Wolembedwa ndi Yohane 17:1-26

  • Pemphero lomaliza la Yesu ali ndi atumwi ake (1-26)

    • Anthu adzapeza moyo wosatha akadziwa Mulungu (3)

    • Akhristu sali mbali ya dziko (14-16)

    • “Mawu anu ndi choonadi” (17)

    • “Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu” (26)

17  Yesu atalankhula zinthu zimenezi, anakweza maso ake kumwamba nʼkunena kuti: “Atate, nthawi yafika. Lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni.+ 2  Inu mwapatsa mwana wanu ulamuliro pa anthu onse+ kuti onse amene inu mwamupatsa,+ awapatse moyo wosatha.+ 3  Moyo wosatha adzaupeza+ akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ndi woona,+ komanso za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.+ 4  Ndakulemekezani padziko lapansi,+ chifukwa ndamaliza kugwira ntchito imene munandipatsa.+ 5  Ndiye tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.+ 6  Anthu amene munawatenga mʼdziko nʼkundipatsa, ine ndawadziwitsa dzina lanu.+ Anali anu, koma munawapereka kwa ine ndipo iwo amvera mawu anu. 7  Tsopano adziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa inu, 8  chifukwa mawu amene munandipatsa ndawapereka kwa iwo.+ Iwo awalandira ndipo adziwa ndithu kuti ine ndinabwera ngati nthumwi yanu+ ndipo akhulupirira kuti ndinu amene munandituma.+ 9  Choncho ndikuwapempherera. Sindikupempherera dziko, koma ndikupempherera anthu amene mwandipatsa, chifukwa ndi anu. 10  Zinthu zonse zimene ine ndili nazo ndi zanu ndipo zinthu zanu zonse ndi zanga.+ Ine ndalemekezeka pakati pa anthu amene mwandipatsa. 11  Ine sindipitiriza kukhala mʼdzikoli chifukwa ndikubwera kwa inu, koma iwowo adakali mʼdzikoli.+ Atate Woyera, ayangʼanireni+ chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa, kuti akhale amodzi* ngati mmene ife tilili.+ 12  Pamene ndinali nawo limodzi, ndinkawayangʼanira+ chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa. Ine ndawateteza moti palibe aliyense wa iwo amene wawonongeka+ kupatulapo mwana wa chiwonongeko,+ kuti lemba likwaniritsidwe.+ 13  Koma tsopano ndikubwera kwa inu, ndipo ndikulankhula zimenezi pamene ndili mʼdziko kuti iwo akhale ndi chimwemwe chosefukira ngati chimene ine ndili nacho.+ 14  Iwo ndawapatsa mawu anu, koma dziko likudana nawo chifukwa sali mbali ya dziko,+ mofanana ndi ine amene sindili mbali ya dziko. 15  Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko, koma kuti muwateteze kwa woipayo.+ 16  Iwo sali mbali ya dziko,+ mofanana ndi ine amenenso sindili mbali ya dziko.+ 17  Ayeretseni* pogwiritsa ntchito choonadi.+ Mawu anu ndi choonadi.+ 18  Inu munanditumiza ine mʼdziko. Mofanana ndi zimenezi, inenso ndawatumiza mʼdziko.+ 19  Ndipo ine ndikudziyeretsa chifukwa cha iwo, kuti iwonso ayeretsedwe ndi choonadi. 20  Sindikupempherera awa okha, koma ndikupemphereranso amene amakhulupirira ine atamvetsera zimene iwo amaphunzitsa. 21  Ndikuchita zimenezi kuti onsewa akhale amodzi+ ngati mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana,+ kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife nʼcholinga choti dziko likhulupirire kuti inu munanditumadi. 22  Ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa, kuti iwo akhale amodzi ngati mmene ifenso tilili amodzi.+ 23  Ine ndikhale wogwirizana ndi iwo, inu mukhale wogwirizana ndi ine, kuti iwo akhale mumgwirizano weniweni,* kuti dziko lidziwe kuti inu munandituma ine komanso kuti mumawakonda ngati mmene mumandikondera ine. 24  Atate, ine ndikufuna kuti amene mwandipatsawa adzakhale limodzi ndi ine kumene ine ndidzakhale,+ kuti adzaone ulemerero wanga umene inu mwandipatsa, chifukwa munandikonda musanayale maziko a dziko.+ 25  Atate Wolungama, ndithudi dziko silikukudziwani,+ koma ine ndikukudziwani+ ndipo awa adziwa kuti inu munandituma. 26  Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo+ kuti iwonso azisonyeza chikondi ngati chimene inu munandisonyeza, kuti inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “azigwirizana.”
Kapena kuti, “Apatuleni.”
Kapena kuti, “akhale ogwirizana kwambiri.”