CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Mumachita Zinthu Mopupuluma?
Davide anapempha zinthu mwaulemu koma anayankhidwa mwachipongwe (1Sa 25:7-11; ia 78 ¶10-12)
Davide ankafuna kupha amuna onse a m’nyumba ya Nabala (1Sa 25:13, 21, 22)
Abigayeli anathandiza Davide kuti asapalamule mlandu wa magazi (1Sa 25:25, 26, 32, 33; ia 80 ¶18)
DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi ndimachita zinthu mopupuluma ndikakwiya, ndikamagula zinthu, kapena ndikafooka? Kapena kodi ndimayamba ndaganiza kaye zomwe zingatsatirepo?’—Miy 15:28; 22:3.