Salimo 25:1-22
Salimo la Davide.
א [Aleph]
25 Ndapereka moyo wanga kwa inu Yehova.
ב [Beth]
2 Inu Mulungu wanga, ndimakudalirani.+Musalole kuti ndichite manyazi.+
Musalole kuti adani anga asangalale chifukwa cha mavuto anga.+
ג [Gimel]
3 Ndithudi, palibe anthu amene amayembekezera inu amene adzachite manyazi.+Koma amene adzachite manyazi ndi anthu amene amachita zachinyengo popanda chifukwa.+
ד [Daleth]
4 Ndidziwitseni njira zanu, inu Yehova.+Ndiphunzitseni kuyenda mʼnjira zanu.+
ה [He]
5 Ndithandizeni kuti ndiziyenda mʼchoonadi chanu ndipo mundiphunzitse,+Chifukwa inu ndinu Mulungu amene mumandipulumutsa.
ו [Waw]
Ndimayembekezera inu tsiku lonse.
ז [Zayin]
6 Kumbukirani chifundo chanu, inu Yehova, komanso chikondi chanu chokhulupirika,+Zimene mumasonyeza nthawi zonse.*+
ח [Heth]
7 Musakumbukire machimo amene ndinachita ndili mnyamata komanso zolakwa zanga.
Mundikumbukire chifukwa cha ubwino wanu, inu Yehova,+Mogwirizana ndi chikondi chanu chokhulupirika.+
ט [Teth]
8 Yehova ndi wabwino komanso wolungama.+
Nʼchifukwa chake amalangiza ochimwa kuti ayende mʼnjira yoyenera.+
י [Yod]
9 Adzatsogolera ofatsa kuti azichita zinthu zoyenera,+Ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuti aziyenda mʼnjira yake.+
כ [Kaph]
10 Njira zonse za Yehova ndi zokhulupirika ndipo nʼzogwirizana ndi chikondi chake chokhulupirikaKwa anthu amene amasunga pangano lake+ ndi zikumbutso zake.+
ל [Lamed]
11 Chifukwa cha dzina lanu, inu Yehova,+Mundikhululukire tchimo langa, ngakhale kuti ndi lalikulu.
מ [Mem]
12 Ngati munthu amaopa Yehova,+
Iye adzamulangiza njira imene akuyenera kusankha.+
נ [Nun]
13 Moyo wake udzasangalala ndi zinthu zabwino,+Ndipo mbadwa* zake zidzatenga dziko lapansi kuti likhale lawo.+
ס [Samekh]
14 Anthu amene amaopa Yehova ndi amene amakhala naye pa ubwenzi wolimba,+Ndipo amawadziwitsa pangano lake.+
ע [Ayin]
15 Maso anga amayangʼana kwa Yehova nthawi zonse,+Chifukwa iye ndi amene amawonjola phazi langa mu ukonde.+
פ [Pe]
16 Tembenukani nʼkundiyangʼana ndipo mundikomere mtima.Chifukwa ndili ndekhandekha ndipo ndilibe wondithandiza.
צ [Tsade]
17 Nkhawa zamumtima mwanga zawonjezeka.+Ndipulumutseni ku mavuto anga.
ר [Resh]
18 Onani mavuto ndi masautso anga,+Ndipo mundikhululukire machimo anga onse.+
19 Onani mmene adani anga achulukira,Komanso onani kuti amadana nane kwambiri.
ש [Shin]
20 Tetezani moyo wanga ndipo mundipulumutse.+
Musalole kuti ndichite manyazi, chifukwa ndathawira kwa inu.
ת [Taw]
21 Kukhala wokhulupirika komanso kuchita zinthu zoyenera kunditeteze,+Chifukwa chiyembekezo changa chili mwa inu.+
22 Inu Mulungu, pulumutsani* Isiraeli ku mavuto ake onse.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Zimene munayamba kuchita kale kwambiri.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wombolani.”