Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Timathokoza Yehova Chifukwa cha Chikondi Chanu

Timathokoza Yehova Chifukwa cha Chikondi Chanu

Ngakhale kuti Akhristu a mpingo wa ku Tesalonika ankakumana ndi mavuto, iwo anasonyeza chikondi kwa Akhristu anzawo. (2At 1:3, 4) Masiku anonso, anthu a Yehova amasonyeza chikondi choterechi kwa abale awo padziko lonse. Nkhani za pa jw.org za mutu wakuti “Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?” zimafotokoza mmene zopereka zanu zimathandizira abale panthawi imene akukumana ndi mavuto. Timakuyamikirani chifukwa cha chikondi chanu komanso mtima wanu wopatsa.

ONERANI VIDIYO YAKUTI NTHAWI ZONSE ‘TIMAYAMIKA MULUNGU CHIFUKWA CHA INU,’ NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

• Kodi zopereka zathu zimathandiza pa zinthu ziti?

• Kodi njira yabwino kwambiri yoperekera thandizo la ndalama kwa abale ndi alongo amene akufunikira thandizo ndi iti?​—Onaninso nkhani ya pa jw.org yakuti “Zimene Ena Ali Nazo Zimathandizira pa Zimene Ena Akusowa