KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Zimene Tinganene
Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso (19 March–15 April)
“Ndife osangalala kukuitanirani kumwambo wofunika kwambiri womwe udzachitike padziko lonse. Mwambo umenewu ndi wokumbukira imfa ya Yesu.” M’patseni kapepala kosindikizidwa kapena ka pachipangizo chamakono. “Kapepalaka kakusonyeza nthawi komanso malo omwe mwambowu udzachitikire m’dera lathu lino [kapena zimene mungachite kuti muchite nawo mwambowu pa intaneti]. Tikukuitananinso kuti mudzamvetsere nkhani yapadera yomwe idzakambidwe kumapeto kwa mlungu woyambira April 4.”
Ngati Munthuyo Wasonyeza Chidwi: Musonyezeni [kapena mutumizireni linki ya] vidiyo yakuti Tizikumbukira Imfa ya Yesu.
Funso la Ulendo Wotsatira: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?
^ ndime 7 ^ ndime 11 Mukhoza kusintha mafunsowa komanso zimene zikuchitika kuti zigwirizane ndi mmene zinthu zilili kwanuko.