Genesis 33:1-20
33 Tsopano Yakobo anakweza maso ake nʼkuona Esau akubwera limodzi ndi amuna 400.+ Ataona choncho, anagawa ana ake nʼkuwapereka kwa Leya, kwa Rakele ndi kwa akapolo ake awiri aja.+
2 Anaika akapolowo ndi ana awo patsogolo,+ Leya ndi ana ake anawaika pakati,+ ndipo Rakele+ ndi Yosefe anawaika pambuyo pawo.
3 Kenako iyeyo anapita kutsogolo kwawo nʼkuyamba kugwada ndipo anaweramitsa nkhope yake pansi mpaka maulendo 7. Anachita zimenezi mpaka kufika pafupi ndi mchimwene wakeyo.
4 Koma Esau anathamanga kukakumana naye ndipo anamukumbatira nʼkumukisa.* Atakumbatirana, onse awiri anagwetsa misozi kwambiri.
5 Kenako Esau anakweza maso ake nʼkuona akazi ndi ana. Ndiyeno anafunsa Yakobo kuti: “Nanga amene uli nawowa ndi ndani?” Iye anayankha kuti: “Amenewa ndi ana amene Mulungu wapatsa ine kapolo wanu.”+
6 Pamenepo akapolo aja anafika pafupi limodzi ndi ana awo ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.
7 Nayenso Leya anafika pafupi limodzi ndi ana ake ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi. Kenako Yosefe anafika limodzi ndi Rakele ndipo nawonso anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+
8 Tsopano Esau anafunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani watumiza magulu onse amene ndakumana nawo aja?”+ Iye anayankha kuti: “Ndachita zimenezi kuti mundikomere mtima mbuyanga.”+
9 Ndiyeno Esau anati: “Ziweto ndili nazo zambiri mʼbale wanga.+ Zimenezo ndi zako, usandipatse.”
10 Koma Yakobo anati: “Ayi chonde, musatero. Ngati mwandikomeradi mtima, landirani mphatso yangayi, chifukwa ndabweretsa mphatsoyi kuti ndidzaone nkhope yanu, ndipo ndaionadi. Zili ngati ndaona nkhope ya Mulungu, chifukwa mwandilandira ndi manja awiri.+
11 Chonde landirani mphatso yangayi, yomwe ndabweretsa pokufunirani mafuno abwino,+ chifukwa Mulungu wandikomera mtima ndipo wandipatsa chilichonse.”+ Yakobo anapitiriza kumukakamiza mpaka analandira mphatsoyo.
12 Kenako Esau anati: “Tiye tinyamuke tizipita, ndipo ine nditsogola.”
13 Koma Yakobo anati: “Monga mukudziwa mbuyanga, anawa ndi osakhwima,+ komanso ndili ndi nkhosa ndi ngʼombe zoyamwitsa. Tikaziyendetsa mofulumira kwambiri kwa tsiku limodzi, ziweto zonse zifa.
14 Chonde mbuyanga, tsogolani ndipo ine kapolo wanu ndizibwera mʼmbuyo mwanu. Ndiziyenda pangʼonopangʼono mogwirizana ndi kuyenda kwa ziwetozi komanso anawa. Ndikakupezani ku Seiri,+ mbuyanga.”
15 Ndiyeno Esau anati: “Chabwino, ndiye ndikusiyireko ena mwa anyamata angawa kuti akuthandize.” Koma iye anati: “Ayi musachite kutero. Musavutike mbuyanga, ndikungosangalala kuti mwandirandira bwino.”
16 Choncho, Esau anabwerera ku Seiri tsiku lomwelo.
17 Kenako Yakobo ananyamuka ulendo wopita ku Sukoti.+ Kumeneko anamanga nyumba yake ndi makola a ziweto zake. Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Sukoti.*
18 Atachoka ku Padani-aramu,+ Yakobo anafika bwino kumzinda wa Sekemu,+ mʼdziko la Kanani.+ Atafika, anamanga msasa pafupi ndi mzindawo.
19 Kenako anagula malo ndipo anamangapo tenti. Anawagula ndi ndalama zasiliva 100, kwa ana a Hamori, bambo ake a Sekemu.+
20 Pamalopo anamangapo guwa lansembe nʼkulitchula kuti Mulungu, Mulungu wa Isiraeli.+