March 21-27
YOBU 6-10
Nyimbo Na. 68 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yobu Anasonyeza Kukhumudwa Kwake”: (10 min.)
Yobu 6:1-3, 9, 10, 26; 7:11, 16—Munthu akakhumudwa amatha kuyankhula zinthu zimene sizili mumtima mwake (w13 8/15 19 ndime 7; w13 5/15 22 ndime 13)
Yobu 9:20-22—Yobu anaganiza molakwika kuti Mulungu analibe nazo ntchito ngakhale kuti iye anayesetsa kukhala wokhulupirika (w15 7/1 12 ndime 2)
Yobu 10:12—Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto ambiri, Yobu ankanena zabwino za Yehova (w09 4/15 7 ndime 18; w09 4/15 10 ndime 13)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yobu 6:14
—Kodi Yobu anasonyeza bwanji kuti kukoma mtima kosatha n’kofunika? (w10 11/15 32 ndime 20) Yobu 7:9, 10; 10:21—Ngati Yobu ankakhulupirira kuti akufa adzauka, n’chifukwa chiyani ananena zimene zili m’mavesiwa? (w06 3/15 14 ndime 11)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: Yobu 9:1-21 (Osapitirira 4 min.)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: wp16.2 16
—Muuzeni munthu amene mukumulalikirayo kuti angathe kupereka ndalama zothandizira ntchito yathu yapadziko lonse. (Osapitirira 2 min.) Ulendo Wobwereza: wp16.2 16
—Muuzeni nkhani imene mudzaphunzire ulendo wotsatira. (Osapitirira 4 min.) Phunziro la Baibulo: fg phunziro 2 ndime 6-8 (Osapitirira 6 min.)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo Na. 114
Muzichita Zinthu Mozindikira Mukamalimbikitsa Ena: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani vidiyo imene akulu anaonera pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yomwe inachitika posachedwapa. Kenako pemphani omvera kuti afotokoze mmene abale awiri a m’vidiyoyi asonyezera chitsanzo chabwino polimbikitsa munthu amene wakhumudwa chifukwa cha imfa ya munthu amene amam’konda.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: cl mutu 27 ndime 19-22 ndi bokosi patsamba 279 (30 min.)
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 27 ndi Pemphero