Genesis 4:1-26

  • Kaini ndi Abele (1-16)

  • Mbadwa za Kaini (17-24)

  • Seti ndi mwana wake Enosi (25, 26)

4  Kenako Adamu anagona ndi mkazi wake Hava ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera.+ Mkaziyo atabereka Kaini*+ ananena kuti: “Ndabereka mwana wamwamuna mothandizidwa ndi Yehova.” 2  Pambuyo pake, Hava anabereka Abele+ mʼbale wake wa Kaini. Abele anali mʼbusa wa ziweto, koma Kaini anali mlimi. 3  Patapita nthawi, Kaini anabweretsa zina mwa zokolola zake zakumunda nʼkuzipereka nsembe kwa Yehova. 4  Koma Abele anabweretsa ana oyamba a ziweto zake+ nʼkuwapereka nsembe, ndipo anaperekanso nsembe mafuta a ziwetozo. Yehova anasangalala ndi Abele komanso nsembe yake.+ 5  Koma sanasangalale ndi Kaini komanso nsembe yake ngakhale pangʼono. Choncho Kaini anapsa mtima kwambiri ndipo nkhope yake inagwa chifukwa cha chisoni. 6  Ndiyeno Yehova anafunsa Kaini kuti: “Nʼchifukwa chiyani wapsa mtima choncho, komanso nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni? 7  Utasintha nʼkumachita zinthu zabwino, kodi sindingayambirenso kusangalala nawe? Koma ngati susintha nʼkumachita zinthu zabwino, uchimo wakubisalira pakhomo, ndipo ukufunitsitsa kukumbwandira. Kodi iweyo suyesetsa kuti uwugonjetse?” 8  Kenako Kaini anauza Abele mʼbale wake kuti: “Tiye tipite kunkhalango.” Ali kunkhalangoko, Kaini anamenya Abele mʼbale wake nʼkumupha.+ 9  Pambuyo pake, Yehova anafunsa Kaini kuti: “Kodi mʼbale wako Abele ali kuti?” Iye anayankha kuti: “Sindikudziwa. Kodi ndine mlonda wa mʼbale wangayo?” 10  Pamenepo Mulungu anati: “Nʼchiyani chimene wachitachi? Tamvetsera, magazi a mʼbale wako akundilirira munthaka.+ 11  Tsopano ndiwe wotembereredwa, ndipo ndikukuthamangitsa mʼdera limene nthaka yake yatsegula pakamwa nʼkulandira magazi a mʼbale wako, amene iwe wakhetsa ndi manja ako.+ 12  Uziti ukalima nthaka, suzikolola mokwanira. Udzakhala moyo woyendayenda ndi wothawathawa padziko lapansi.” 13  Kaini atamva zimenezi anauza Yehova kuti: “Chilango cha kulakwa kwanga nʼchachikulu kwambiri moti sindingathe kuchipirira. 14  Lero mukundithamangitsa pamalo ano ndipo sindidzathanso kukuyandikirani. Ndidzakhala woyendayenda ndi wothawathawa padziko lapansi, ndipo aliyense wondipeza, ndithu adzandipha.” 15  Ndiyeno Yehova anauza Kaini kuti: “Chifukwa cha zimene wanenazi, aliyense amene adzaphe iweyo Kaini, adzalangidwa maulendo 7.” Choncho Yehova anaikira Kaini chizindikiro* kuti aliyense womupeza asamuphe. 16  Kenako Kaini anachoka pamaso pa Yehova nʼkupita kukakhala kudera la Nodi,* kumʼmawa kwa Edeni.+ 17  Patapita nthawi, Kaini anagona ndi mkazi wake+ ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nʼkubereka Inoki. Ndiyeno Kaini anayamba kumanga mzinda umene anaupatsa dzina la mwana wake lakuti Inoki. 18  Kenako Inoki anabereka Irade, Irade anabereka Mehuyaeli, Mehuyaeli anabereka Metusaeli, ndipo Metusaeli anabereka Lameki. 19  Lameki anakwatira akazi awiri. Woyamba anali Ada ndipo wachiwiri anali Zila. 20  Ada anabereka Yabala. Yabala anali munthu woyamba kukhala mʼmatenti nʼkumaweta ziweto. 21  Dzina la mʼbale wake wa Yabala linali Yubala. Yubala anali munthu woyamba pa anthu onse oimba zeze ndi chitoliro. 22  Komanso Zila anabereka Tubala-kaini, amene anali mmisiri wosula zipangizo zamtundu uliwonse zakopa ndi zachitsulo. Ndipo mlongo wake wa Tubala-kaini anali Naama. 23  Kenako Lameki ananena ndakatulo iyi kwa akazi ake, Ada ndi Zila: “Tamverani mawu anga inu akazi a Lameki.Tcherani khutu ku zonena zanga: Ndapha munthu chifukwa chondivulaza,Ndaphadi mnyamata chifukwa chondimenya. 24  Ngati wopha Kaini adzalangidwe+ maulendo 7,Ndiye kuti wopha Lameki, adzalangidwa maulendo 77.” 25  Adamu anagonanso ndi mkazi wake Hava ndipo anabereka mwana wamwamuna. Hava anapatsa mwanayo dzina lakuti Seti*+ chifukwa atabadwa, Havayo ananena kuti: “Mulungu wandipatsa* mwana wina mʼmalo mwa Abele amene Kaini anamupha.”+ 26  Nayenso Seti anabereka mwana wamwamuna nʼkumupatsa dzina lakuti Enosi.+ Pa nthawi imeneyi, anthu anayamba kuitanira pa dzina la Yehova.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza kuti, “Woberekedwa.”
Nʼkutheka kuti chizindikiro chimenechi linali lamulo lochenjeza anthu.
Mawu akuti, “kudera la Nodi” amatanthauza kuti kudera la anthu othawa kwawo.
Kutanthauza, “Wosankhidwa; Kuika; Kukhazikitsa.”
Kapena kuti, “Mulungu wandisankhira.”