Yesaya 6:1-13
6 Chaka chimene Mfumu Uziya inamwalira,+ ine ndinaona Yehova atakhala pampando wachifumu wolemekezeka komanso wokwezeka,+ ndipo zovala zake zinadzaza mʼkachisi.
2 Pamwamba pake panali aserafi. Mserafi aliyense anali ndi mapiko 6. Aliyense anaphimba nkhope yake ndi mapiko awiri, anaphimba mapazi ake ndi mapiko awiri ndipo mapiko ena awiriwo ankaulukira.
3 Aliyense ankauza mnzake kuti:
“Woyera, woyera, woyera ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”
4 Chifukwa cha mawu ofuulawo, mafelemu a zitseko anayamba kunjenjemera ndipo mʼnyumbamo munadzaza utsi.+
5 Kenako ndinanena kuti: “Tsoka kwa ine!
Maso anga aona Mfumu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.Ndifa ine basi,Chifukwa ndine munthu wa milomo yodetsedwa,Ndipo ndikukhala pakati pa anthu a milomo yodetsedwa.”+
6 Zitatero, mserafi mmodzi anaulukira kwa ine. Mʼmanja mwake munali khala lamoto+ limene analitenga paguwa lansembe ndi chopanira.+
7 Iye anakhudza pakamwa panga nʼkunena kuti:
“Taona! Khalali lakhudza milomo yako.
Zolakwa zako zachotsedwa,Ndipo tchimo lako laphimbidwa.”
8 Kenako ndinamva mawu a Yehova akufunsa kuti: “Kodi nditumize ndani, ndipo ndi ndani amene apite mʼmalo mwa ife?”+ Ine ndinayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”+
9 Iye anamuuza kuti, “Pita ukauze anthu awa kuti:
‘Mudzamva mobwerezabwerezaKoma simudzamvetsetsa.Mudzaona mobwerezabwereza,Koma simudzazindikira chilichonse.’+
10 Uchititse anthu awa kuumitsa mtima wawo,+Uchititse makutu awo kuti asamamve,+Ndipo umate maso awo,Kuti asamaone ndi maso awowo,Ndiponso kuti asamamve ndi makutu awo,Nʼcholinga choti mtima wawo usamvetse zinthuKomanso kuti asabwerere nʼkuchiritsidwa.”
11 Atatero ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, inu Yehova?” Iye anayankha kuti:
“Mpaka mizinda yawo itawonongedwa nʼkukhala mabwinjaMpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamoNdiponso mpaka dziko litawonongekeratu nʼkukhala bwinja.+
12 Mpaka Yehova atathamangitsira anthu kutali+Ndiponso mpaka mbali yaikulu ya dzikolo itakhala bwinja.
13 Koma mʼdzikolo mudzakhalabe chakhumi ndipo chidzawotchedwanso ngati mtengo waukulu, ndiponso ngati chimtengo chachikulu, chimene chikadulidwa pamatsala chitsa. Mbewu* yopatulika idzakhala chitsa chake.”
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mbadwa.”