Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Ntchito Yovuta Yomwe Inatheka Ndi Mzimu Woyera

Ntchito Yovuta Yomwe Inatheka Ndi Mzimu Woyera

Kuyambira kale, anthu a Mulungu akhala akuchita zinthu zochititsa chidwi, osati chifukwa cha nzeru zawo, koma chifukwa cha thandizo la Yehova. Mu 1954, gulu la Yehova linatulutsa vidiyo ya Chingelezi ya mutu wakuti The New World Society in Action. Vidiyoyi inapangidwa ndi abale ndi alongo otumikira pa Beteli omwe analibe luso lopanga mavidiyo. Iwo anakwanitsa kugwira ntchito yovutayi chifukwa cha mzimu woyera wa Yehova. Mzimuwu umatithandiza kukhala otsimikiza kuti tikamadalira Yehova, tikhoza kukwanitsa kuchita utumiki uliwonse omwe tapatsidwa.​—Zek 4:6.

ONERANI VIDIYO YAKUTI KUPANGA VIDIYO YA “THE NEW WORLD SOCIETY IN ACTION,” NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani anaganiza zopanga vidiyo yokhudza likulu lathu la padziko lonse?

  • Kodi vidiyoyi inasonyeza bwanji kuti atumiki a pa Beteli ali ngati thupi la munthu?​—1Ak 12:14-20

  • Kodi abale amene ankapanga vidiyoyi anakumana ndi mavuto otani, nanga anathana nawo bwanji?

  • Kodi nkhaniyi yatiphunzitsa chiyani zokhudza mzimu woyera wa Yehova?