Yesaya 54:1-17
54 “Fuula mosangalala iwe mkazi amene sunaberekepo mwana.+
Iwe amene sunamvepo zowawa za pobereka,+ sangalala ndipo ufuule mosangalala.+Chifukwa ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiriKuposa ana a mkazi yemwe ali ndi mwamuna,”*+ akutero Yehova.
2 “Kulitsa tenti yako.+
Tambasula nsalu za chihema chako chachikulu.
Usaumire pochita zimenezi. Talikitsa zingwe za tenti yakoNdipo ulimbitse zikhomo zake.+
3 Chifukwa mudzafalikira mbali yakumanja ndi kumanzere.
Ana ako adzatenga mitundu ya anthu kukhala yawo,Ndipo adzakhala mʼmizinda imene inasiyidwa yabwinja.+
4 Usachite mantha,+ chifukwa sudzachititsidwa manyazi.+Usachite manyazi, chifukwa sudzakhumudwitsidwa.
Iwe udzaiwala manyazi apaubwana wako,Ndipo sudzakumbukiranso kunyozeka kwa paumasiye wako.
5 Chifukwa Wokupanga Wamkulu+ ali ngati mwamuna* wako,+Dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,Ndipo Woyera wa Isiraeli ndiye Wokuwombola.+
Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.+
6 Yehova anakuitana ngati kuti unali mkazi wosiyidwa komanso amene ali ndi chisoni,*+Ngati mkazi amene anakwatiwa ali mtsikana kenako nʼkusiyidwa,” akutero Mulungu wako.
7 “Ndinakusiya kwa kanthawi kochepa,Koma ndidzakusonkhanitsa pamodzi mwachifundo chachikulu.+
8 Chifukwa cha mkwiyo wanga waukulu ndinakubisira nkhope yanga kwa kanthawi,+Koma chifukwa cha chikondi changa chokhulupirika chimene sichidzatha ndidzakuchitira chifundo,”+ akutero Yehova, Wokuwombola.+
9 “Kwa ine, zimenezi zili ngati masiku a Nowa.+
Monga mmene ndinalumbirira kuti madzi amʼnthawi ya Nowa sadzamizanso dziko lapansi,+Ndikulumbiranso kuti sindidzakukwiyira kapena kukudzudzula.+
10 Mapiri akhoza kuchotsedwa,Ndipo zitunda zikhoza kugwedezeka,Koma chikondi changa chokhulupirika sichidzachotsedwa pa iwe,+Ndipo pangano langa lamtendere silidzagwedezeka,”+ akutero Yehova, amene akukuchitira chifundo.+
11 “Iwe mkazi amene uli pamavuto,+ amene ukukankhidwa ndi mphepo yamkuntho ndiponso amene sunatonthozedwe,+Ine ndikukumanga ndi miyala komanso simenti yolimba,Ndipo ndikumanga maziko ako ndi miyala ya safiro.+
12 Nsanja za mpanda wa mzinda wako ndidzazimanga ndi miyala ya rube,Mageti ako ndidzawamanga ndi miyala yonyezimira,*Ndipo mpanda wonse wa mzinda wako ndidzaumanga ndi miyala yamtengo wapatali.
13 Ana ako onse azidzaphunzitsidwa ndi Yehova,+Ndipo mtendere wa ana ako udzakhala wochuluka.+
14 Udzakhazikika molimba mʼchilungamo.+
Palibe amene adzakupondereze,+Sudzaopa kanthu ndipo palibe chimene chidzakuchititse mantha,Chifukwa palibe chilichonse choopsa chimene chidzakuyandikire.+
15 Ngati aliyense atakuukira,Sadzakhala kuti watumidwa ndi ine.
Aliyense amene adzakuukire adzagwa chifukwa cha iwe.+
16 Ine ndi amene ndinalenga mmisiri,Amene amauzira moto wamakalaNʼkupanga chida chankhondo ndi luso lake.
Ine ndinalenganso munthu wowononga kuti aziwononga.+
17 Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana,+Ndipo lilime lililonse limene lidzalimbane nawe pamlandu udzalitsutsa.
Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova,Ndipo chilungamo chawo nʼchochokera kwa ine,” akutero Yehova.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “ali ndi mbuye.”
^ Kapena kuti, “ali ngati mbuye.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wopwetekedwa mtima.”
^ Kapena kuti, “miyala yofiira ngati moto.”