Levitiko 25:1-55

  • Chaka cha Sabata (1-7)

  • Chaka cha Ufulu (8-22)

  • Kubweza katundu kwa mwiniwake (23-34)

  • Zoyenera kuchita ndi anthu osauka (35-38)

  • Malamulo okhudza ukapolo (39-55)

25  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose paphiri la Sinai kuti: 2  “Uza Aisiraeli kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsani,+ dzikolo lizikasunga sabata la Yehova.+ 3  Kwa zaka 6 muzikalima minda yanu, ndipo pa zaka 6 zimenezo muzidzadulira mitengo yanu ya mpesa ndi kukolola mbewu zanu.+ 4  Koma mʼchaka cha 7 dzikolo lizidzasunga sabata lopuma pa zonse, sabata la Yehova. Musamadzadzale mbewu mʼminda yanu kapena kudulira mitengo yanu ya mpesa. 5  Musamadzakolole mbewu zomera zokha kuchokera pa mbewu zimene munakolola chaka chapita, ndipo musamadzakololenso mphesa za mʼmitengo yanu yosadulirayo. Chaka chimenecho dziko lizidzapuma pa zonse. 6  Koma mungathe kudya chakudya chimene chamera mʼmunda mwanu mʼchaka cha sabatacho. Inuyo, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, waganyu wanu ndi alendo amene akukhala mʼnyumba mwanu mungathe kudya. 7  Zimene zamerazo zikhalenso chakudya cha ziweto zanu ndi zilombo zakutchire. Mbewu zonse zomera zokha zikhale chakudya. 8  Muzidzawerenga masabata 7 azaka, zaka 7 kuchulukitsa maulendo 7. Nthawi yonse ya masabata 7 azaka izidzakwana zaka 49. 9  Ndiyeno mʼmwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo, muzidzaliza lipenga la nyanga ya nkhosa mokweza kwambiri. Pa Tsiku Lochita Mwambo Wophimba Machimo,+ muzidzaliza lipengalo kuti limveke mʼdziko lanu lonse. 10  Chaka cha 50 chizidzakhala chopatulika ndipo muzidzalengeza ufulu kwa anthu onse okhala mʼdzikolo.+ Chizikhala Chaka cha Ufulu kwa inu, ndipo aliyense azibwerera kumalo ake ndi kubanja lake.+ 11  Chaka cha 50 chidzakhala Chaka cha Ufulu kwa inu. Musadzalime minda yanu kapena kukolola mbewu zomera zokha, kapenanso kukolola mphesa zamʼmitengo yosadulira.+ 12  Chimenecho ndi Chaka cha Ufulu ndipo chizikhala chopatulika kwa inu. Zimene mungathe kudya ndi zimene zamera zokha mʼminda yanu.+ 13  MʼChaka cha Ufulu chimenechi, aliyense wa inu azibwerera kumalo ake.+ 14  Mukamagulitsa chinthu kwa mnzanu kapena kugula chinthu kwa mnzanu, musamachitirane chinyengo.+ 15  Ukamagula malo kwa mnzako, uziwerenga zaka zimene zadutsa kuchokera mʼChaka cha Ufulu. Azikugulitsa malowo mogwirizana ndi zaka zimene zatsala kuti udzalepo mbewu.+ 16  Ngati patsala zaka zambiri, angathe kukweza mtengo wogulitsira malowo, koma ngati patsala zaka zochepa, azitsitsa mtengo wa malowo, chifukwa akukugulitsa kuchuluka kwa mbewu zimene udzakolole. 17  Pasapezeke aliyense pakati panu wochitira mnzake chinyengo,+ ndipo muziopa Mulungu wanu,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ 18  Mukamasunga malamulo anga komanso kutsatira zigamulo zanga mudzakhala otetezeka mʼdzikolo.+ 19  Dzikolo lidzakupatsani zipatso zake.+ Mudzadya ndi kukhuta, ndipo mudzakhala otetezeka mmenemo.+ 20  Koma ngati munganene kuti: “Popeza sitidzalima minda yathu nʼkukolola mbewu zathu, tidzadya chiyani mʼchaka cha 7?”+ 21  Dziwani kuti ndidzakudalitsani mʼchaka cha 6, ndipo dzikolo lidzakupatsani chakudya chokwanira zaka zitatu.+ 22  Kenako mudzadzala mbewu mʼchaka cha 8, ndipo mudzapitiriza kudya chakudya chimene munakolola chija mpaka mʼchaka cha 9. Mudzadya chakalecho mpaka mutakololanso china. 23  Musamagulitsiretu malo anu mpaka kalekale+ chifukwa dzikolo ndi langa.+ Kwa ine, inu ndinu alendo mʼdziko langa.+ 24  Mʼdziko lanu lonselo, munthu azikhala ndi ufulu wogulanso malo ake. 25  Mʼbale wanu akasauka nʼkugulitsa ena mwa malo ake, womuwombola amene ndi wachibale wake wapafupi azibwera ndi kugulanso zimene mʼbale wakeyo anagulitsa.+ 26  Ngati munthu alibe womuwombola, koma walemera nʼkukhala ndi ndalama zowombolera malo ake, 27  aziwerenga zaka zimene zadutsa kuchokera pamene anagulitsa malowo, ndipo azibweza ndalama zotsala kwa munthu amene anagula malowo. Akatero azibwerera kumalo akewo.+ 28  Koma ngati munthu amene anagulitsa malo sanapeze ndalama zoti angabwezere kwa amene anagulayo, malo amene anagulitsawo apitirizebe kukhala a munthu amene anawagulayo mpaka Chaka cha Ufulu chitafika.+ Mʼchaka chimenecho malowo azibwezedwa kwa mwiniwake ndipo amene anagulitsa maloyo azibwerera kumalo akewo.