Salimo 63:1-11
Nyimbo ya Davide, pamene anali mʼchipululu cha Yuda.+
63 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ine ndikukufunafunani.+
Ine ndikulakalaka inu.*+
Ndalefuka* chifukwa cholakalaka inuMʼdziko louma komanso lopanda madzi, kumene sikumera chilichonse.+
2 Choncho ndakuonani mʼmalo oyera.Ndaona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.+
3 Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchabwino kuposa moyo,+Milomo yanga idzakulemekezani.+
4 Choncho ndidzakutamandani moyo wanga wonse.Ndidzapemphera mʼdzina lanu nditakweza manja anga.
5 Ndakhutira* ndi gawo labwino komanso losangalatsa kwambiri,*Choncho milomo yanga idzakutamandani pofuula mosangalala.+
6 Ndimakukumbukirani ndili pabedi langa,Ndimaganizira mozama za inu usiku wonse.*+
7 Chifukwa inu mumandithandiza,+Ndipo ndimafuula mosangalala mumthunzi wa mapiko anu.+
8 Ndimakhala* nanu pafupi kwambiri.Dzanja lanu lamanja limandigwira mwamphamvu.+
9 Koma amene akufuna kuwononga moyo wanga*Adzatsikira kumanda.
10 Adzaphedwa ndi lupanga,Adzakhala chakudya cha nkhandwe.
11 Koma mfumu idzasangalala ndi zimene Mulungu adzaichitire.
Munthu aliyense wolumbira mʼdzina la Mulungu adzasangalala kwambiri,*Chifukwa pakamwa pa anthu olankhula zabodza padzatsekedwa.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Moyo wanga ukulakalaka inu.”
^ Kapena kuti, “Thupi langa lalefuka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi mafuta komanso kunenepa.”
^ Kapena kuti, “Moyo wanga wakhutira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “pa maulonda a usiku.”
^ Kapena kuti, “Moyo wanga umakhala.”
^ Kapena kuti, “akufuna kundipha.”
^ Kapena kuti, “adzadzitamandira.”