Yesaya 23:1-18

  • Uthenga wokhudza Turo (1-18)

23  Uwu ndi uthenga wokhudza Turo:+ Lirani mofuula inu sitima zapamadzi za ku Tarisi,+ Chifukwa chakuti doko lawonongedwa ndipo simungathenso kufikapo. Anthu amva zimenezi ali kudziko la Kitimu.+  2  Khalani chete inu anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Amalonda a ku Sidoni,+ amene amawoloka nyanja, akulemeretsani.  3  Mbewu za ku Sihori,* zokolola zakumtsinje wa Nailo,Zimene zinkakubweretserani ndalama, zinadutsa pamadzi ambiri,+Nʼkubweretsa phindu la anthu a mitundu ina.+  4  Chita manyazi iwe Sidoni, iwe mzinda wotetezeka umene uli mʼmbali mwa nyanja,Chifukwa nyanja yanena kuti: “Sindinamvepo zowawa zapobereka, ndipo sindinaberekepo,Komanso sindinalerepo anyamata kapena atsikana.”*+  5  Anthu adzamva chisoni chachikulu akadzamva za Turo,+Ngati mmene anamvera chisoni atamva za Iguputo.+  6  Wolokerani ku Tarisi. Lirani mofuula, inu anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja.  7  Kodi uwu ndi mzinda wanu uja, umene unali wosangalala kuyambira kalekale, kuyambira pachiyambi pake? Mapazi ake ankautengera kumayiko akutali kuti ukakhale kumeneko.  8  Ndi ndani waganiza kuti achitire Turo zinthu zimenezi,Mzinda umene unkaveka anthu zisoti zachifumu,Umene amalonda ake anali akalonga,Umenenso ochita malonda ake ankalemekezedwa padziko lonse lapansi?+  9  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndi amene waganiza zochita zimenezi,Kuti athetse kukongola kwa mzindawo komanso kunyada kwake,Kuti achititse manyazi anthu onse amene ankalemekezedwa padziko lonse lapansi.+ 10  Iwe mwana wamkazi wa Tarisi, sefukira mʼdziko lako ngati kusefukira kwa mtsinje wa Nailo. Kulibenso doko la sitima zapanyanja.+ 11  Mulungu watambasulira dzanja lake panyanja.Wagwedeza maufumu. Yehova walamula kuti malo otetezeka a ku Foinike awonongedwe.+ 12  Iye wanena kuti: “Sudzasangalalanso,+Iwe namwali woponderezedwa, mwana wamkazi wa Sidoni. Nyamuka, wolokera ku Kitimu.+ Koma ngakhale kumeneko, sukapezako mpumulo.” 13  Taonani dziko la Akasidi.+ Anthu awa, osati Asuri,+Ndi amene anapanga mzindawo kuti ukhale malo okhala nyama zamʼchipululu. Amanga nsanja zawo zomenyerapo nkhondo.Agumula nyumba zake zachifumu zokhala ndi mpanda wolimba,+Ndipo iwo asandutsa mzindawo kukhala bwinja lokhalokha. 14  Lirani mofuula, inu sitima zapamadzi za ku Tarisi,Chifukwa malo anu otetezeka awonongedwa.+ 15  Pa tsiku limenelo, Turo adzaiwalidwa kwa zaka 70,+ mofanana ndi zaka za moyo wa* mfumu imodzi. Pamapeto pa zaka 70 zimenezo, Turo adzakhala ngati hule wamʼnyimbo yakuti: 16  “Iwe hule amene unaiwalidwa, tenga zeze nʼkumazungulira mumzinda. Imba zeze wakoyo mwaluso.Imba nyimbo zambiri,Kuti anthu akukumbukire.” 17  Pamapeto pa zaka 70, Yehova adzakumbukira Turo. Mzindawo udzayambiranso kulandira malipiro ndipo udzachita uhule ndi maufumu onse apadziko lapansi. 18  Koma phindu lake ndi malipiro akewo zidzakhala zopatulika kwa Yehova. Zinthu zimenezi sizidzasungidwa kapena kuikidwa pambali, chifukwa malipiro akewo adzakhala a anthu okhala pamaso pa Yehova, kuti anthuwo azidya mpaka kukhuta ndiponso kuti azivala zovala zokongola.+

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wotuluka mumtsinje wa Nailo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anamwali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi masiku a.”