira,+ ndipo anauza Ayuda kuti azitumikira Yehova Mulungu wa Isiraeli.
17 Koma anthu ankaperekabe nsembe mʼmalo okwezeka, kungoti ankazipereka kwa Yehova Mulungu wawo.
18 Nkhani zina zokhudza Manase, pemphero limene anapereka kwa Mulungu wake ndiponso mawu a anthu amasomphenya amene analankhula naye mʼdzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli, zalembedwa munkhani za mafumu a Isiraeli.
19 Nkhani zokhudza pemphero lake,+ zokhudza mmene Mulungu anamvera pemphero lake lochonderera, machimo ake onse komanso kusakhulupirika kwake+ zinalembedwa mʼmawu a amasomphenya ake. Munalembedwanso nkhani zokhudza kumene iye anamangako malo okwezeka nʼkuikako mizati yopatulika*+ ndi zifaniziro zogoba iye asanadzichepetse.
20 Kenako, mofanana ndi makolo ake, Manase anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda panyumba yake. Ndiyeno mwana wake Amoni anakhala mfumu mʼmalo mwake.+
21 Amoni+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 22 ndipo analamulira zaka ziwiri ku Yerusalemu.+
22 Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Manase bambo ake.+ Amoni ankapereka nsembe kwa zifaniziro zonse zogoba zimene bambo ake anapanga+ ndipo anapitiriza kuzitumikira.
23 Koma iye sanadzichepetse pamaso pa Yehova+ ngati mmene anachitira Manase bambo ake+ moti Amoni anapalamula kwambiri.
24 Patapita nthawi, atumiki ake anamukonzera chiwembu+ ndipo anamuphera mʼnyumba mwake.
25 Koma anthu amʼdzikolo anapha anthu onse amene anachitira chiwembu Mfumu Amoni.+ Kenako anthuwo anaika mwana wake Yosiya+ kuti akhale mfumu mʼmalo mwake.
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anadutsitsa.”
^ Mabaibulo ena amati, “akubisala mʼdzenje.”
^ Kapena kuti, “amkuwa.”
^ Kapena kuti, “anakhazika pansi mtima wa Yehova Mulungu wake.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.