Genesis 19:1-38
19 Angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo. Loti anali atakhala pageti la mzinda wa Sodomu. Atawaona ananyamuka kukakumana nawo, ndipo anawagwadira nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi.+
2 Ndiyeno anati: “Chonde ambuye anga, tiyeni kunyumba ya kapolo wanu. Tikakusambitseni mapazi ndiponso mukagone, kuti mawa mulawirire nʼkupitiriza ulendo wanu.” Koma iwo anati: “Ayi, ife tigona mʼbwalo lamumzindawu usiku wa lero.”
3 Ndiyeno Loti anawaumiriza kwambiri moti iwo anapita naye kunyumba kwake. Kumeneko anawakonzera phwando, nʼkuwaphikira mkate wopanda zofufumitsa, ndipo anadya.
4 Koma iwo asanagone, chigulu cha amuna a mumzinda wa Sodomu, chinafika nʼkuzungulira nyumba ya Loti. Pachigulupo panali anyamata komanso achikulire.
5 Iwo ankauza Loti mofuula kuti: “Kwanu kuno kwabwera amuna enaake usiku uno. Ali kuti amuna amenewo? Atulutse kuti tigone nawo.”+
6 Choncho Loti anatuluka mʼnyumbamo kuti alankhule nawo ndipo anatseka chitseko.
7 Ndiyeno iye anati: “Chonde abale anga, musachite zoipazi.
8 Paja ine ndili ndi ana aakazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna. Bwanji ndikutulutsireni amenewo kuti muchite nawo zimene mukufuna. Koma amuna okhawa musawachite chilichonse, chifukwa ndi alendo anga ndipo ndikuyenera kuwateteza.”+
9 Koma iwo anati: “Choka apa!” Ananenanso kuti: “Iwe ndi wobwera kwathu kuno, ndipo ukukhala monga mlendo. Ndiye lero uzitiuza zochita? Tsopano iweyo tikuchita zoopsa kuposa iwowo.” Atatero iwo anamupanikiza kwambiri Loti, moti anatsala pangʼono kuthyola chitseko.
10 Kenako alendo aja anatulutsa manja ndi kumukokera Loti mʼnyumbamo, nʼkutseka chitseko.
11 Ndipo anachititsa khungu amuna amene anali pakhomo la nyumbayo, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, moti anthuwo anavutika kufufuza khomo.
12 Ndiyeno alendowo anafunsa Loti kuti: “Kodi uli ndi achibale alionse kuno? Uwatulutse mumzinda uno, kaya ndi akamwini ako, ana ako aamuna, ana ako aakazi kapena aliyense amene ndi mʼbale wako.
13 Malo ano tiwawononga chifukwa Yehova wamva madandaulo ambiri okhudza anthuwa,+ moti Yehova watituma kudzawononga mzindawu.”
14 Choncho Loti anatuluka nʼkupita kukalankhula ndi akamwini ake omwe ankayembekezera kukwatira ana ake. Iye anawauza mobwerezabwereza kuti: “Fulumirani! Tulukani mumzinda uno, chifukwa Yehova auwononga.” Koma akamwini akewo ankangoona ngati akunena zocheza.+
15 Kutatsala pangʼono kucha, angelowo anayamba kumuuza Loti kuti afulumire. Iwo anamuuza kuti: “Fulumira! Tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwa, kuti musawonongedwe limodzi ndi mzindawu chifukwa cha kulakwa kwake.”+
16 Iye ankazengereza koma popeza Yehova anamuchitira chifundo,+ alendowo anagwira dzanja la iyeyo, mkazi wake ndi ana ake aakazi awiriwo nʼkuwatulutsa kukawasiya kunja kwa mzinda.+
17 Atafika nawo kunja kwa mzinda, anawauza kuti: “Thawani mupulumutse moyo wanu! Musayangʼane kumbuyo+ komanso musaime pamalo alionse mʼchigawochi.+ Thawirani kudera lakumapiri kuti musaphedwe!”
