MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzigwiritsa Ntchito Zimene Zikuchitika M’dera Lanu Mukakhala mu Utumiki
Pamene ankachita utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu ankaphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito zinthu zimene zinkachitika pa nthawiyo. (Lu 13:1-5) Inunso mukhoza kugwiritsa ntchito zimene zikuchitika m’dera lanu pofuna kuthandiza anthu kuti akhale ndi chidwi ndi uthenga wa Ufumu. Pambuyo potchula zinthu monga kukwera mitengo kwa zinthu, ngozi zam’chilengedwe, zipolowe, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena zinthu zina, mukhoza kufunsa funso lowathandiza kuganiza. Mwina mungafunse kuti: “Kodi mavuto monga . . . adzathadi?” kapena “Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chingathetse . . . ?” Kenako muwerengereni lemba logwirizana ndi nkhaniyo. Ngati munthuyo wasonyeza chidwi, muonetseni vidiyo, kapena mugawireni chimodzi mwa Zinthu Zophunzitsira. Tiyeni tizichita “zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino” pamene tikuyesetsa kuti tiwafike pamtima anthu onse a m’gawo lathu.—1Ak 9:22, 23.
Kodi ndi nkhani ziti zimene zingachititse chidwi anthu a m’gawo lanu?