Nehemiya 12:1-47
12 Ansembe ndi Alevi amene anapita ndi Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa+ ndi awa: Seraya, Yeremiya, Ezara,
2 Amariya, Maluki, Hatusi,
3 Sekaniya, Rehumu, Meremoti,
4 Ido, Ginetoi, Abiya,
5 Miyamini, Maadiya, Biliga,
6 Semaya, Yoyaribi, Yedaya,
7 Salelu, Amoki, Hilikiya ndi Yedaya. Amenewa anali atsogoleri a ansembe komanso a abale awo mʼmasiku a Yesuwa.
8 Ndiyeno panali Alevi awa: Yesuwa, Binui, Kadimiyeli,+ Serebiya, Yuda ndiponso Mataniya,+ amene ankatsogolera nyimbo zotamanda Mulungu limodzi ndi abale ake.
9 Ndipo abale awo, Bakibukiya ndi Uni, ankaima moyangʼanizana nawo nʼkumagwira ntchito ya ulonda.*
10 Yesuwa anabereka Yoyakimu, Yoyakimu anabereka Eliyasibu,+ Eliyasibu anabereka Yoyada.+
11 Yoyada anabereka Yonatani ndipo Yonatani anabereka Yaduwa.
12 Mʼmasiku a Yoyakimu anthu awa ndi amene anali ansembe, atsogoleri a nyumba za makolo: Woimira nyumba ya Seraya+ anali Meraya, woimira nyumba ya Yeremiya anali Hananiya.
13 Woimira nyumba ya Ezara+ anali Mesulamu, woimira nyumba ya Amariya anali Yehohanani.
14 Woimira nyumba ya Maluka anali Yonatani, woimira nyumba ya Sebaniya anali Yosefe.
15 Woimira nyumba ya Harimu+ anali Adena, woimira nyumba ya Merayoti anali Helikai.
16 Woimira nyumba ya Ido anali Zekariya, woimira nyumba ya Ginetoni anali Mesulamu.
17 Woimira nyumba ya Abiya+ anali Zikiri, woimira nyumba ya Miniyamini anali . . . ,* woimira nyumba ya Moadiya anali Pilitai.
18 Woimira nyumba ya Biliga+ anali Samuwa, woimira nyumba ya Semaya anali Yehonatani.
19 Woimira nyumba ya Yoyaribi anali Matenai, woimira nyumba ya Yedaya+ anali Uzi.
20 Woimira nyumba ya Salai anali Kalai, woimira nyumba ya Amoki anali Ebere.
21 Woimira nyumba ya Hilikiya anali Hasabiya ndipo woimira nyumba ya Yedaya anali Netaneli.
22 Mʼmasiku a Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa,+ mayina a atsogoleri a nyumba za makolo za Alevi, ankawalemba ngati mmene ankachitira ndi ansembe mpaka kudzafika mʼnthawi ya ufumu wa Dariyo wa ku Perisiya.
23 Alevi amene anali atsogoleri a nyumba za makolo ankalembedwa mʼbuku la zochitika za pa nthawi imeneyo mpaka kudzafika mʼmasiku a Yohanani, mwana wa Eliyasibu.
24 Atsogoleri a Alevi anali Hasabiya, Serebiya ndi Yesuwa+ mwana wa Kadimiyeli.+ Ndipo abale awo ankaima moyangʼanizana nawo nʼkumatamanda ndi kuyamika Mulungu mogwirizana ndi malangizo a Davide,+ munthu wa Mulungu woona. Gulu lililonse la alonda linaima moyandikana ndi gulu lina la alonda.
25 Mataniya,+ Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu+ ankalondera mageti.+ Iwo ankalondera zipinda zosungira zinthu zomwe zinali pafupi ndi mageti.
26 Anthu amenewa ankatumikira mʼmasiku a Yoyakimu mwana wa Yesuwa+ amene anali mwana wa Yozadaki, komanso mʼmasiku a Nehemiya amene anali bwanamkubwa, ndi Ezara+ amene anali wansembe komanso wokopera Malemba.
27 Ndiyeno mwambo wotsegulira mpanda wa Yerusalemu uli pafupi, anthu anafunafuna Alevi mʼmadera onse amene ankakhala nʼkubwera nawo ku Yerusalemu. Anachita izi kuti potsegulira mpandawo pakhale kusangalala, kuimba nyimbo zoyamika Mulungu+ ndiponso kuimba pogwiritsa ntchito zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze.
28 Ana a oimbawo* anasonkhana pamodzi kuchokera mʼchigawo,* mʼmadera onse ozungulira Yerusalemu komanso mʼmidzi yonse kumene Anetofa ankakhala.+
29 Ena anachokera ku Beti-giligala+ komanso mʼmadera a ku Geba+ ndi ku Azimaveti,+ chifukwa oimbawo anamanga midzi yawo kuzungulira Yerusalemu yense.
