Genesis 26:1-35

  • Isaki ndi Rabeka ku Gerari (1-11)

    • Mulungu anatsimikizira lonjezo lake kwa Isaki (3-5)

  • Kukanganirana zitsime (12-25)

  • Pangano la Isaki ndi Abimeleki (26-33)

  • Akazi awiri a Chihiti a Esau (34, 35)

26  Tsopano mʼdzikomo munagwa njala yaikulu ngati imene inagwa mʼmasiku a Abulahamu.+ Choncho Isaki anapita kwa Abimeleki, mfumu ya Afilisiti, ku Gerari. 2  Ndiyeno Yehova anaonekera kwa iye nʼkumuuza kuti, “Usapite ku Iguputo. Ukhale mʼdziko limene ndikusonyeze. 3  Ukhale ngati mlendo mʼdzikoli,+ ndipo ndidzapitiriza kukhala nawe ndi kukudalitsa, chifukwa mayiko onsewa ndidzawapereka kwa iwe ndi kwa mbadwa* zako.+ Ndidzakwaniritsa lumbiro limene ndinalumbira kwa bambo ako Abulahamu+ kuti: 4  ‘Ndidzachulukitsa mbadwa zako ngati nyenyezi zakumwamba,+ ndipo mayiko onsewa ndidzawapereka kwa mbadwa* zako.+ Mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa mbadwa zako.’+ 5  Ndidzachita zimenezi chifukwa Abulahamu anamvera mawu anga, ndipo ankachita zofuna zanga ndi kusunga malamulo anga onse.”+ 6  Choncho Isaki anapitiriza kukhala ku Gerari.+ 7  Anthu akumeneko ankamufunsafunsa za mkazi wake, ndipo iye ankawayankha kuti, “Ndi mchemwali wanga ameneyu.”+ Ankaopa kunena kuti, “Ameneyu ndi mkazi wanga,” chifukwa anati: “Anthu a kuno akhoza kundipha chifukwa cha Rabeka,” pakuti mkaziyo anali wokongola mochititsa kaso.+ 8  Patapita nthawi, Abimeleki mfumu ya Afilisiti ankayangʼana pawindo, ndipo anaona Isaki akucheza mwachikondi ndi mkazi wake* Rabeka.+ 9  Nthawi yomweyo Abimeleki anaitanitsa Isaki nʼkumufunsa kuti: “Ameneyu ndi mkazi wako eti? Nanga nʼchifukwa chiyani unanena kuti, ‘Ndi mchemwali wangaʼ?” Ndiyeno Isaki anayankha kuti: “Ndinanena choncho poopa kuti andipha chifukwa cha iye.”+ 10  Koma Abimeleki anapitiriza kuti: “Nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi?+ Munthu wina akanatha kugona ndi mkazi wakoyu, ndipo ukanatipalamulitsa.”+ 11  Kenako Abimeleki analamula anthu ake onse kuti: “Aliyense amene angavutitse munthu uyu komanso mkazi wake, aphedwa.” 12  Zitatero, Isaki anayamba kudzala mbewu mʼdzikomo. Mʼchaka chimenechi anakolola zochuluka moti pa thumba limodzi lililonse la mbewu zimene anadzala anakolola matumba 100, chifukwa Yehova ankamudalitsa.+ 13  Isaki analemera, ndipo zinthu zinapitiriza kumuyendera bwino moti anali ndi chuma chambiri. 14  Iye anali ndi nkhosa komanso ngʼombe zankhaninkhani. Analinso ndi atumiki ochuluka kwambiri,+ moti Afilisitiwo anayamba kumʼchitira nsanje. 15  Choncho Afilisitiwo anatenga dothi nʼkukwirira zitsime zonse zimene atumiki a Abulahamu bambo ake anakumba, bambo akewo ali moyo.+ 16  Kenako Abimeleki anauza Isaki kuti: “Uchoke kwathu kuno, chifukwa wakhala munthu wamphamvu kwambiri kuposa ifeyo.” 17  Choncho Isaki anachoka kumeneko nʼkukamanga msasa wake mʼchigwa cha* Gerari+ nʼkuyamba kukhala kumeneko. 