FUNSO 7
Kodi Baibulo Linaneneratu Zinthu Ziti Zokhudza Masiku Ano?
“Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina . . . Zonsezi ndi chiyambi cha mavuto aakulu.”
“Kudzakhala aneneri ambiri abodza ndipo adzasocheretsa anthu ambiri. Chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo, chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.”
“Mukadzamva phokoso la nkhondo ndi malipoti a nkhondo, musadzachite mantha. Zimenezi zikuyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.”
“Kudzachitika zivomerezi zamphamvu ndipo kudzakhala miliri ndi njala mʼmalo osiyanasiyana. Kudzaoneka zinthu zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikiro zodabwitsa.”
“Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi ena, onenera ena zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, ochitira anzawo zoipa, osamva za ena, odzitukumula chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.”