Yoswa 13:1-33

  • Madera amene anali asanalandidwe (1-7)

  • Kugawa malo a kumʼmawa kwa Yorodano (8-14)

  • Cholowa cha fuko la Rubeni (15-23)

  • Cholowa cha fuko la Gadi (24-28)

  • Cholowa cha Manase, kumʼmawa kwa Yorodano (29-32)

  • Yehova ndi cholowa cha Alevi (33)

13  Tsopano Yoswa anali atakalamba, ndipo anali ndi zaka zambiri.+ Choncho Yehova anamuuza kuti: “Iweyo wakalamba ndipo uli ndi zaka zambiri, koma madera oti alandidwe adakali ambiri. 2  Madera amene atsala ndi awa:+ Madera onse a Afilisiti ndi madera onse a Agesuri.+ 3  (Dera loyambira kukamtsinje kotuluka mu Nailo* kumʼmawa kwa Iguputo, kukafika kumpoto kumalire ndi Ekironi, lomwe linkaonedwa kuti ndi la Akanani.)+ Komanso madera a olamulira 5 a Afilisiti+ omwe ndi Gaza, Asidodi,+ Asikeloni,+ Gati+ ndi Ekironi,+ ndiponso dera la Aavimu.+ 4  Kumʼmwera kwatsala dera lonse la Akanani. Patsalanso mzinda wa Asidoni+ wotchedwa Meara, mpaka kukafika ku Afeki kumalire a Aamori, 5  dera la Agebala+ ndiponso dera lonse la Lebanoni chakumʼmawa, kuyambira ku Baala-gadi mʼmunsi mwa phiri la Herimoni mpaka ku Lebo-hamati.*+ 6  Ine ndidzathamangitsa pamaso pa Aisiraeli anthu onse okhala kudera lamapiri, kuchokera ku Lebanoni+ mpaka ku Misirepotu-maimu+ komanso Asidoni+ onse. Iweyo ungopereka maderawa kwa Aisiraeli+ kuti akhale cholowa chawo mogwirizana ndi zimene ndinakulamula.+ 7  Maderawa uwagawe kwa mafuko 9 ndiponso kwa hafu ya fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.”+ 8  Mose mtumiki wa Yehova anapereka cholowa kwa hafu ina ya fuko la Manase, kwa fuko la Rubeni ndi kwa fuko la Gadi, kutsidya lakumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano.+ 9  Cholowa chawo chinayambira kumzinda wa Aroweli+ umene uli mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni,+ ndiponso mzinda umene uli pakatikati pa chigwacho, kuphatikizapo malo onse okwera a Medeba mpaka kukafika ku Diboni. 10  Anawapatsanso mizinda yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori imene inkalamulira ku Hesiboni, mpaka kumalire ndi Aamoni.+ 11  Anapatsidwanso Giliyadi, dera la Agesuri, la Amaakati,+ phiri lonse la Herimoni ndi dera lonse la Basana+ mpaka ku Saleka.+ 12  Mafukowa anapatsidwanso dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Ogi mfumu ya Basana, imene inali kulamulira ku Asitaroti ndi ku Edirei. (Mfumu Ogi inali mmodzi mwa Arefai otsala.)+ Mose anagonjetsa anthu onsewa nʼkuwathamangitsa.+ 13  Koma Aisiraeli sanathamangitse+ Agesuri ndi Amaakati, ndipo iwo akukhalabe pakati pawo mpaka lero. 14  Fuko la Levi lokha ndi limene sanalipatse malo monga cholowa chawo.+ Cholowa chawo ndi nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ mogwirizana ndi zimene anawalonjeza.+ 15  Kenako Mose anagawira cholowa fuko la Rubeni motsatira mabanja awo. 16  Dera lawo linayambira ku Aroweli, mzinda umene uli mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakatikati pa chigwacho komanso malo onse okwera a Medeba. 17  Linafikanso ku Hesiboni ndi midzi yake yonse+ imene inali mʼmalo okwera, ku Diboni, ku Bamoti-baala komanso ku Beti-baala-meoni.+ 18  Linaphatikizaponso Yahazi,+ Kademoti,+ Mefaata,+ 19  Kiriyataimu, Sibima,+ Zereti-sahara, malo amene anali mʼphiri la kuchigwa, 20  Beti-peori, dera lotsetsereka la ku Pisiga,+ Beti-yesimoti,+ 21  mizinda yonse ya mʼmalo okwera ndiponso dziko lonse la Sihoni mfumu ya Aamori imene inali kulamulira ili ku Hesiboni.+ Mfumu imeneyi Mose anaigonjetsa+ limodzi ndi atsogoleri a ku Midiyani, Evi, Rekemu, Zuri, Hura, ndi Reba.+ Amenewa anali mafumu omwe anali pansi pa ulamuliro wa Sihoni ndipo ankakhala mʼdzikolo. 22  Balamu+ mwana wa Beori, wolosera zamʼtsogolo uja,+ anali mmodzi mwa anthu amene Aisiraeli anawapha ndi lupanga. 23  Malire a fuko la Rubeni anali mtsinje wa Yorodano. Dera limeneli linali cholowa cha anthu a fuko la Rubeni chimene anapatsidwa motsatira mabanja awo. Iwo anapatsidwa derali limodzi ndi mizinda komanso midzi ya kumeneko. 24  Komanso Mose anagawira cholowa fuko la Gadi motsatira mabanja awo. 25  Dera lawo linali mzinda wa Yazeri,+ mizinda yonse ya ku Giliyadi komanso hafu ya dziko la Aamoni,+ mpaka kukafika ku Aroweli kufupi ndi Raba.+ 26  Kuchokera ku Hesiboni+ linakafika ku Ramati-mizipe ndi ku Betonimu, ndiponso kuchokera ku Mahanaimu+ mpaka kumalire ndi Debiri. 27  Gawo lawolo linaphatikizaponso mizinda ya mʼchigwa ya Beti-harana, Beti-nimira,+ Sukoti,+ Zafoni ndi dera lotsala la dziko la Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.+ Mtsinje wa Yorodano ndi umene unali malire awo kuchokera kumunsi kwa nyanja ya Kinereti,*+ kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano. 28  Dera limeneli linali cholowa cha anthu a fuko la Gadi chimene anapatsidwa motsatira mabanja awo. Iwo anapatsidwa derali limodzi ndi mizinda komanso midzi ya kumeneko. 29  Komanso Mose anapereka cholowa kwa hafu ya fuko la Manase motsatira mabanja awo.+ 30  Dera lawo linayambira ku Mahanaimu,+ dera lonse la Basana, dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Mfumu Ogi ya Basana ndiponso midzi yonse yaingʼono ya Yairi+ ku Basana. Dera lawoli linali ndi matauni 60. 31  Mose anapereka hafu ya dera la Giliyadi, Asitaroti, Edirei+ ndi mizinda ya ufumu wa Ogi mʼdziko la Basana kwa ana a Makiri,+ mwana wa Manase. Anapereka dzikoli kwa hafu ya ana a Makiri motsatira mabanja awo. 32  Chimenechi ndi cholowa chimene Mose anawapatsa kuti chikhale chawo, pamene anali mʼchipululu cha Mowabu, kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano, chakumʼmawa kwa Yeriko.+ 33  Koma fuko la Alevi, Mose sanalipatse cholowa.+ Chifukwa cholowa chawo ndi Yehova Mulungu wa Isiraeli, mogwirizana ndi zimene anawalonjeza.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “loyambira ku Sihori.”
Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
Imeneyi ndi nyanja ya Genesareti yomwe inkadziwikanso kuti nyanja ya Galileya.