Genesis 46:1-34
46 Choncho Isiraeli anatenga banja lake komanso zinthu zonse zimene anali nazo nʼkunyamuka. Atafika ku Beere-seba+ anapereka nsembe kwa Mulungu wa bambo ake Isaki.+
2 Ndiyeno Mulungu analankhula ndi Isiraeli mʼmasomphenya usiku kuti: “Yakobo, Yakobo!” Ndipo Yakobo anayankha kuti: “Ine mbuyanga!”
3 Mulungu anamuuza kuti: “Ine ndine Mulungu woona, Mulungu wa bambo ako.+ Usaope kupita ku Iguputo, chifukwa kumeneko ndidzakupangitsa kukhala mtundu waukulu.+
4 Ineyo ndipita nawe ku Iguputo, ndiponso ine ndi amene ndidzabwere nawe mʼdziko lino kuchokera kumeneko.+ Ndipo Yosefe ndi amene adzakutseke maso pa imfa yako.”+
5 Kenako Yakobo ananyamuka ku Beere-sebako. Ana a Isiraeliwo anatenga Yakobo bambo awo, limodzi ndi ana awo komanso akazi awo. Anawatengera mʼngolo zimene Farao anatumiza.
6 Anatenganso ziweto zawo zonse ndi katundu wawo yense amene anapeza mʼdziko la Kanani. Kenako Yakobo ndi ana ake onse anafika ku Iguputo.
7 Anafika limodzi ndi ana ake aamuna ndi aakazi limodzinso ndi zidzukulu zake. Anafika ndi banja lake lonse.
8 Awa ndi mayina a ana a Isiraeli, kapena kuti ana a Yakobo, omwe anapita nawo ku Iguputo:+ Mwana woyamba wa Yakobo anali Rubeni.+
9 Ana a Rubeni anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+
10 Ana a Simiyoni+ anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shauli+ mwana wa mkazi wa Chikanani.
11 Ana a Levi+ anali Gerisoni, Kohati ndi Merari.+
12 Ana a Yuda+ anali Ere, Onani, Shela,+ Perezi+ ndi Zera.+ Koma Ere ndi Onani anafera kudziko la Kanani.+
Ana a Perezi anali Hezironi ndi Hamuli.+
13 Ana a Isakara anali Tola, Puva, Yabi ndi Simironi.+
14 Ana a Zebuloni+ anali Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.+
15 Amenewa ndi ana a Leya, amene anaberekera Yakobo ku Padani-aramu, kuphatikizapo Dina+ mwana wamkazi wa Yakobo. Ana onse aamuna ndi aakazi komanso zidzukulu zake analipo 33.
16 Ana a Gadi+ anali Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.+
17 Ana a Aseri+ anali Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya ndipo mchemwali wawo anali Sera.
Ana a Beriya anali Hiberi ndi Malikieli.+
18 Amenewa ndi ana a Zilipa,+ yemwe Labani anamupereka kwa mwana wake wamkazi Leya. Iye anaberekera Yakobo ana amenewa. Onse pamodzi analipo 16.
19 Ana a Rakele, mkazi wa Yakobo, anali Yosefe+ ndi Benjamini.+
20 Yosefe anabereka Manase+ ndi Efuraimu+ ku Iguputo. Anabereka anawa ndi mkazi wake Asenati+ mwana wa Potifera, wansembe wa mzinda wa Oni.*
21 Ana a Benjamini+ anali Bela, Bekeri, Asibeli, Gera,+ Namani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu+ ndi Aridi.+
22 Amenewa ndi ana amene Rakele anaberekera Yakobo. Onse pamodzi analipo 14.
23 Mwana wa* Dani+ anali Husimu.+
24 Ana a Nafitali+ anali Yahazeeli, Guni, Yezera ndi Silemu.+
25 Amenewa ndi ana a Biliha, yemwe Labani anamupereka kwa mwana wake wamkazi Rakele. Iye anaberekera Yakobo ana amenewa. Onse pamodzi analipo 7.
26 Mbadwa zonse za Yakobo zimene anapita nazo ku Iguputo zinalipo 66,+ osawerengera akazi a ana ake.
27 Ana amene Yosefe anabereka ku Iguputo analipo awiri. Anthu onse amʼnyumba ya Yakobo amene anali nawo ku Iguputo analipo 70.+
28 Yakobo anatumiza Yuda+ kuti atsogole kupita kwa Yosefe kukamudziwitsa kuti akubwera ku Goseni. Iwo atafika ku Goseni,+
29 Yosefe anauza anthu kuti amukonzere galeta lake, kenako ananyamuka kuti akakumane ndi Isiraeli bambo ake ku Goseni. Atangofika kwa bambo akewo, nthawi yomweyo anawakumbatira nʼkulira kwa kanthawi.*
30 Kenako Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Tsopano ndingathe kufa mwamtendere. Ndaona nkhope yako ndipo ndadziwa kuti udakali moyo.”
31 Ndiyeno Yosefe anauza abale ake ndi amʼnyumba ya bambo ake kuti: “Ndipite kwa Farao+ ndikamudziwitse kuti, ‘Abale anga ndi amʼnyumba ya bambo anga amene anali mʼdziko la Kanani, abwera kuno kwa ine.+
32 Anthuwa ndi abusa+ ndipo amaweta ziweto.+ Abwera ndi nkhosa, ngʼombe ndi zinthu zonse zimene ali nazo.’+
33 Farao akakuitanani nʼkukufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’
34 Inu mukayankhe kuti: ‘Akapolo anufe takhala tikuweta ziweto kuyambira tili ana kufikira lero, ifeyo ndi makolo athu omwe.’+ Mukayankhe choncho kuti mukhale ku Goseni+ kuno, chifukwa aliyense woweta nkhosa Aiguputo amanyansidwa naye.”+
Mawu a M'munsi
^ Amene ndi Heliyopolisi.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana a.” Nʼkutheka kuti panali ana ena aamuna amene mayina awo sanatchulidwe.
^ Kapena kuti, “nʼkulira mobwerezabwereza.”