Ekisodo 26:1-37

  • Chihema (1-37)

    • Nsalu za tenti (1-14)

    • Mafelemu ndi zoikapo mafelemu (15-30)

    • Katani ndi nsalu yotchinga (31-37)

26  “Upange chihema+ pogwiritsa ntchito nsalu 10 zopangira tenti. Nsaluzo zikhale za ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri. Pansaluzo upetepo+ akerubi.+ 2  Nsalu iliyonse ikhale mamita 13* mulitali ndipo mulifupi mwake ikhale mamita awiri. Nsalu zonse muyezo wake ukhale wofanana.+ 3  Ulumikize nsalu 5 kuti ikhale nsalu imodzi yaikulu ndipo uchite chimodzimodzi ndi nsalu 5 zinazo. 4  Kumapeto kwa nsalu imodzi yaikulu, upange zingwe zopota zabuluu zokolekamo ngowe. Uchitenso chimodzimodzi kumapeto kwa nsalu inayo, pamalo amene nsalu ziwirizi zidzalumikizane. 5  Uike zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu imodzi, ndipo uikenso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu inayo kuti zikhale moyangʼanizana pamalo olumikizirana. 6  Upangenso ngowe 50 zagolide nʼkulumikiza nsalu za tenti zija ndi ngowezo kuti nsaluzo zikhale chinsalu chimodzi chopangira chihema.+ 7  Upangenso nsalu za ubweya wa mbuzi+ zoyala pachihemacho. Nsaluzo zikhale zokwana 11.+ 8  Nsalu iliyonse ikhale mamita 13 mulitali komanso mamita awiri mulifupi. Nsalu zonse 11 muyezo wake ukhale wofanana. 9  Ulumikize nsalu 5 pamodzi komanso ulumikize nsalu 6 pamodzi, kenako upinde nsalu ya 6 imene ili kutsogolo kwa nsalu zolumikizanazo. 10  Uike zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni kwa nsalu za chihema zolumikizanazo. Uikenso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu zina zolumikizana, pomwe magulu awiri a nsalu zomwe zalumikizanazo adzakumane. 11  Upange ngowe 50 zakopa nʼkuzilowetsa mʼzingwe zopota zokolekamo ngowezo, nʼkulumikiza nsaluzo kuti zikhale chinsalu chimodzi chopangira chihema. 12  Kumbuyo kwa chihemacho kukhala nsalu yotsala. Choncho hafu ya nsalu yotsalayo ilendewere mpaka mʼmunsi. 13  Ndipo kumbali iliyonse mulitali mwa chinsalucho, mutsala nsalu yokwana masentimita 45. Nsalu yotsalayo izilendewera mpaka mʼmunsi kuti iphimbe chihemacho. 14  Upangenso chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira ndi chophimba chinanso pamwamba pake cha zikopa za akatumbu.+ 15  Upange mafelemu+ oimika a chihema amatabwa a mthethe.+ 16  Felemu lililonse likhale mamita 4 mulitali mwake, ndipo mulifupi mwake likhale masentimita 70. 17  Felemu lililonse likhale ndi zolumikizira ziwiri zoyandikana. Mafelemu onse a chihema uwapange choncho. 18  Upange mafelemu 20 a mbali yakumʼmwera ya chihemacho. 19  Upange zitsulo 40 zasiliva zokhazikapo mafelemu+ 20 aja. Zitsulo ziwiri zikhale pansi pa felemu lililonse kuti mulowe zolumikizira ziwiri.+ 20  Kumbali ina ya chihemacho, mbali yakumpoto kukhale mafelemu 20, 21  ndi zitsulo zake 40 zasiliva zokhazikapo mafelemu. Zitsulo ziwiri zikhale pansi pa felemu lililonse. 22  Upange mafelemu 6 nʼkuwaika kumbuyo kwa chihemacho, mbali yakumadzulo.+ 23  Ndiyeno upange mafelemu awiri kuti akhale ochirikiza mʼmakona awiri akumbuyo kwa chihemacho. 24  Mafelemu amenewa akhale ndi matabwa awiri ophatikiza kuyambira pansi mpaka pamwamba. Matabwawo alumikizane pamphete yoyamba. Mafelemu awiriwo apangidwe mofanana ndipo akhale ochirikiza mʼmakona. 25  Pakhale mafelemu 8 ndi zitsulo 16 zasiliva zokhazikapo mafelemu. Zitsulo ziwiri zikhale pansi pa felemu lililonse. 26  Upangenso ndodo za mtengo wa mthethe, ndodo 5 zikhale za mafelemu a mbali imodzi ya chihema.+ 27  Ndipo ndodo 5 zikhale za mafelemu a mbali ina ya chihema, ndodo zinanso 5 zikhale za mafelemu akumbuyo kwa chihema, mbali yakumadzulo. 28  Ndodo imene ikudutsa pakati pa mafelemu onse iyambire kumayambiriro mpaka kumapeto. 29  Mafelemuwo uwakute ndi golide,+ ndipo mphete zake zolowetsamo ndodo uzipange ndi golide. Ndodozo uzikute ndi golide. 30  Upange chihemacho motsatira pulani yake imene ndakuonetsa mʼphiri.+ 31  Upange katani+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pakataniyi upetepo akerubi. 32  Katani imeneyi uipachike pazipilala 4 za mtengo wa mthethe zokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo kataniyi tikhale tagolide. Zipilala zimenezi zikhale pazitsulo 4 zasiliva. 33  Kataniyi uipachike mʼmunsi mwa ngowe zolumikizira nsalu zapamwamba pa chihema, ndipo uike likasa la Umboni+ kuseri kwa kataniyi. Kataniyi ikhale malire a Malo Oyera+ ndi Malo Oyera Koposa.+ 34  Ukatero uike chivundikiro pamwamba pa likasa la Umboni mʼMalo Oyera Koposa. 35  Uike tebulo kunja kwa katani. Uikekonso choikapo nyale+ moyangʼanizana ndi tebulo kumbali yakumʼmwera ya chihemacho. Koma tebulolo uliike mbali yakumpoto. 36  Ndiyeno uwombe nsalu yotchinga* khomo la chihema. Nsaluyo ikhale ya ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 37  Nsalu yotchinga* khomo la chihema uipangire zipilala 5 za mtengo wa mthethe zokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo nsaluyo tikhale tagolide. Ndipo upange zitsulo 5 zakopa zokhazikapo zipilalazo.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 28.” Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “katani yotchinga.”
Kapena kuti, “Katani yotchinga.”