30 Ndiyeno ansembe ndi Alevi anadziyeretsa nʼkuyeretsanso anthu,+ mageti+ ndi mpandawo.+
31 Kenako ndinabwera ndi akalonga a Yuda pamwamba pa mpandawo. Ndinaikanso magulu akuluakulu awiri oimba nyimbo zoyamika Mulungu ndiponso magulu ena oti aziwatsatira pambuyo. Gulu lina la oimba linkayenda pampandawo mbali yakumanja kulowera ku Geti la Milu ya Phulusa.+
32 Hoshaya ndi hafu ya akalonga a Yuda ankayenda pambuyo pa oimbawo
33 pamodzi ndi Azariya, Ezara, Mesulamu,
34 Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya.
35 Analinso ndi ena mwa ana a ansembe oimba malipenga:+ Zekariya mwana wa Yonatani. Yonatani anali mwana wa Semaya, Semaya anali mwana wa Mataniya, Mataniya anali mwana wa Mikaya, Mikaya anali mwana wa Zakuri ndipo Zakuri anali mwana wa Asafu.+
36 Panalinso Semaya, Azareli, Milalai, Gilelai, Maai, Netaneli, Yuda ndi Haneni, abale ake a Zekariya. Anali ndi zipangizo zoimbira za Davide,+ munthu wa Mulungu woona, ndipo amene ankawatsogolera anali Ezara+ wokopera Malemba.*
37 Oimbawo atafika pa Geti la Kukasupe,+ gulu lowatsatira lija lili pambuyo pawo, anayenda pamalo okwera a mpandawo kudutsa pamasitepe+ ochokera ku Mzinda wa Davide+ mpaka kukafika kumtunda kwa Nyumba ya Davide.+ Kenako anafika ku Geti la Kumadzi, chakumʼmawa.
38 Gulu lina loimba nyimbo zoyamika Mulungu linkayenda kumanzere, ndipo ine ndi hafu ya anthuwo tinkabwera pambuyo pawo. Oimbawo ankayenda pampandawo, kudutsa pamwamba pa Nsanja ya Mauvuni+ mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+
39 Anadutsanso pamwamba pa Geti la Efuraimu,+ Geti la Mzinda Wakale,+ Geti la Nsomba+ mpaka kukafika pa Nsanja ya Hananeli,+ Nsanja ya Meya ndi ku Geti la Nkhosa,+ ndipo anaima pa Geti la Alonda.
40 Kenako magulu awiri oimba nyimbo zoyamikawo anaima panyumba ya Mulungu woona ndipo ine ndi atsogoleri amene ndinali nawo tinaimanso pomwepo.
41 Panafikanso ansembe otsatirawa okhala ndi malipenga: Eliyakimu, Maaseya, Miniyamini, Mikaya, Elioenai, Zekariya, Hananiya,
42 Maaseya, Semaya, Eliezara, Uzi, Yehohanani, Malikiya, Elamu ndi Ezeri. Oimbawo anaimba mokweza ndipo amene ankawatsogolera anali Izirahiya.
43 Pa tsiku limenelo anapereka nsembe zambiri ndipo anasangalala+ chifukwa Mulungu woona anawachititsa kuti asangalale kwambiri. Akazi ndi ana nawonso anasangalala+ moti phokoso lachisangalalo ku Yerusalemu linamveka kutali.+
44 Pa tsikuli anasankha amuna kuti aziyangʼanira nyumba zosungiramo+ zopereka,+ mbewu zoyambirira kucha+ ndiponso chakhumi.+ Anawapatsa udindo woti azitutira mʼnyumbamo magawo oyenera kuperekedwa kwa ansembe ndi Alevi+ mogwirizana ndi Chilamulo,+ kuchokera mʼminda yonse yamʼmizinda yawo. Popeza anthu a ku Yuda anasangalala chifukwa cha ansembe ndi Alevi amene ankatumikira.
45 Ansembe ndi Alevi anayamba kugwira ntchito ya Mulungu wawo ndiponso kusunga lamulo lakuti azikhala oyera, ngati mmene ankachitira oimba ndi alonda apageti, mogwirizana ndi malangizo a Davide ndi mwana wake Solomo.
46 Kalelo mʼmasiku a Davide ndi Asafu, kunali atsogoleri a anthu oimba ndiponso a nyimbo zotamanda ndi kuyamika Mulungu.+
47 Mʼmasiku a Zerubabele+ komanso a Nehemiya, Aisiraeli onse ankapereka magawo a chakudya kwa oimba+ ndi alonda apageti+ mogwirizana ndi zimene ankafunikira tsiku lililonse. Ankaikanso padera gawo lina la Alevi+ ndipo Aleviwo ankaikanso padera gawo la mbadwa za Aroni.
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “akamachita utumiki wawo.”
^ Zikuoneka kuti mʼMalemba a Chiheberi sanamutchule dzina.
^ Kapena kuti, “Ana a oimba ochita kuphunzitsidwawo.”
^ Chimenechi chinali chigawo cha Yorodano.
^ Kapena kuti, “mlembi.”