Nyimbo ya Solomo 7:1-13
7 “Mapazi ako akukongola kwambiri munsapato zako,Iwe mwana wamkazi wolemekezeka.
Ntchafu zako nʼzoumbidwa bwino ngati zinthu zodzikongoletsera,Ntchito ya manja a munthu waluso.
2 Mchombo wako uli ngati mbale yolowa.
Vinyo wosakaniza bwino asasowepo.
Mimba yako ili ngati mulu wa tirigu,Wozunguliridwa ndi maluwa.
3 Mabere ako awiri ali ngati ana awiri a insa,Ana amapasa a insa.+
4 Khosi lako+ lili ngati nsanja ya mnyanga wa njovu.+
Maso ako+ ali ngati madamu a madzi a ku Hesiboni,+Amene ali pafupi ndi geti la Bati-rabimu.
Mphuno yako ili ngati nsanja ya ku Lebanoni,Imene inayangʼana cha ku Damasiko.
5 Mutu wako ndi wokongola ngati phiri la Karimeli,+Ndipo tsitsi lako lopotanapotana+ lili ngati ubweya wa nkhosa wapepo.+
Mfumu yakopeka* ndi tsitsi lako lalitali lokongolalo.
6 Ndiwe wokongola kwambiri mtsikana iwe ndipo ndiwe wosangalatsa,Kuposa zinthu zina zonse zimene zimasangalatsa mtima wa munthu.
7 Ndiwe wamtali ngati mtengo wa kanjedza,Ndipo mabere ako ali ngati zipatso zake.+
8 Ine ndinanena kuti, ‘Ndikwera mtengo wa kanjedzaKuti ndikathyole nthambi zake zokhala ndi zipatso.’
Mabere ako akhale ngati phava la zipatso za mpesa,Ndipo mpweya wamʼkamwa mwako ununkhire ngati maapozi,
9 Ndipo mʼkamwa mwako mununkhire ngati vinyo wabwino kwambiri.”
“Adutse mwamyaa kukhosi kwa wokondedwa wanga,Ngati vinyo amene amadutsa mwamyaa pakamwa nʼkuyambitsa tulo kwa amuna.
10 Wachikondi wangayo, ine ndine wakewake,+Ndipo iye amalakalaka ineyo.
11 Bwera wachikondi wanga,Tiye tipite kumunda.Tiye tikakhale pakati pa maluwa a hena.+
12 Tiye tilawirire mʼmamawa tipite kuminda ya mpesa.Tikaone ngati mitengo ya mpesa yaphukira,Ngati maluwa amasula+Ngati mitengo ya makangaza yachita maluwa.+
Kumeneko ndikakusonyeza chikondi changa.+
13 Zipatso za mandereki*+ zikununkhira,Pamakomo olowera kunyumba zathu pali zipatso zosiyanasiyana zokoma kwambiri.+
Ndakusungira zipatso zatsopano ndi zakale zomwe,Iwe wachikondi wanga.”
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “yatengeka.”
^ “Mandereki” ndi chitsamba cha mʼgulu la mbatata, chimene chimabereka zipatso.