Ezekieli 44:1-31
44 Munthu uja anandipititsanso kugeti lakunja la malo opatulika, limene linayangʼana kumʼmawa+ ndipo tinapeza kuti linali lotseka.+
2 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Geti ili lipitiriza kukhala lotseka. Silikuyenera kutsegulidwa ndipo munthu aliyense sakuyenera kudzera pageti limeneli chifukwa chakuti Yehova, Mulungu wa Isiraeli, walowa kudzera pageti limeneli.+ Choncho likuyenera kukhala lotseka.
3 Koma mtsogoleri wa anthu azidzakhala mʼkanyumba kapageti kameneka kuti azidzadya chakudya pamaso pa Yehova+ chifukwa iye ndi mtsogoleri. Azidzalowa mmenemo kudzera kukhonde la kanyumbako ndipo azidzatulukiranso komweko.”+
4 Kenako anandipititsa kutsogolo kwa kachisi kudzera pageti lakumpoto. Nditayangʼana ndinaona kuti ulemerero wa Yehova wadzaza mʼkachisi wa Yehova.+ Choncho ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+
5 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, uchite chidwi,* uonetsetse ndipo umvetsere mwatcheru zonse zimene ndikuuze zokhudza malangizo ndi malamulo a kachisi wa Yehova. Uonetsetse khomo lolowera mʼkachisi ndi makomo onse otulukira mʼmalo opatulika.+
6 Uuze anthu opandukawo, a nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Mwanyanya kuchita zinthu zonyansa, inu a nyumba ya Isiraeli.
7 Mukabweretsa alendo amene ndi osachita mdulidwe wamumtima ndi mdulidwe wa khungu lawo nʼkulowa nawo mʼmalo anga opatulika, iwo amadetsa kachisi wanga. Mumapereka mkate wanga, mafuta ndi magazi, pamene mukuphwanya pangano langa chifukwa cha zonyansa zanu zonse zimene mukuchita.
8 Inu simunasamalire zinthu zanga zopatulika.+ Mʼmalomwake munasankha anthu ena kuti azigwira ntchito zapamalo anga opatulika mʼmalo mwa inu.”
9 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Mlendo aliyense amene akukhala mu Isiraeli yemwe sanachite mdulidwe wamumtima ndi mdulidwe wa khungu, asalowe mʼmalo anga opatulika.”
10 Koma Alevi amene anachoka kwa ine nʼkupita kutali+ pa nthawi imene Aisiraeli anachoka kwa ine nʼkuyamba kutsatira mafano awo onyansa* adzakumana ndi zotsatira za zochita zawo zoipa.
11 Kenako Aleviwo adzakhala atumiki mʼmalo anga opatulika kuti azidzayangʼanira mageti a kachisi+ komanso kutumikira pakachisi. Iwo azidzapha nyama za nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina za anthu ndipo adzaimirira pamaso pa anthuwo nʼkumawatumikira.
12 Ine ndalumbira nditakweza dzanja langa kuti ndiwalange chifukwa chakuti ankatumikira anthu pamaso pa mafano awo onyansa. Ndipo anakhala chinthu chopunthwitsa nʼkuchititsa kuti anthu a nyumba ya Isiraeli achimwe.+ Choncho adzakumana ndi zotsatira za zochita zawo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
13 ‘Sadzayandikira kwa ine kuti anditumikire monga ansembe kapena kuyandikira zinthu zanga zilizonse zoyera kapena zoyera koposa. Iwo adzachita manyazi chifukwa cha zinthu zonyansa zimene anachita.