+ 29  Munthu akagulitsa nyumba mumzinda wokhala ndi mpanda, azikhala ndi ufulu woiwombola+ chaka chimodzi chisanathe kuchokera pamene anaigulitsa. Azikhala ndi ufulu umenewu kwa chaka chathunthu. 30  Koma ngati sanaiwombole chaka chimodzicho chisanathe, nyumba imene ili mumzinda wokhala ndi mpanda izikhala ya amene anagulayo mpaka kalekale, mʼmibadwo yake yonse, ndipo isamabwezedwe mʼChaka cha Ufulu. 31  Koma nyumba zimene zili mʼmidzi yopanda mpanda zizitengedwa monga mbali ya munda wa kunja kwa mzinda. Ufulu woiwombola uzikhalapobe, ndipo mʼChaka cha Ufulu izibwezedwa kwa mwiniwake. 32  Koma nyumba za Alevi zimene zili mʼmizinda yawo,+ Aleviwo azikhala ndi ufulu woziwombola mpaka kalekale. 33  Ndipo ngati Mlevi anagulitsa nyumba mumzinda wawo ndipo sanaiwombole, izibwezedwa kwa Mleviyo mʼChaka cha Ufulu.+ Zizikhala choncho chifukwa nyumba zamʼmizinda ya Alevi pakati pa Aisiraeli ndi za Aleviwo basi.+ 34  Komanso, asagulitse malo odyetserako ziweto+ ozungulira mizinda yawo, chifukwa amenewo ndi malo awo mpaka kalekale. 35  Mʼbale wanu akasauka pakati panu ndipo sangathe kudzisamalira, muzimuthandiza+ ngati mmene mungathandizire mlendo wokhala pakati panu,+ kuti nayenso akhale ndi moyo. 36  Musamalandire chiwongoladzanja kapena kupezerapo phindu+ pa iye.* Muziopa Mulungu wanu+ ndipo mʼbale wanu azikhala ndi moyo pakati panu. 37  Mukamukongoza ndalama musamafunepo chiwongoladzanja+ kapena kumupatsa chakudya kuti mupezerepo phindu. 38  Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo,+ kuti ndikupatseni dziko la Kanani. Ndinachita izi kuti ndikusonyezeni kuti ine ndine Mulungu wanu.+ 39  Mʼbale wanu amene mukukhala naye pafupi akasauka nʼkudzigulitsa kwa inu,+ musamamugwiritse ntchito ngati kapolo.+ 40  Muzimuona ngati waganyu+ komanso ngati mlendo. Azikugwirirani ntchito mpaka Chaka cha Ufulu. 41  Mʼchaka chimenecho iye ndi ana ake* azichoka nʼkubwerera kwa achibale ake. Azibwerera kumalo a makolo ake.+ 42  Aisiraeli ndi akapolo anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+ Choncho asamadzigulitse ngati mmene anthu amagulitsira kapolo. 43  Musamamuchitire nkhanza,+ ndipo muziopa Mulungu wanu.+ 44  Akapolo anu aamuna ndi aakazi azichokera mʼmitundu yokuzungulirani. Muzigula kapolo wamwamuna kapena wamkazi kuchokera mʼmitundu imeneyi. 45  Komanso muzigula akapolo kuchokera kwa ana a alendo okhala pakati panu.+ Mungagule akapolo kuchokera kwa iwo ndi kwa ana amene alendowo abereka mʼdziko lanu. Amenewa muziwagula kuti akhale akapolo anu. 46  Akapolowa mungathe kusiyira ana anu monga cholowa chawo mpaka kalekale. Anthu amenewa ndi amene azikhala antchito anu, koma Aisiraeli, omwe ndi abale anu musamawachitire nkhanza.+ 47  Koma ngati mlendo wokhala pakati panu walemera, ndipo mʼbale wanu amene akukhala naye pafupi wasauka nʼkudzigulitsa kwa mlendoyo, kapena kwa munthu wina wa mʼbanja la mlendoyo, 48  mʼbale wanuyo azikhalabe ndi ufulu wowomboledwa. Mmodzi mwa abale ake angathe kumuwombola.+ 49  Komanso mchimwene wa bambo ake, mwana wa mchimwene wa bambo akewo, wachibale wake aliyense wapafupi, kapena kuti aliyense wa mʼbanja lake angathe kumuwombola. Kapenanso mwiniwakeyo akalemera, azidziwombola.+ 50  Kuti achite zimenezi, iye aziwerengera limodzi ndi amene anamugulayo nthawi imene yadutsa kuchokera chaka chimene anadzigulitsa kudzafika Chaka cha Ufulu.+ Ndalama zimene anamugulira zizigwirizana ndi kuchuluka kwa zakazo.+ Malipiro a ntchito imene azigwira pa nthawi yotsalayo azifanana ndi a waganyu.+ 51  Ngati kwatsala zaka zochuluka, ndalama zake zodziwombolera zizigwirizana ndi zaka zimene zatsala. 52  Koma ngati kwatsala zaka zochepa kuti Chaka cha Ufulu chifike, aziwerenga yekha zaka zotsalazo, ndipo azipereka ndalama zodziwombolera zogwirizana ndi zaka zotsalazo. 53  Azimugwirira ntchito mofanana ndi waganyu chaka ndi chaka ndipo muzionetsetsa kuti sakumuchitira nkhanza.+ 54  Koma ngati sangathe kudziwombola potsatira njira zimenezi, adzachoka mʼChaka cha Ufulu,+ iye pamodzi ndi ana ake.* 55  Chifukwa Aisiraeli ndi akapolo anga. Iwo ndi akapolo anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kumupatsa ngongole yakatapira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana ake aamuna.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana ake aamuna.”