Yakobo ndi Labani Anachita Pangano Lamtendere
N’chifukwa chiyani Yakobo ndi Labani anaunjika mulu wamiyala?
-
Unali ngati umboni kwa anthu onse kuti anachita pangano la mtendere
-
Unkawakumbutsa kuti Yehova akuona ngati akukwaniritsa pangano lawo
Masiku anonso, Yehova amafuna kuti tizikhala mwamtendere ndi abale komanso alongo athu. Kodi zinthu zitatu zotsatirazi zingatithandize bwanji kuti tizikhala mwamtendere ndi ena?
-
Kukambirana momasuka.—Mt 5:23, 24
-
Kukhululukirana ndi mtima wonse.—Akl 3:13
-
Kukhala woleza mtima.—Aro 12:21