July 29–August 4
SALIMO 69
Nyimbo Na. 13 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Zimene Zinachitika pa Moyo wa Yesu Zinanenedweratu mu Salimo 69
(10 min.)
Yesu ankadedwa popanda chifukwa (Sl 69:4; Yoh 15:24, 25; w11 8/15 11 ¶17)
Yesu ankadzipereka panyumba ya Yehova (Sl 69:9; Yoh 2:13-17; w10 12/15 8 ¶7-8)
Yesu anavutika kwambiri mumtima komanso anamumwetsa vinyo wosakaniza ndi zinthu zowawa zamadzimadzi (Sl 69:20, 21; Mt 27:34; Lu 22:44; Yoh 19:34; g95 10/22 31 ¶4; it-2 650)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: N’chifukwa chiyani Yehova anaikanso maulosi okhudza Mesiya m’Malemba a Chiheberi?
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Sl 69:30, 31—Kodi mavesiwa angatithandize bwanji kuti mapemphero athu azikhala abwino? (w99 1/15 18 ¶11)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 69:1-25 (th phunziro 2)
4. Kuleza Mtima—Zomwe Yesu Anachita
(7 min.) Nkhani yokambirana. Onerani VIDIYO, kenako kambiranani kabuku ka lmd phunziro 8 mfundo 1-2.
5. Kuleza Mtima—Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu
(8 min.) Nkhani yokambirana kuchokera mu kabuku ka lmd phunziro 8 mfundo 3-5 ndi “Onaninso Malemba Awa.”
Nyimbo Na. 134
6. Zofunika Pampingo
(5 min.)
7. Mfundo Zofunika pa Nthawi ya Kulambira kwa Pabanja
(10 min.) Nkhani yokambirana.
Mu January 2009, Phunziro la Buku la Mpingo linaphatikizidwa ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu komanso Msonkhano wa Utumiki kukhala msonkhano umodzi wa mkati mwa mlungu. Zimenezi zinapereka mwayi kwa mabanja kuti azikhala ndi nthawi yawoyawo yochita kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse. Ambiri anayamikira kwambiri dongosolo limeneli chifukwa linawathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova komanso anthu a m’banja lawo.—De 6:6, 7.
Kodi ndi mfundo zina ziti zimene zingathandize mitu ya mabanja kuti kulambira kwa pabanja kuzikhala kothandiza?
-
Muzichita mlungu uliwonse. Ngati n’kotheka, muzikhala ndi nthawi yokhazikika yochita kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse. Muzisankhiratu tsiku lina limene mungachite kulambiraku ngati tsiku limene munakhazikitsa pachitika zinthu zina zomwe zingakulepheretseni
-
Muzikonzekera. Muzikambirana ndi mkazi wanu komanso nthawi zina muzifunsa ana anu nkhani zomwe mungakambirane pa kulambira kwa pabanja. Kukonzekeraku sikukuyenera kukhala kwa nthawi yaitali, makamaka ngati zimene mukufuna kukambiranazo mumazichita mobwerezabwereza
-
Muzichita zinthu mogwirizana ndi mmene zinthu zilili m’banja lanu. Ana akamakula, zinthu zimene amafunikira komanso zimene angakwanitse kuchita zimasintha. Kulambiraku kuyenera kuthandiza aliyense m’banja lanu kuti akule mwauzimu
-
Muziyesetsa Kuti Aliyense Azikhala Womasuka. Ngati nyengo ili bwino, nthawi zina mukhoza kumachitira panja. Muzikhala ndi kanthawi kopuma. Ngakhale kuti nthawi zina mungakambirane za mavuto amene akuchitika m’banja lanu, musamagwiritse ntchito nthawi imeneyi podzudzula kapena kukalipira ana anu pa zimene amalakwitsa
-
Muzisinthasintha. Mwachitsanzo, pa kulambira kwa pabanja mungakonzekere mbali inayake ya pamisonkhano yampingo yotsatira, kuonera ndi kukambirana vidiyo inayake ya pa jw.org kapena kukonzekera zimene mungachite mu utumiki. Ngakhale kuti kulambira kwa pabanja kuyenera kuchitika mokambirana, mukhozanso kugwiritsa ntchito nthawi imeneyi kuti aliyense aphunzire Baibulo payekha
Kambiranani funso ili:
-
Kodi mwagwiritsapo ntchito bwanji mfundo zimenezi pa kulambira kwanu kwa pabanja?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 13 ¶8-16, bokosi patsamba 105