Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azidzidyetsa Mwauzimu

Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azidzidyetsa Mwauzimu

Kuti ophunzira amudziwe bwino Yehova komanso akhale olimba mwauzimu, ayenera kuphunzira zambiri osati mfundo za choonadi zokha zomwe timawaphunzitsa. (Mt 5:3; Ahe 5:12–6:2) Ayeneranso kuphunzira mmene angamadzidyetsere okha mwauzimu.

Phunziro likangoyamba kumene, muzisonyeza ophunzira anu mmene angamakonzekerere phunziro la Baibulo ndipo muziwalimbikitsa kuchita zimenezi. (mwb18.03 6) Muziwalimbikitsa kuti azipemphera asanayambe kuphunzira paokha. Muziwathandiza kupeza komanso kugwiritsa ntchito zinthu zophunzirira za pazipangizo zamakono. Muziwasonyeza mmene angapezere zinthu zatsopano pa jw.org ndi JW Broadcasting®. Pakapita nthawi, muziwaphunzitsa kuti aziwerenga Baibulo tsiku lililonse, azikonzekera misonkhano yampingo, komanso azifufuza mayankho a mafunso awo. Muziwathandiza kuti aziganizira mozama zimene akuphunzirazo.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITHANDIZA AMENE MUKUPHUNZIRA NAWO BAIBULO KUTI AZIDZIDYETSA MWAUZIMU, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Anita anathandiza bwanji Jane kudziwa kuti kuphunzira kumaphatikizapo zambiri osati kungodziwa mayankho okha?

  • Kodi n’chiyani chinathandiza Jane kutsimikiza kuti Yehova salakwitsa akamaletsa anthu zachiwerewere?

  • Muzithandiza ophunzira anu kudziwa mmene angadziphunzitsire okha komanso mmene angagwiritsire ntchito zimene aphunzirazo

    Pa nkhani yoganizira mozama zomwe waphunzira, kodi Jane anazindikira chiyani?