2 Mbiri 7:1-22
7 Solomo atangomaliza kupemphera,+ moto unatsika kuchokera kumwamba+ nʼkutentha nsembe yopsereza ndiponso nsembe zina ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumbayo.+
2 Ansembe sanathe kulowa mʼnyumba ya Yehova chifukwa ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.+
3 Aisiraeli onse ankaonerera pamene moto unkatsika ndiponso pamene ulemerero wa Yehova unali pamwamba pa nyumbayo. Ataona zimenezi, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo kufika pansi ndipo anayamika Yehova, “chifukwa iye ndi wabwino ndipo chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”
4 Kenako mfumuyo ndi anthu onse anapereka nsembe kwa Yehova.+
5 Mfumu Solomo inapereka nsembe ngʼombe 22,000 ndi nkhosa 120,000. Choncho mfumuyo ndi anthu onse anatsegulira nyumba ya Mulungu woona.+
6 Ansembe anali ataimirira pamalo awo a ntchito. Nawonso Alevi anaimirira pamalo awo ndipo ananyamula zipangizo zoimbira Yehova nyimbo.+ (Mfumu Davide anapanga zipangizo zimenezi kuti azizigwiritsa ntchito poyamikira Yehova komanso pomutamanda kudzera mwa iwowo,* “chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”) Ansembe ankaimba malipenga+ mokweza patsogolo pawo, Aisiraeli onse ataimirira.
7 Solomo anapatula pakati pa bwalo la nyumba ya Yehova kuti aperekerepo nsembe zopsereza+ ndiponso mafuta a nsembe zamgwirizano. Anatero chifukwa paguwa lansembe lakopa*+ limene iye anamanga sipakanakwana kuperekerapo nsembe zopsereza,+ nsembe zambewu ndiponso mafuta.+
8 Pa nthawi imeneyo Solomo anachita chikondwerero masiku 7+ pamodzi ndi Aisiraeli onse. Linali gulu lalikulu la anthu amene anachokera kumadera osiyanasiyana, kuyambira ku Lebo-hamati* nʼkutsetsereka mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+
9 Koma pa tsiku la 8* anachita msonkhano wapadera+ chifukwa kwa masiku 7 anatsegulira guwa lansembe ndipo kwa masiku 7 ena anachita chikondwerero.
10 Pa tsiku la 23 la mwezi wa 7, Solomo anauza anthuwo kuti azipita kwawo. Iwo anapita akusangalala+ komanso akumva bwino mumtima, chifukwa cha zabwino zimene Yehova anachitira Davide, Solomo ndiponso anthu ake Aisiraeli.+
11 Choncho Solomo anamaliza kumanga nyumba ya Yehova ndi nyumba yachifumu.+ Zilizonse zimene iye anaganiza kuchita mumtima mwake zokhudza nyumba ya Yehova ndi nyumba yake zinayenda bwino.+
12 Kenako Yehova anaonekera kwa Solomo+ usiku nʼkumuuza kuti: “Ndamva pemphero lako ndipo ndasankha malo ano kukhala nyumba yanga yoperekeramo nsembe.+
13 Ndikatseka kumwamba ndipo mvula sinagwe, ndikalamula dzombe kuti lidye zomera zamʼdzikoli, ndikatumiza mliri pakati pa anthu anga,
14 anthu anga otchedwa ndi dzina langa+ akadzichepetsa,+ kupemphera, kundifunafuna komanso kusiya njira zawo zoipa,+ ine ndidzamva ndili kumwamba nʼkuwakhululukira tchimo lawo ndipo ndidzachiritsa dziko lawo.+
15 Tsopano maso anga akhala otseguka ndipo makutu anga azimvetsera mapemphero operekedwa pamalo ano.+
16 Ndasankha ndi kuyeretsa nyumbayi kuti dzina langa likhale pamenepa mpaka kalekale+ ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala pamenepa nthawi zonse.+
17 Iweyo ukayenda mʼnjira zanga ngati mmene bambo ako Davide anachitira, pochita zonse zimene ndakulamula ndiponso ukamamvera malangizo anga ndi ziweruzo zanga,+
18 inenso ndidzakhazikitsa mpando wako wachifumu,+ ngati mmene ndinapanganirana ndi bambo ako Davide+ kuti, ‘Munthu wa mʼbanja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+
19 Koma inuyo mukadzatembenuka nʼkusiya kutsatira malamulo anga amene ndakupatsani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira,+
20 ineyo ndidzachotsa Aisiraeli mʼdziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba iyi yomwe ndaiyeretsa chifukwa cha dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga. Ndidzachititsa anthu kuinyoza ndiponso kuinenera mawu achipongwe pakati pa mitundu yonse ya anthu.+
21 Ndipo nyumbayi idzakhala bwinja. Aliyense wodutsa pafupi adzaiyangʼana modabwa,+ ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova anachitira zimenezi dzikoli komanso nyumbayi?’+
22 Ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chakuti anasiya Yehova+ Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa mʼdziko la Iguputo+ ndipo anatenga milungu ina nʼkumaigwadira ndi kuitumikira.+ Nʼchifukwa chake iye anawabweretsera tsoka lonseli.’”+
Mawu a M'munsi
^ Nʼkutheka kuti akunena za Alevi.
^ Kapena kuti, “lamkuwa.”
^ Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Limeneli linali tsiku lotsatira pambuyo pa chikondwerero kapena kuti tsiku la 15.