October 4-10
YOSWA 8-9
Nyimbo Na. 127 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Zimene Tikuphunzira pa Nkhani ya Agibeoni”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Yos 8:29—N’chifukwa chiyani mfumu ya ku Ai anaipachika pamtengo? (it-1 1030)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) Yos 8:28–9:2 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 2)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. M’patseni kapepala koitanira anthu kumisonkhano yathu, ndipo kenako yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? (th phunziro 11)
Nkhani: (5 min.) lfb mutu 31—Mutu: Kodi Tingaphunzire Chiyani pa Pangano Limene Yoswa Anachita ndi Agibeoni? (th phunziro 13)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzisonyeza Kuti Ndinu Wodzichepetsa (1Pe 5:5): (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani mafunso otsatirawa: Kodi Petulo ndi Yohane anachita chiyani potsatira malangizo a Yesu okhudza Pasika? Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani pa nkhani ya kudzichepetsa usiku woti afa mawa lake? Kodi tikudziwa bwanji kuti Petulo ndi Yohane anaphunzirapo kanthu pa zimenezi? Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odzichepetsa?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lvs mutu 5 ndime 16-23, mfundo za m’Baibulo tsa. 71-74
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 119 ndi Pemphero