Ezara 7:1-28
7 Zimenezi zitachitika, mu ulamuliro wa mfumu Aritasasita+ ya ku Perisiya, Ezara*+ anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku Babulo. Iye anali mwana wa Seraya.+ Seraya anali mwana wa Azariya, Azariya anali mwana wa Hilikiya,+
2 Hilikiya anali mwana wa Salumu, Salumu anali mwana wa Zadoki, Zadoki anali mwana wa Ahitubu,
3 Ahitubu anali mwana wa Amariya, Amariya anali mwana wa Azariya,+ Azariya anali mwana wa Merayoti,
4 Merayoti anali mwana wa Zerahiya, Zerahiya anali mwana wa Uzi, Uzi anali mwana wa Buki,
5 Buki anali mwana wa Abisuwa, Abisuwa anali mwana wa Pinihasi,+ Pinihasi anali mwana wa Eliezara+ ndipo Eliezara anali mwana wa Aroni+ wansembe wamkulu.
6 Ezara anabwera kuchokera ku Babulo. Iye anali wokopera* Malemba ndipo ankadziwa bwino* Chilamulo cha Mose+ chimene Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka. Mfumu inamupatsa zonse zimene anapempha chifukwa dzanja la Yehova Mulungu wake linkamuthandiza.
7 Ena mwa Aisiraeli, ansembe, Alevi,+ oimba,+ alonda apageti+ ndi atumiki apakachisi*+ anapita ku Yerusalemu mʼchaka cha 7 cha mfumu Aritasasita.
8 Ezara anabwera ku Yerusalemu mʼmwezi wa 5, mʼchaka cha 7 cha mfumuyo.
9 Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, iye ananyamuka kuchokera ku Babulo ndipo anafika ku Yerusalemu pa tsiku loyamba la mwezi wa 5. Iye anafika ku Yerusalemu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linkamuthandiza.+
10 Ezara anakonzekeretsa mtima wake* kuti aphunzire Chilamulo cha Yehova, azichigwiritsa ntchito+ komanso kuti aziphunzitsa malamulo ndi ziweruzo mu Isiraeli.+
11 Izi nʼzimene zinali mʼkalata imene Mfumu Aritasasita inapereka kwa wansembe Ezara wokopera Malemba,* katswiri pophunzira* malamulo a Yehova ndi malangizo amene anapereka kwa Aisiraeli:
12 * “Kuchokera kwa Aritasasita,+ mfumu ya mafumu, kupita kwa wansembe Ezara, wokopera* Chilamulo cha Mulungu wakumwamba: Mtendere ukhale nawe. Tsopano
13 ndaika lamulo lakuti aliyense mu ufumu wanga pakati pa anthu a Isiraeli, ansembe awo ndi Alevi amene akufuna kupita nawe ku Yerusalemu apite.+
14 Iwe watumizidwa ndi mfumu komanso alangizi ake 7 kuti ukafufuze ngati anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu akutsatira Chilamulo cha Mulungu wako, chimene uli nacho.*
15 Utenge siliva ndi golide zimene mfumu ndi alangizi ake apereka mwakufuna kwawo kwa Mulungu wa Isiraeli, amene amakhala ku Yerusalemu.
16 Utengenso siliva ndi golide yense amene ulandire* mʼchigawo chonse cha Babulo, limodzi ndi mphatso za anthu komanso za ansembe omwe akupereka mwakufuna kwawo kunyumba ya Mulungu wawo, yomwe ili ku Yerusalemu.+
17 Ndalamazi ukagulire mwamsangamsanga ngʼombe zamphongo,+ nkhosa zamphongo,+ ana a nkhosa,+ limodzi ndi nsembe zake zambewu+ ndiponso nsembe zake zachakumwa.+ Zimenezi ukazipereke paguwa lansembe lapanyumba ya Mulungu wako, yomwe ili ku Yerusalemu.
