CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bwenzi Labwino?
Muzitonthoza komanso kulimbikitsa mnzanu amene akuda nkhawa (1Sa 20:1, 2; w19.11 7 ¶18)
Muzichenjeza mnzanu ku zinthu zoopsa (1Sa 20:12, 13; w08 2/15 8 ¶7)
Muzimuikira kumbuyo ena akamamunenera zoipa (1Sa 20:30-32; w09 10/15 19 ¶11)
Anthu a Yehova ali ndi mwayi waukulu wokhala ndi anzawo abwino. Kuti tikhale ndi mabwenzi, tiyenera kukhala aubwenzi. Kodi ndi ndani amene mungakonde kuti akhale mnzanu mumpingo?