Yobu 24:1-25

  • Yankho la Yobu likupitirira (1-25)

    • ‘Nʼchifukwa chiyani Mulungu sanakhazikitse nthawi’ (1)

    • Ananena kuti Mulungu amalola kuti zinthu zoipa zizichitika (12)

    • Anthu ochimwa amakonda mdima (13-17)

24  “Nʼchifukwa chiyani Wamphamvuyonse sanakhazikitse nthawi yachiweruzo?+ Nʼchifukwa chiyani anthu amene amamudziwa sanaone tsiku lake lachiweruzo?  2  Anthu amasuntha zizindikiro za malire.+Iwo amaba ziweto nʼkuzipititsa pamalo awo odyetsera ziweto.  3  Amathamangitsa bulu wa ana amasiyeNdipo amalanda ngʼombe yamphongo ya mkazi wamasiye kuti ikhale chikole.+  4  Amachititsa kuti osauka athawe mumsewu.Anthu ovutika apadziko lapansi amabisala akawaona.+  5  Osaukawo amafunafuna chakudya ngati abulu+ amʼchipululu,Amafunafuna chakudya cha ana awo mʼchipululu.  6  Amakolola mʼmunda mwa munthu winaNdipo amakunkha mʼmunda wa mpesa wa munthu woipa.  7  Osaukawo amakhala usiku wonse ali maliseche,+Amakhala pamphepo opanda chofunda.  8  Amanyowa ndi mvula mʼmapiri,Ndipo amakhala pafupi ndi matanthwe chifukwa chakuti alibe pobisala.  9  Oipa amalanda mwana wamasiye kumʼchotsa pabere.+Ndipo amatenga zovala za osauka kuti zikhale chikole,+ 10  Moti amakakamizika kuyenda maliseche,Komanso amasenza mitolo ya tirigu ali ndi njala. 11  Osaukawo amagwira ntchito mwakhama mʼmigula* ya mʼminda dzuwa likuswa mtengo.*Amaponda mphesa koma amakhala ndi ludzu.+ 12  Anthu amene akufa amakhala akubuula mumzinda.Anthu amene avulala koopsa amapempha* thandizo,+Koma Mulungu saona zimenezi ngati zolakwika.* 13  Pali ena amene amapandukira kuwala.+Iwo sazindikira njira zake,Ndipo sayenda mʼnjira zake. 14  Munthu wopha anthu amadzuka mʼmamawa.Iye amapha anthu ovutika komanso osauka,+Ndipo usiku amakhala wakuba. 15  Munthu wachigololo amadikira kuti kude madzulo.+Iye amati, ‘Palibe amene andione,’+ Ndipo amaphimba nkhope yake. 16  Mumdima anthu oipawo amathyola nyumba za anthu,Masana amadzitsekera mʼnyumba. Iwo amadana ndi kuwala.+ 17  Kwa iwo mʼmawa nʼchimodzimodzi ndi mdima wandiweyani,Amadziwa zoopsa zamumdima wandiweyani. 18  Koma iwo amatengedwa mwamsanga ndi madzi. Malo awo adzakhala otembereredwa.+ Sadzabwerera kuminda yawo ya mpesa. 19  Mofanana ndi madzi amunthaka* amene amauma mʼnyengo yachilimwe komanso kunja kukatentha,Anthu ochimwa nawonso amasowa akapita ku Manda.*+ 20  Mayi ake adzamuiwala* ndipo mphutsi zidzamudya. Iye sadzakumbukiridwanso.+ Ndipo kupanda chilungamo kudzathyoledwa ngati mtengo. 21  Iye amachitira zoipa mkazi wosabereka,Komanso amachitira nkhanza mkazi wamasiye. 22  Mulungu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake powononga anthu amphamvu.Ngakhale atakhala ndi mphamvu, iwo sadziwa ngati angakhalebe ndi moyo kapena ayi. 23  Mulungu amawalola kuti azidzidalira komanso kuti akhale otetezeka.+Koma maso ake amaona chilichonse chimene akuchita.*+ 24  Oipawo amakhala okwezeka kwa kanthawi, kenako nʼkutha.+ Iwo ali ngati ngala za tirigu zimene zimadulidwa nʼkuikidwa pamodzi.Amatsitsidwa+ ndipo amafa mofanana ndi anthu ena onse. 25  Choncho ndi ndani amene angapereke umboni wosonyeza kuti ndine wabodzaKapena kutsutsa mawu angawa?”

Mawu a M'munsi

Migula ndi mizera ikuluikulu. Ena amati milambala.
Mabaibulo ena amati, “amagwira ntchito yoyenga mafuta mʼminda ya anthu oipa.”
Kapena kuti, “Moyo wa anthu amene avulala umapempha.”
Mabaibulo ena amati, “Mulungu saimba aliyense mlandu wochita zoipa.”
Kapena kuti, “madzi oundana amene asungunuka.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mimba idzamuiwala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Koma maso ake ali pa njira zawo.”