Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 10:1-11
10 Kenako ndinaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba ndipo anali atavala mtambo.* Kumutu kwake kunali utawaleza ndipo nkhope yake inali ngati dzuwa.+ Miyendo yake inali* ngati zipilala zamoto.
2 Mʼdzanja lake, anali ndi mpukutu waungʼono wotambasula. Iye anaponda panyanja ndi phazi lake lakumanja koma ndi phazi lake lakumanzere anaponda pamtunda.
3 Kenako anafuula ndi mawu okweza ngati kubangula kwa mkango.+ Atafuula choncho, panamveka mawu a mabingu 7.+
4 Ndiye mabingu 7 aja atalankhula, ndinkafuna kulemba. Koma ndinamva mawu ochokera kumwamba+ akuti: “Usunge mwachinsinsi* zimene mabingu 7 amenewa alankhula ndipo usazilembe.”
5 Mngelo amene ndinamuona ataimirira panyanja ndi pamtunda uja, anakweza dzanja lake lamanja kumwamba.
6 Iye analumbira mʼdzina la Mulungu amene adzakhale ndi moyo mpaka kalekale,+ amene analenga kumwamba ndi zinthu zonse zimene zili kumeneko, dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zili mmenemo komanso nyanja ndi zinthu zonse zimene zili mmenemo.+ Analumbira kuti: “Nthawi yodikira yatha.
7 Masiku oti mngelo wa 7+ alize lipenga akadzatsala pangʼono kukwana,+ chinsinsi chopatulika+ chimene Mulungu analengeza kwa akapolo ake aneneri,+ monga uthenga wabwino, chidzakwaniritsidwa ndithu.”
8 Kenako ndinamva mawu kuchokera kumwamba+ akulankhulanso ndi ine kuti: “Pita, katenge mpukutu wotambasula umene uli mʼdzanja la mngelo amene waima panyanja ndi pamtunda uja.”+
9 Choncho ndinapita kwa mngeloyo nʼkumuuza kuti andipatse mpukutu waungʼonowo. Iye anandiuza kuti: “Tenga mpukutuwu udye.+ Ukupweteketsa mʼmimba, koma mʼkamwa mwako ukhala wokoma ngati uchi.”
10 Ndinatengadi mpukutu waungʼonowo mʼdzanja la mngeloyo nʼkuudya.+ Mʼkamwa mwanga unkakoma ngati uchi,+ koma nditaudya mʼmimba mwanga munayamba kupweteka.
11 Ndiye ndinauzidwa kuti: “Uyenera kuneneranso zokhudza mitundu ya anthu, mayiko, zilankhulo ndi mafumu ambiri.”
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “anali atakutidwa ndi mtambo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mapazi ake anali.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Utsekere.”