Yobu 40:1-24

  • Mafunso enanso ochokera kwa Yehova (1-24)

    • Yobu anavomereza kuti alibe chonena (3-5)

    • “Kodi unganene kuti ndine wopanda chilungamo?” (8)

    • Mulungu anafotokoza mphamvu za mvuu (15-24)

40  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Yobu kuti:  2  “Kodi opezera ena chifukwa ayenera kutsutsana ndi Wamphamvuyonse?+ Amene akufuna kudzudzula Mulungu ayankhe.”+  3  Ndiyeno Yobu anayankha Yehova kuti:  4  “Ine ndine wopanda pake.+ Kodi ndingakuyankheni chiyani? Ndaika dzanja langa pakamwa.+  5  Ndalankhula kambirimbiri.Koma pano sindiyankha kapena kunena chilichonse.”  6  Ndiyeno Yehova anayankha Yobu kudzera mumphepo yamkuntho kuti:+  7  “Konzeka ngati mwamuna wamphamvu.Ndikufunsa mafunso ndipo iweyo undiyankhe.+  8  Kodi unganene kuti ndine wopanda chilungamo? Kodi ungandiweruze kuti ndine wolakwa kuti iweyo ukhale wolondola?+  9  Kodi uli ndi dzanja lamphamvu ngati la Mulungu woona?+Kapena kodi mawu ako angagunde ngati mabingu mofanana ndi mawu a Mulungu?+ 10  Udziveke ulemerero ndiponso mphamvu,Ndipo uvale ulemu ndi ulemerero. 11  Utulutse mkwiyo wonse umene uli nawo,Yangʼana aliyense amene ndi wodzikweza ndipo umutsitse. 12  Yangʼana aliyense wodzikweza ndipo umutsitse,Ndipo oipa uwaponderezere pamalo amene ali. 13  Uwabise onse mufumbi,Uwamange* nʼkuwaika mʼmalo amdima, 14  Ukatero ngakhale ine ndidzavomereza*Kuti dzanja lako lamanja lingakupulumutse. 15  Ine ndinapanga mvuu* ndipo ndinapanganso iweyo. Iyo imadya udzu ngati ngʼombe yamphongo. 16  Mphamvu zake zili mʼchiuno mwake,Ndipo minofu yapamimba pake ndi yamphamvu kwambiri. 17  Imalimbitsa mchira wake ngati mtengo wa mkungudza,Mitsempha yamʼntchafu zake ndi yolukanalukana. 18  Mafupa ake ali ngati mapaipi akopa,*Miyendo yake ili ngati ndodo zachitsulo. 19  Iyo ndi yoyamba komanso yaikulu kwambiri pa nyama zamtundu umenewu zimene Mulungu analenga.Amene anaipanga ndi yekhayo amene angaiyandikire ndi lupanga. 20  Mapiri amaipatsa chakudya,Ndipo nyama zonse zakutchire zimasewera mmenemo. 21  Imagona pansi pa mitengo yaminga,Pamthunzi wa mabango amʼmadambo. 22  Mitengo yaminga imaipatsa mthunzi,Ndipo imazunguliridwa ndi mitengo ya msondodzi yamʼchigwa.* 23  Mtsinje ukadzaza, iyo sichita mantha. Imalimba mtima ngakhale madzi a mu Yorodano+ atasefukira nʼkumaimenya kumaso. 24  Kodi alipo amene angaigwire iyo ikuonaKapena kubowola mphuno yake ndi ngowe?”*

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Umange nkhope zawo.”
Kapena kuti, “ndidzakuyamikira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Behemoti.”
Kapena kuti, “amkuwa.”
Kapena kuti, “yamʼkhwawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “msampha.”