MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mumacheza ndi Ndani pa Intaneti?
Mawu akuti mnzako amatanthauza “munthu amene umagwirizana naye chifukwa choti mumakondana kapena kulemekezana.” Mwachitsanzo, Yonatani ndi Davide anakhala pa ubwenzi wolimba kwambiri kungochokera pamene Davide anapha Goliyati. (1Sa 18:1) Aliyense anasonyeza makhalidwe amene anachititsa kuti mnzake ayambe kumukonda. Choncho kuti munthu ukhale pa ubwenzi wolimba ndi munthu wina, zimadalira ngati ukumudziwadi molondola. Kuti umudziwe bwino munthu wina pamafunika nthawi komanso khama. Komabe, pa malo ochezera a pa intaneti munthu ukhoza kukhala ndi “anzako” mwa kungodina batani. Chifukwa choti anthu pa intaneti akhoza kupanga pulani ya zimene angalembe komanso akhoza kubisa kuti ena asaone zinthu zina zokhudza iwowo, kumakhala kovuta kudziwa makhalidwe awo enieni. Choncho tiyenera kuganizira mosamala tisanavomere anthu oti tizicheza nawo pa intaneti. Ngati munthu wina amene simukumudziwa akufuna kuti mukhale mnzake pa intaneti, musamachite mantha kukana poopa kuti mumukhumudwitsa. Chifukwa choopa zimene zingachitike, anthu ena anasankha kuti asamagwiritse ntchito n’komwe malo ochezera a pa intaneti. Komabe, ngati mwasankha kugwiritsa ntchito malowa, kodi muyenera kukumbukira chiyani?
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZICHITA ZINTHU MOSAMALA MUKAMACHEZA NDI ANZANU PA INTANETI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi muyenera kuganizira chiyani musanaike zithunzi kapena musanalembe ndemanga pa malo ochezera a pa intaneti?
-
N’chifukwa chiyani muyenera kusankha mosamala anzanu ocheza nawo pa intaneti?
-
N’chifukwa chiyani muyenera kudziikira malire pa nthawi imene mumathera mukucheza ndi anzanu pa intaneti?—Aef 5:15, 16