18 Zilizonse zimene iweyo ndi abale ako mudzaone kuti nʼzabwino kuchita ndi siliva ndi golide wotsala, mogwirizana ndi zimene Mulungu wanu akufuna, mudzachite zimenezo.
19 Ziwiya zimene wapatsidwa kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wapanyumba ya Mulungu wako, ukaziike pamaso pa Mulungu ku Yerusalemu.+
20 Zinthu zina zonse zofunika panyumba ya Mulungu wako zimene ukuyenera kupereka, ukazitenge kunyumba yosungiramo chuma cha mfumu.+
21 Ineyo mfumu Aritasasita ndalamula asungichuma onse amene ali kutsidya lina la Mtsinje,* kuti chilichonse chimene wansembe Ezara,+ wokopera* Chilamulo cha Mulungu wakumwamba, angapemphe kwa inu chichitidwe mwamsanga.
22 Mumʼpatse ngakhale matalente* 100 a siliva, miyezo ya kori* 100 ya tirigu, mitsuko* 100 ya vinyo,+ mitsuko 100 ya mafuta+ ndi mchere+ wambiri.
23 Zonse zimene Mulungu wakumwamba walamula zokhudza nyumba yake, zichitidwe ndi mtima wonse+ kuti asakwiyire kwambiri ineyo, ana anga ndi anthu anga.+
24 Ndikufuna kukuuzaninso kuti si zololeka kulandira msonkho kuchokera kwa ansembe, Alevi, oimba,+ alonda apakhomo, atumiki a pakachisi*+ ndi anthu ogwira ntchito panyumba ya Mulungu. Musawakhometse msonkho umene munthu aliyense amakhoma, msonkho wakatundu+ komanso msonkho wamsewu.
25 Iweyo Ezara, pogwiritsa ntchito nzeru zimene Mulungu wako wakupatsa,* uike akuluakulu a zamalamulo ndi oweruza kuti nthawi zonse aziweruza anthu onse akutsidya la Mtsinje komanso onse odziwa malamulo a Mulungu wako. Aliyense amene sadziwa malamulowo, uzimuphunzitsa.+
26 Aliyense wosatsatira Chilamulo cha Mulungu wako ndi lamulo la mfumu, azipatsidwa chiweruzo msangamsanga, kaya choti aphedwe, athamangitsidwe, alipitsidwe kapena aikidwe mʼndende.”
27 Atamandike Yehova Mulungu wa makolo athu, amene waika maganizo amenewa mumtima mwa mfumu, kuti nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu ikongoletsedwe.+
28 Iye wandisonyeza chikondi chokhulupirika pamaso pa mfumu,+ pamaso pa alangizi ake+ ndiponso pamaso pa akalonga onse amphamvu a mfumu. Ineyo ndinalimba mtima* chifukwa dzanja la Yehova Mulungu wanga linkandithandiza, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri a Aisiraeli kuti tipitire limodzi.
Mawu a M'munsi
^ Kutanthauza “Thandizo.”
^ Kapena kuti, “mlembi.”
^ Kapena kuti, “Iye anali katswiri wokopera.”
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
^ Kapena kuti, “anatsimikiza mumtima mwake.”
^ Kapena kuti, “mlembi.”
^ Kapena kuti, “katswiri wokopera.”
^ Mavesi a Eza 7:12 mpaka 7:26 analembedwa mʼChiaramu.
^ Kapena kuti, “mlembi”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chimene chili mʼmanja mwako.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “upeze.”
^ Kapena kuti, “amene ali chakumtsinje wa Firate.”
^ Kapena kuti, “mlembi.”
^ Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
^ Mtsuko umodzi unkakwana malita 22. Onani Zakumapeto B14.
^ Muyezo wa kori unali wokwana malita 220. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mogwirizana ndi nzeru za Mulungu zimene zili mʼmanja mwako.”
^ Kapena kuti, “ndinadzilimbitsa.”