Oweruza 15:1-20

  • Samisoni anabwezera Afilisiti (1-20)

15  Kenako, pa nthawi yokolola tirigu, Samisoni anapita kukaona mkazi wake uja ndipo anatenga kamwana ka mbuzi. Atafika anati: “Ndikufuna ndilowe kuchipinda kwa mkazi wanga.” Koma bambo a mkaziyo anamukaniza kulowa. 2  Iwo anati: “Ine ndinkaganiza kuti unadana naye,+ choncho ndinamʼpereka kwa mmodzi wa anyamata amene ankakhala nawe aja.+ Mngʼono wakeyu ndi wokongola kuposa iyeyu. Bwanji utenge ameneyu mʼmalomwake?” 3  Koma Samisoni anati: “Ulendo uno sindikhala ndi mlandu ndi Afilisiti ndikawachitira zoipa.” 4  Choncho Samisoni ananyamuka nʼkukagwira nkhandwe 300. Kenako anatenga nkhandwezo ziwiriziwiri nʼkuzimanga michira. Atatero, anaika muuni umodzi pakati pa michira iwiriyo. 5  Kenako anayatsa miyuniyo ndi moto, nʼkukusira nkhandwezo mʼminda ya Afilisti ya mbewu zosakolola. Choncho anayatsa chilichonse, kuyambira mitolo ya mbewu, mbewu zosakolola, minda ya mpesa komanso minda ya maolivi. 6  Zitatero, Afilisiti anafunsa kuti: “Wachita zimenezi ndi ndani?” Ndiyeno anauzidwa kuti: “Ndi Samisoni, mkamwini wa munthu wa ku Timuna uja, chifukwa munthuyu anatenga mkazi wa Samisoni nʼkumupereka kwa mmodzi mwa anyamata amene ankakhala ndi Samisoni ngati anzake a mkwati.”+ Afilisiti atamva zimenezi anapita kukatentha ndi moto mtsikanayo pamodzi ndi bambo ake.+ 7  Koma Samisoni anawauza kuti: “Ngati khalidwe lanu ndi limeneli, ndiye sindikusiyani mpaka ndibwezere.”+ 8  Ndiyeno anayamba kuwapha mmodzimmodzi. Kenako anapita nʼkumakakhala kuphanga la thanthwe la Etami. 9  Patapita nthawi, Afilisiti anabwera nʼkumanga msasa ku Yuda ndipo ankayendayenda ku Lehi.+ 10  Ndiyeno anthu a ku Yuda anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kudzatiukira?” Iwo anayankha kuti: “Tabwera kudzagwira* Samisoni kuti timʼchite zimene iye watichitira.” 11  Zitatero, amuna 3,000 a ku Yuda anapita kuphanga la thanthwe la Etami nʼkuuza Samisoni kuti: “Kodi iwe, sukudziwa kuti Afilisiti ndi amene akutilamulira?+ Ndiye nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi?” Iye anawayankha kuti: “Ndawachita zimene iwo anandichitira.” 12  Koma iwo anamuuza kuti: “Tabwera kudzakugwira* kuti tikakupereke kwa Afilisiti.” Samisoni anayankha kuti: “Lumbirani kuti inuyo simundichitira chilichonse choipa.” 13  Iwo anamuyankha kuti: “Ayi, sitikupha. Tingokumanga nʼkukakupereka kwa iwowo.” Choncho anamʼmanga ndi zingwe ziwiri zatsopano nʼkumʼtulutsa kuphangako. 14  Atafika naye ku Lehi, Afilisiti nʼkumuona, anafuula chifukwa chosangalala. Ndiyeno mzimu wa Yehova unamupatsa mphamvu,+ ndipo zingwe zimene anamʼmanga nazo manja zija zinadukaduka ngati ulusi wowauka ndi moto nʼkugwa pansi.+ 15  Zitatero, anapeza fupa laliwisi la nsagwada za bulu wamphongo ndipo analitenga nʼkupha nalo amuna 1,000.+ 16  Kenako Samisoni anati: “Ndi fupa la nsagwada za bulu, milumilu! Ndi fupa la nsagwada za bulu, ndapha anthu 1,000.”+ 17  Atamaliza kulankhula zimenezi, anataya fupalo ndipo malowo anawapatsa dzina lakuti Ramati-lehi.*+ 18  Ndiyeno anamva ludzu koopsa, ndipo anafuulira Yehova kuti: “Ndinu amene mwandipulumutsa ine mtumiki wanu. Ndiye kodi ndife ndi ludzu, nʼkufera mʼmanja mwa anthu osadulidwa?” 19  Choncho Mulungu anangʼamba nthaka ku Lehi ndipo panayamba kutuluka madzi.+ Samisoni atamwa madziwo, ludzu lake linatha ndipo anapezanso mphamvu. Nʼchifukwa chake anapatsa malowo dzina lakuti Eni-hakore.* Malo amenewa ali ku Lehi mpaka lero. 20  Samisoni anaweruza Isiraeli zaka 20 pa nthawi ya Afilisiti.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kudzamanga.”
Kapena kuti, “kudzakumanga.”
Kutanthauza “Malo Okwezeka a Fupa la Nsagwada.”
Kutanthauza “Kasupe wa Munthu Wofuula.”