18 Koma Loti anawauza kuti: “Chonde Yehova, kumeneko ayi!
19 Mwandisonyeza kale chifundo ine mtumiki wanu komanso mwandisonyeza kukoma mtima kwakukulu* populumutsa moyo wanga.+ Koma sinditha kuthawira kudera lakumapiri chifukwa ndikuopa kuti tsoka likandigwera kumeneko nʼkufa.+
20 Chonde, taonani pali tauni yaingʼono pafupipa ndipo ndingathe kuthawira kumeneko. Tauni imeneyi ndi yaingʼono. Chonde ndiloleni ndithawire mʼtauni imeneyi. Ndikatero, ndipulumutsa moyo wanga.”
21 Pamenepo iye anayankha Loti kuti: “Chabwino, ndavomera zimene wapempha.+ Sindiwononga tauni imene wanenayo.+
22 Tiye, fulumira! Thawira kumeneko, ndipo sindichita chilichonse mpaka utakafika.”+ Nʼchifukwa chake anapatsa tauniyo dzina lakuti Zowari.*+
23 Pamene Loti ankafika ku Zowari nʼkuti dzuwa litatuluka.
24 Kenako Yehova anagwetsa sulufule ndi moto ngati mvula ku Sodomu ndi Gomora. Sulufule ndi motowo zinachokera kwa Yehova kumwamba.+
25 Choncho anawononga mizindayi. Anawononga chigawo chonsecho, kuphatikizapo anthu onse okhala mʼmizindayi komanso zomera zapanthaka.+
26 Koma mkazi wa Loti amene anali kumbuyo kwake, anayangʼana kumbuyo, ndipo anasanduka chipilala chamchere.+
27 Tsopano Abulahamu ananyamuka mʼmawa kwambiri nʼkupita pamalo amene anaimirira pamaso pa Yehova aja.+
28 Atayangʼana kumunsi ku Sodomu ndi Gomora ndi kudera lonse la chigawocho, anaona zoopsa. Kumeneko chiutsi chinali tolo! Chinkafuka ngati chiutsi chochokera pa uvuni wa njerwa.+
29 Koma Mulungu sanaiwale zimene anauza Abulahamu. Choncho pamene ankawononga mizinda ya mʼchigawocho, anatulutsa Loti mʼmizinda imeneyo. Imeneyi ndi mizinda imene Loti ankakhalako.+
30 Kenako Loti anachoka ku Zowari limodzi ndi ana ake aakazi awiri aja nʼkukakhala kudera lakumapiri,+ chifukwa ankachita mantha kukhala ku Zowari.+ Kumeneko, iye ndi ana ake awiriwo anayamba kukhala mʼphanga.
31 Ndiyeno mwana woyamba kubadwa anauza mngʼono wake kuti: “Bambo athuwatu akalamba, ndipo mʼdera lino mulibe mwamuna woti angatikwatire ngati mmene anthu amachitira.
32 Tiye tiwapatse vinyo bambowa kuti amwe, ndipo tigone nawo kuti tikhale ndi ana kuchokera kwa iwo.”
33 Choncho usiku umenewo iwo anakhala akuwapatsa vinyo bambo awo kuti azimwa. Kenako mwana woyamba kubadwayo anapita nʼkukagona ndi bambo akewo. Koma kuyambira pamene mwanayo anapita kukagona nawo mpaka pamene anachoka, bambowo sanadziwe chilichonse.
34 Tsiku lotsatira, mwana woyambayo anauza mngʼono wake kuti: “Ndinagona nawo bambo usiku. Leronso usiku tiwapatse vinyo kuti amwe. Ndiye iwenso upite ukagone nawo, kuti tikhale ndi ana kuchokera kwa iwo.”
35 Choncho usiku umenewonso anakhala akuwapatsa vinyo bambo awo kuti azimwa. Kenako, mwana wamngʼono uja anapita nʼkukagona nawo. Koma kuyambira pamene mwanayo anapita kukagona nawo mpaka pamene anachoka, bambowo sanadziwe chilichonse.
36 Choncho ana a Loti awiri onsewo anakhala oyembekezera atagona ndi bambo awo.
37 Mwana woyamba anabereka mwana wamwamuna nʼkumupatsa dzina lakuti Mowabu.+ Iye ndi tate wa Amowabu amasiku ano.+
38 Mwana wamngʼono nayenso anabereka mwana wamwamuna nʼkumupatsa dzina lakuti Beni-ami. Iye ndi tate wa Aamoni+ amasiku ano.