Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizigwiritsa Ntchito Mwanzeru Mabuku Ndiponso Magazini

Tizigwiritsa Ntchito Mwanzeru Mabuku Ndiponso Magazini

Yesu ananena kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mat. 10:8) Timatsatira malangizowa chifukwa sitilipiritsa anthu tikawapatsa Baibulo kapena mabuku ena. (2 Akor. 2:17) Komabe tizikumbukira kuti mabukuwa ndi amtengo wapatali chifukwa amakhala ndi mfundo zochokera m’Mawu a Mulungu. Pamafunikanso ndalama zambiri komanso pamakhala ntchito yaikulu kuti mabukuwa asindikizidwe ndiponso kutumizidwa kumipingo padziko lonse. Choncho tiyenera kungotenga mabuku ndi magazini omwe tingagwiritsedi ntchito.

Tizichita zinthu mozindikira tikamagawira mabuku ndi magazini ngakhale pamene tikulalikira pamalo opezeka anthu ambiri. (Mat. 7:6) M’malo mongogawira zinthu kwa anthu amene akudutsa, ndi bwino kukambirana nawo kaye kuti tione ngati ali ndi chidwi. Mafunso amene ali m’bokosili angatithandize pa nkhaniyi. Ngati tingayankhe kuti inde pa funso limodzi, zingasonyeze kuti munthuyo ali ndi chidwi. Ngati tikukayikira kuti ali ndi chidwi, ndi bwino kungomupatsa kapepala. Komabe munthu akapempha magazini kapena buku linalake, tikhoza kumupatsa.Miy. 3:27, 28.