Wolembedwa ndi Mateyu 4:1-25
4 Kenako mzimu unatsogolera Yesu kuchipululu ndipo kumeneko anayesedwa+ ndi Mdyerekezi.+
2 Atasala kudya masiku 40 masana ndi usiku, anamva njala.
3 Ndiyeno Woyesayo+ anabwera nʼkumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani miyalayi kuti isanduke mitanda ya mkate.”
4 Koma iye anayankha kuti, “Malemba amati: ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu alionse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.’”*+
5 Kenako Mdyerekezi anamutenga nʼkupita naye mumzinda woyera,+ ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi*+
6 nʼkumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu mudziponye pansi, paja Malemba amati: ‘Iye adzalamula angelo ake zokhudza inu,’ komanso amati, ‘Adzakunyamulani mʼmanja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala.’”+
7 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amanenanso kuti: ‘Yehova* Mulungu wanu musamamuyese.’”+
8 Kenako Mdyerekezi anamutenganso nʼkupita naye paphiri lalitali kwambiri ndipo anamuonetsa maufumu onse apadziko ndi ulemerero wawo.+
9 Ndiyeno anamuuza kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutagwada pansi kamodzi kokha nʼkundilambira.”
10 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Choka Satana! Chifukwa Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira+ ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”+
11 Kenako Mdyerekezi uja anamusiya+ ndipo kunabwera angelo nʼkuyamba kumutumikira.+
12 Tsopano Yesu atamva kuti Yohane amutsekera mundende,+ anachoka kumeneko nʼkupita ku Galileya.+
13 Kenako atachoka ku Nazareti, anafika ku Kaperenao+ nʼkupeza malo okhala mʼmbali mwa nyanja mʼzigawo za Zebuloni ndi Nafitali,
14 kuti mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yesaya akwaniritsidwe. Iye ananena kuti:
15 “Anthu amene akukhala mʼdziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, mʼmbali mwa msewu wakunyanja kutsidya lina la Yorodano, ku Galileya kumene kunkakhala anthu a mitundu ina,
16 anthu amene ankakhala mumdima anaona kuwala kwakukulu, ndipo anthu amene ankakhala mʼdera lamthunzi wa imfa, kuwala+ kunawaunikira.”+
17 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira kuti: “Lapani, chifukwa Ufumu wakumwamba wayandikira.”+
18 Pamene ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya,* Yesu anaona amuna awiri apachibale akuponya ukonde wophera nsomba mʼnyanja. Iwo anali asodzi ndipo mayina awo anali Simoni wotchedwa Petulo+ ndi Andireya.+
19 Iye anawauza kuti: “Nditsatireni ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.”+
20 Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo nʼkumutsatira.+
21 Atadutsa pamenepo, anaona amuna enanso awiri apachibale, Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane.+ Iwo anali mʼngalawa limodzi ndi bambo awo, a Zebedayo, akusoka maukonde awo, ndipo anawaitana.+
22 Nthawi yomweyo anasiya ngalawa ija ndi bambo awo nʼkumutsatira.
23 Atatero, anayendayenda mʼGalileya+ yense ndipo ankaphunzitsa mʼmasunagoge+ mwawo, ankalalikira uthenga wabwino wa Ufumu komanso ankachiritsa matenda amtundu uliwonse amene anthu ankadwala.+
24 Choncho mbiri yake inafalikira mu Siriya monse. Anthu anamubweretsera onse amene ankadwala matenda osiyanasiyana komanso amene ankamva kupweteka mʼthupi,+ ogwidwa ndi ziwanda,+ akhunyu+ komanso anthu akufa ziwalo ndipo iye anawachiritsa.
25 Choncho anthu ambirimbiri ochokera ku Galileya, ku Dekapoli,* ku Yerusalemu, ku Yudeya komanso kutsidya lina la Yorodano, anamutsatira.
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “anamukweza pamalo okwera kwambiri a kachisi.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ MʼBaibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesarete komanso nyanja ya Tiberiyo.
^ Kapena kuti, “Chigawo cha Mizinda 10.”