18  Ndiyeno Isaki anafukula zitsime zimene zinakumbidwa mʼmasiku a Abulahamu bambo ake. Afilisiti anakwirira zitsime zimenezi Abulahamu atamwalira,+ ndipo iye anazitchulanso mayina amene bambo ake anazipatsa.+ 19  Pamene atumiki a Isaki ankakumba zitsime mʼchigwacho,* anapeza chitsime cha madzi abwino. 20  Koma abusa a ku Gerari anayamba kukangana ndi abusa a Isaki, kuti: “Ndi madzi athu amenewa!” Choncho iye anapatsa chitsimecho dzina lakuti Eseke,* chifukwa abusawo anakangana naye. 21  Kenako iwo anakumbanso chitsime china, koma anayambanso kukanganirana chitsimecho. Choncho anachipatsa dzina lakuti Sitina.* 22  Pambuyo pake anasamuka kumeneko, ndipo anakumbanso chitsime china. Koma sanakanganirane chitsime chimenechi. Choncho iye anachipatsa dzina lakuti Rehoboti* nʼkunena kuti: “Chifukwa chake nʼchakuti, tsopano Yehova watipatsa malo okwanira, ndipo watipangitsa kuti tichulukane mʼdziko lino.”+ 23  Kenako iye anachokanso kumeneko nʼkupita ku Beere-seba.+ 24  Usiku umenewo, Yehova anaonekera kwa iye ndipo anamuuza kuti: “Ine ndine Mulungu wa bambo ako Abulahamu.+ Usaope,+ chifukwa ndili nawe. Ndidzakudalitsa ndi kuchulukitsa mbadwa* zako chifukwa cha Abulahamu mtumiki wanga.”+ 25  Kumeneko Isaki anamanga guwa lansembe nʼkuitanira pa dzina la Yehova.+ Anamanganso tenti yake,+ ndipo atumiki ake anakumba chitsime kumeneko. 26  Patapita nthawi, Abimeleki anafika kwa iye kuchokera ku Gerari limodzi ndi Ahuzati mlangizi wake komanso Fikolo mkulu wa asilikali ake.+ 27  Ndiyeno Isaki anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kwa ine? Si paja munadana nane ine nʼkundithamangitsa kwanu kuja?” 28  Koma iwo anayankha kuti: “Ife taona kuti Yehova ali ndi iwe.+ Choncho tinaganiza zokupempha kuti, ‘tilumbire kuti pakati pa iwe ndi ife pakhale mtendere ndipo tichite nawe pangano.+ 29  Tichite pangano kuti sudzatichitira choipa chilichonse, chifukwa ifenso sitinakuchitire choipa chilichonse. Tinakuchitira zabwino zokhazokha, chifukwa tinakuuza kuti uchoke kwathu kuja mwamtendere. Ndipo panopa Yehova wakudalitsa.’” 30  Kenako Isaki anawakonzera phwando, ndipo iwo anadya ndi kumwa. 31  Mʼmawa wake, analawirira kudzuka nʼkulumbiritsana.+ Kenako Isaki anatsanzikana nawo ndipo iwo anachoka mwamtendere. 32  Tsiku limenelo, atumiki a Isaki anapita kwa iye nʼkumuuza zokhudza chitsime chimene anakumba.+ Anamuuza kuti: “Ife tapeza madzi.” 33  Choncho chitsimecho anachipatsa dzina lakuti Siba.* Nʼchifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beere-seba+ mpaka lero. 34  Esau atakwanitsa zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wa Beeri, Muhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa Eloni, Muhiti.+ 35  Akaziwo anabweretsa chisoni kwa Isaki ndi Rabeka.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “akukumbatira mkazi wake.”
Kapena kuti, “mʼkhwawa la.”
Kapena kuti, “mʼkhwawamo.”
Kutanthauza, “Mkangano.”
Kutanthauza, “Kuimba Mlandu.”
Kutanthauza, “Malo Aakulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kutanthauza, “Lumbiro” kapena “7.”