Kalata Yopita kwa Aroma 6:1-23
6 Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi tipitirize kuchimwa kuti kukoma mtima kwakukulu kuwonjezeke?
2 Ayi ndithu. Popeza tinafa ku uchimo,+ ndiye tipitirize kuchimwa chifukwa chiyani?+
3 Kapena simudziwa kuti tonsefe amene tinabatizidwa ndipo tsopano ndife ogwirizana ndi Khristu Yesu+ tinabatizidwanso mu imfa yake?+
4 Choncho tinaikidwa naye limodzi mʼmanda pamene tinabatizidwa mu imfa yake,+ kuti mofanana ndi Khristu amene anaukitsidwa kudzera mu ulemerero wa Atate, ifenso tikhale moyo watsopano.+
5 Chifukwa ngati tagwirizana naye pofa imfa yofanana ndi yake,+ ndithudi tidzagwirizananso naye poukitsidwa mofanana naye.+
6 Chifukwa tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa naye+ limodzi pamtengo nʼcholinga chakuti thupi lathu lauchimo likhale lopanda mphamvu,+ kuti tisakhalenso akapolo a uchimo.+
7 Chifukwa munthu amene wafa sakhalanso ndi mlandu* wa machimo ake.
8 Ndiponso, ngati tinafa limodzi ndi Khristu, timakhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo limodzi ndi iye.
9 Tikudziwa kuti popeza Khristu waukitsidwa,+ sadzafanso+ ndipo imfa sikumulamuliranso ngati mfumu.
10 Iye anafa kuti achotse uchimo kamodzi kokha basi+ ndipo moyo umene ali nawo, ali nawo kuti azichita chifuniro cha Mulungu.
11 Nanunso muzidziona ngati akufa pa nkhani ya uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.+
12 Choncho musalole kuti uchimo uzilamulirabe ngati mfumu mʼmatupi anu oti akhoza kufawo+ kuti muzitsatira zilakolako zawo.
13 Ndipo musapereke matupi* anu ku uchimo kuti akhale zida zochitira zinthu zosalungama, koma dziperekeni kwa Mulungu ngati anthu amene aukitsidwa. Matupi anunso muwapereke kwa Mulungu ngati zida zochitira chilungamo.+
14 Uchimo usamakulamulireni ngati mfumu, chifukwa simukutsatira Chilamulo,+ koma mukusangalala ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+
15 Kodi zikatere ndiye kuti tizichita tchimo chifukwa chakuti sitikutsatira Chilamulo koma tikusangalala ndi kukoma mtima kwakukulu?+ Ayi ndithu.
16 Kodi simukudziwa kuti mukamadzipereka kwa winawake ngati akapolo omvera, mumakhala akapolo a amene mukumumverayo?+ Mumakhala akapolo a uchimo+ umene umatsogolera ku imfa,+ kapena akapolo a kumvera komwe kumatsogolera ku chilungamo.
17 Koma tikuthokoza Mulungu kuti ngakhale kuti poyamba munali akapolo a uchimo, munamvera mochokera pansi pa mtima mfundo zatsopano zomwe munaphunzitsidwa.
18 Inde, popeza munamasulidwa ku uchimo,+ munakhala akapolo a chilungamo.+
19 Ndikulankhulatu ngati munthu chifukwa cha kufooka kwa matupi anu. Mmene munaperekera ziwalo zanu kuti zikhale akapolo a zonyansa ndiponso akapolo a kusamvera malamulo nʼcholinga chakuti muzichita zinthu zophwanya malamulo, perekaninso ziwalo zanu kuti mukhale akapolo a chilungamo ndiponso oyera.+
20 Chifukwa pamene munali akapolo a uchimo, munali omasuka ku chilungamo.
21 Kodi pa nthawiyo munkabala zipatso zotani? Zinali zinthu zimene panopa mumachita nazo manyazi. Ndipo mapeto a zinthu zimenezo ndi imfa.+
22 Koma tsopano chifukwa munamasulidwa ku uchimo nʼkukhala akapolo a Mulungu, mukubala zipatso za chiyero+ ndipo pamapeto pake mudzakhala ndi moyo wosatha.+
23 Chifukwa malipiro a uchimo ndi imfa,+ koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha+ kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.+