Zitsanzo za Ulaliki
NSANJA YA OLONDA
Funso: Kodi mukuona kuti mphatso yaikulu kwambiri imene Mulungu anatipatsa ndi iti?
Lemba: Yoh. 3:16
Perekani Magaziniyo: Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza chifukwa chimene Mulungu anatumizira Yesu padziko lapansi kuti adzatifere komanso mmene tingasonyezere kuti timayamikira mphatsoyi.
KODI UFUMU WA MULUNGU N’CHIYANI?
Funso: [Musonyezeni tsamba loyamba la kapepalako.] Kodi mungayankhe bwanji funso ili? Kodi Ufumu wa Mulungu ndi chinachake chimene chimakhala mumtima mwa munthu aliyense, mawu ongophiphiritsira kapena ndi boma limene lili kumwamba?
Lemba: Dan. 2:44; Yes. 9:6
Perekani Kapepalako: Kapepala aka kakufotokoza zimene Ufumu wa Mulungu ungakuchitireni.
KAPEPALA KOITANIRA ANTHU KU CHIKUMBUTSO
Tikuitanira anthu ku mwambo wofunika kwambiri. [Perekani kapepalako.] Pa 11 April, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse adzasonkhana kuti akumbukire imfa ya Yesu ndiponso kumvetsera nkhani ya m’Baibulo yokhudza mmene imfayi ingatithandizire. Kapepalaka kakusonyeza nthawi ndiponso malo amene mwambowu udzachitikire kunoko. Tidzasangalala kwambiri ngati mutabwera.
LEMBANI ULALIKI WANUWANU
Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito