Kwa Agalatiya 3:1-29

  • Ntchito za Chilamulo komanso chikhulupiriro (1-14)

    • Wolungama adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro (11)

  • Lonjezo la Abulahamu silinkadalira Chilamulo (15-18)

    • Khristu ndi mbadwa ya Abulahamu (16)

  • Kumene Chilamulo chinachokera komanso cholinga chake (19-25)

  • Ndinu ana a Mulungu chifukwa cha chikhulupiriro (26-29)

    • Ophunzira a Khristu ndi mbadwa za Abulahamu (29)

3  Agalatiya opusa inu! Kodi ndi ndani amene anakupusitsani,+ inu amene munakhala ngati mwaona Yesu Khristu atakhomereredwa pamtengo?+ 2  Ndikufuna ndikufunseni* chinthu chimodzi: Kodi munalandira mzimu chifukwa cha ntchito za chilamulo kapena chifukwa chokhulupirira zimene munamva?+ 3  Kodi ndinu opusa chonchi? Munayamba ndi kudalira mzimu, kodi tsopano mukufuna kumaliza ndi kudalira nzeru za anthu omwe si angwiro?+ 4  Kodi kuvutika konse kuja kunangopita pachabe? Ndikukhulupirira kuti sikunapite pachabe. 5  Ndiye kodi amene amakupatsani mzimu ndi kuchita zinthu zamphamvu pakati panu,+ amachita zimenezi chifukwa chakuti inuyo mukuchita ntchito za chilamulo kapena chifukwa chakuti munakhulupirira uthenga wabwino umene munamva? 6  Taganizirani za Abulahamu. Iye “anakhulupirira zimene Yehova* anamuuza ndipo ankaonedwa kuti ndi wolungama.”+ 7  Ndithudi mukudziwa kuti amene amakhalabe ndi chikhulupiriro ndi amene ali ana a Abulahamu.+ 8  Kale malemba ananeneratu kuti Mulungu adzaona anthu a mitundu ina kuti ndi olungama chifukwa cha chikhulupiriro. Choncho analengezeratu uthenga wabwino kwa Abulahamu wakuti: “Kudzera mwa iwe, mitundu yonse idzadalitsidwa.”+ 9  Choncho amene ali ndi chikhulupiriro champhamvu akudalitsidwa limodzi ndi Abulahamu, yemwe anali ndi chikhulupiriro.+ 10  Onse amene amadalira ntchito za chilamulo ndi otembereredwa, chifukwa Malemba amati: “Munthu aliyense amene sakupitiriza kutsatira zinthu zonse zimene zinalembedwa mumpukutu wa Chilamulo ndi wotembereredwa.”+ 11  Komanso, nʼzodziwikiratu kuti palibe munthu amene Mulungu angamuone kuti ndi wolungama chifukwa cha chilamulo,+ popeza “wolungama adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+ 12  Tsopano Chilamulo sichidalira chikhulupiriro. Koma “aliyense amene akuchita za mʼChilamulo adzakhala ndi moyo chifukwa cha chilamulocho.”+ 13  Khristu anatigula+ nʼkutimasula+ ku temberero la Chilamulo. Anachita zimenezi pokhala temberero mʼmalo mwa ife, chifukwa Malemba amati: “Munthu aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.”+ 14  Cholinga chake chinali chakuti kudzera mwa Khristu Yesu, mitundu ya anthu ipeze madalitso amene Abulahamu analonjezedwa,+ kuti tidzalandire mzimu wolonjezedwawo+ chifukwa cha chikhulupiriro chathu. 15  Abale, ndipereke fanizo mogwirizana ndi zimene zimachitika pakati pa anthu: Pangano likakhazikitsidwa, ngakhale kuti ndi pangano la anthu, palibe amene angalithetse kapena kuwonjezerapo mfundo zina. 16  Tsopano malonjezo anaperekedwa kwa Abulahamu ndi kwa mbadwa yake.*+ Malemba sanena kuti: “Kwa mbadwa zako,”* ngati kuti mbadwazo nʼzambiri. Koma akunena kuti, “kwa mbadwa yako,”* kutanthauza kuti ndi imodzi, amene ndi Khristu.+ 17  Komanso ineyo ndikuti: Choyamba, Mulungu anachita pangano ndi Abulahamu ndipo patapita zaka 430+ anapereka Chilamulo kwa anthu ake. Koma Chilamulocho sichinathetse pangano ndi lonjezo limene Mulungu anachita ndi Abulahamu, kuti lonjezolo lisagwirenso ntchito. 18  Chifukwa ngati Mulungu amapereka cholowa kudzera mʼchilamulo ndiye kuti sichidaliranso lonjezo. Koma mokoma mtima Mulungu wachipereka kwa Abulahamu kudzera mu lonjezo.+ 19  Ndiye nʼchifukwa chiyani Chilamulo chinaperekedwa? Anatipatsa Chilamulochi kuti machimo aonekere,+ mpaka mbadwa* imene inapatsidwa lonjezolo itafika.+ Angelo anapereka Chilamulocho+ kudzera mʼdzanja la mkhalapakati.+ 20  Ngati pangano likukhudza munthu mmodzi sipakhala mkhalapakati. Ndi mmenenso zinalili ndi Mulungu, anali yekha pamene anapereka lonjezoli. 21  Ndiye kodi Chilamulo chimatsutsa malonjezo a Mulungu? Ayi ndithu. Chifukwa pakanaperekedwa lamulo lopatsa moyo, bwenzi tikuonedwa kuti ndife olungama chifukwa chotsatira chilamulo. 22  Koma Malemba amasonyeza kuti anthu akulamuliridwa ndi uchimo, kuti lonjezo limene limakhalapo chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu, liperekedwe kwa anthu amene akumukhulupirira. 23  Komabe chikhulupirirocho chisanafike, chilamulo ndi chimene chinkatiyangʼanira ndipo chinatiika mu ukapolo. Pa nthawi imeneyo, tinkayembekezera chikhulupiriro chimene chinali chitatsala pangʼono kuonekera.+ 24  Choncho Chilamulo chinakhala wotiyangʼanira* amene anatitsogolera kwa Khristu,+ kuti tionedwe kuti ndife anthu olungama chifukwa cha chikhulupiriro.+ 25  Koma popeza chikhulupirirocho tsopano chafika,+ sitilinso pansi pa wotiyangʼanirayo.*+ 26  Ndipotu nonsenu ndinu ana a Mulungu+ chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu.+ 27  Chifukwa nonsenu amene munabatizidwa ndipo ndinu ogwirizana ndi Khristu mwakhala ndi makhalidwe ngati a Khristu.+ 28  Palibe Myuda kapena Mgiriki,+ palibe kapolo kapena mfulu,+ palibenso mwamuna kapena mkazi+ chifukwa nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.+ 29  Ndiponso ngati muli ophunzira a Khristu, ndinudi mbadwa* za Abulahamu,+ olandira cholowa+ mogwirizana ndi lonjezolo.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mundiuze.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yake.”
Kapena kuti, “mbewu.”
Kapena kuti, “wotitsogolera.”
Kapena kuti, “wotitsogolerayo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”