Salimo 97:1-12
97 Yehova wakhala Mfumu!+
Dziko lapansi lisangalale.+
Zilumba zambiri zikondwere.+
2 Mitambo ndi mdima wandiweyani zamuzungulira.+Maziko a mpando wake wachifumu ndi chilungamo komanso chiweruzo cholungama.+
3 Moto umachoka kwa iye+Nʼkupsereza adani ake omuzungulira.+
4 Kungʼanima kwa mphezi zake kumaunika dziko.Dziko lapansi limaona zimenezi ndipo limanjenjemera.+
5 Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,+Pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.
6 Kumwamba kumalengeza za chilungamo chake,Ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.+
7 Onse amene akutumikira chifaniziro chilichonse achite manyazi,+Amene amadzitama chifukwa cha milungu yawo yopanda pake.+
Muweramireni,* inu milungu yonse.+
8 Ziyoni wamva ndipo akusangalala,+Matauni* a ku Yuda akukondweraChifukwa cha zigamulo zanu, inu Yehova.+
9 Chifukwa inu Yehova, ndinu Wamʼmwambamwamba woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.Ndinu wokwezeka kwambiri kuposa milungu ina yonse.+
10 Inu amene mumakonda Yehova, muzidana ndi zoipa.+
Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika.+Amawapulumutsa mʼmanja mwa* oipa.+
11 Kuwala kwaunikira olungama+Ndipo owongoka mtima akusangalala.
12 Sangalalani chifukwa cha Yehova, olungama inu,Ndipo yamikirani dzina lake loyera.*
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Mulambireni.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aakazi.”
^ Kapena kuti, “ku mphamvu za.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chikumbutso chake choyera.”