14 Koma ine ndidzawaika kuti azidzayangʼanira ntchito zapakachisi, kuti azichita utumiki wapakachisi ndi zinthu zonse zimene zikuyenera kuchitika mʼkachisimo.+
15 Ana a Zadoki, omwe ndi Alevi ansembe,+ amene ankagwira ntchito zapamalo anga opatulika pa nthawi imene Aisiraeli anachoka kwa ine,+ ndi amene adzandiyandikire nʼkumanditumikira. Iwo adzaima pamaso panga nʼkundipatsa mafuta+ ndi magazi,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
16 ‘Iwo ndi amene adzalowe mʼmalo anga opatulika. Adzayandikira tebulo langa kuti anditumikire+ ndipo adzagwira ntchito zimene apatsidwa ponditumikira.+
17 Iwo akalowa mʼtinyumba tamʼmageti a bwalo lamkati, azivala zovala zansalu.+ Akamatumikira mʼtinyumba tamʼmageti a bwalo lamkati kapena mkati mwenimwenimo, asamavale chovala chilichonse cha ubweya wa nkhosa.
18 Iwo azivala nduwira zansalu kumutu kwawo ndi makabudula ansalu aatali.+ Asamavale chovala chilichonse chimene chingachititse kuti atuluke thukuta.
19 Asanapite kubwalo lakunja kumene kuli anthu, azivula zovala zawo zimene anavala potumikira+ nʼkuziika mʼzipinda zodyera zopatulika.*+ Akatero azivala zovala zina kuti asachititse kuti anthu akhale oyera chifukwa cha zovala zawozo.
20 Asamamete mpala kumutu kwawo+ kapena kusiya tsitsi lakumutu kwawo kuti litalike kwambiri. Iwo azingoyepula tsitsi lakumutu kwawo.
21 Ansembe asamamwe vinyo ngati akukalowa mʼbwalo lamkati.+
22 Iwo asamakwatire mkazi wamasiye kapena amene mwamuna wake anamusiya ukwati.+ Koma angathe kukwatira namwali yemwe ndi mbadwa ya Isiraeli kapena mkazi wamasiye amene anali mkazi wa wansembe.+
23 Iwo aziphunzitsa anthu anga za kusiyana kwa chinthu chopatulika ndi chinthu chomwe si chopatulika. Ndipo aziwaphunzitsanso kusiyana kwa chinthu chodetsedwa ndi chinthu choyera.+
24 Ngati pali mlandu, iwo ndi amene akuyenera kukhala oweruza+ ndipo aziweruza motsatira malamulo anga.+ Azisunga malamulo ndi malangizo anga okhudza zikondwerero zanga+ zonse ndipo aziyeretsa masabata anga.
25 Iwo asamayandikire munthu aliyense wakufa kuopera kuti angakhale odetsedwa. Koma wansembe akhoza kudzidetsa chifukwa cha bambo ake, mayi ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, mchimwene wake kapena mchemwali wake amene ndi wosakwatiwa.+
26 Ndipo wansembe akamaliza kudziyeretsa, azimuwerengera masiku 7.
27 Pa tsiku limene adzalowe mʼmalo oyera, mʼbwalo lamkati, kuti akatumikire mʼmalo oyerawo, adzapereke nsembe yake yamachimo,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
28 ‘Ndipo cholowa chawo ndi ichi: Cholowa chawo ndi ine.+ Musawapatse malo alionse mu Isiraeli, chifukwa cholowa chawo ndi ine.
29 Iwowa ndi amene azidzadya nsembe yambewu,+ nsembe yamachimo ndi nsembe yakupalamula+ ndipo chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mu Isiraeli chidzakhala chawo.+
30 Zipatso zonse zabwino kwambiri zoyambirira kucha komanso zopereka zanu za mtundu uliwonse zidzakhala za ansembe.+ Ufa wanu wamisere wa zokolola zanu zoyambirira muziupereka kwa wansembe.+ Zimenezi zidzachititsa kuti anthu amʼnyumba mwanu adalitsidwe.+
31 Ansembe asamadye mbalame iliyonse kapena nyama iliyonse imene aipeza yakufa kapena imene yakhadzulidwa ndi chilombo.’”+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wako ukhale pa.”
^ Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
^ Kapena kuti, “mʼzipinda zopatulika.”